Onani zimene zilipo

Lengezani Uthenga Wabwino!

Msonkhano wa Cigawo wa Mboni za Yehova wa 2024

Kuloŵa ni ulele Sikudzakhala kupititsamo mbale ya pelekani-pelekani

Mfundo Zikulu-zikulu

Tsiku Loyamba: Mudzaona maumboni oonetsa kuti nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zimafotokoza umoyo wa Yesu molondola. Mudzaphunzilanso mmene nkhani za m’Baibo zimenezi zimatiphindulila masiku ano.

Tsiku Laciŵili: Kodi Baibo inalosela ciyani za kubadwa kwa Yesu, komanso za umoyo wake ali mwana? Nanga kodi maulosiwo anakwanilitsikadi?

Tsiku Lacitatu: Mu nkhani yozikika m’Baibo yakuti “Cifukwa Cake Sitiopa Uthenga Woipa,” mudzaphunzila cifukwa cake anthu mamiliyoni masiku ano amaona kuti ni otetezeka, komanso cifukwa cake saopa za m’tsogolo ngakhale kuti zinthu pa dzikoli zikuipila-ipila.

Seŵelo Lalikulu

Uthenga Wabwino Wolalikidwa na Yesu: Gawo 1

Kuwala Kwenikweni kwa Dziko

Kubadwa kwa Yesu kozizwitsa kunali ciyambi cabe ca zinthu za padela kwambili zimene zinacitika Yesu ali mwana. Makolo ake anathawila naye ku Iguputo pomwe mfumu yoipa inali kumufuna-funa kuti imuphe. Patapita nthawi, iye anadabwitsa ena mwa aphunzitsi aluso a m’nthawi yake. Bwelani mudzaone zocitika zimenezi na zina, pa tsiku loyamba komanso laciŵili, mu gawo 1 la mbali ziŵili.

Tambani mavidiyo otsatilawa okamba za msonkhano wa caka cino

N’ciyani Cimacitika pa Msonkhano Wathu Wacigawo?

Onani zinthu zina zimene mungayembekezele pa msonkhano wa cigawo wa Mboni za Yehova.

Msonkhano wa Cigawo wa Mboni za Yehova wa 2024: Lengezani Uthenga Wabwino!

Onani zimene tidzaphunzila pa msonkhano wa caka cino.

Kadyonkho ka Seŵelo Lalikulu: Uthenga Wabwino Wolalikidwa na Yesu

Anthu ambili amaidziŵa bwino nkhani ya kubadwa kwa Yesu kozizwitsa. Koma kodi n’ciyani cinacitika Yesu asanabadwe, komanso pambuyo pake?