Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Asa, Yehosafati, Hezekiya, Yosiya

Tumikilani Yehova ndi Mtima Wathunthu

Tumikilani Yehova ndi Mtima Wathunthu

“Inu Yehova, conde kumbukilani kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupilika ndiponso ndi mtima wathunthu.”—2 MAF. 20:3.

NYIMBO: 52, 65

1-3. Kodi kutumikila Yehova ndi “mtima wathunthu” kumatanthauza ciani? Fotokozani citsanzo

POKHALA opanda ungwilo, timalakwitsa zinthu. Koma ubwino ni wakuti Yehova sacita nafe “mogwilizana ndi macimo athu.” Iye satelo ngati tilapa ndi kum’pempha mwacikhulupililo ndi modzicepetsa kuti atikhululukile pa maziko a nsembe ya dipo la Yesu. (Sal. 103:10) Komabe, monga mmene Davide anauzila Solomo, kuti kulambila kwathu kukhale kovomelezeka pamaso pa Yehova, tifunika ‘kum’tumikila ndi mtima wathunthu.’ (1 Mbiri 28:9) Kodi zimenezi zingatheke bwanji kwa ife anthu opanda ungwilo?

2 Kuti tidziŵe, tiyeni tiyelekezele umoyo wa Mfumu Asa ndi Mfumu Amaziya. Mafumu aciyuda onse aŵiliwa anacita zoyenela pamaso pa Yehova, koma Asa anatelo ndi mtima wathunthu. (2 Mbiri 15:16, 17; 25:1, 2; Miy. 17:3) Onse anali opanda ungwilo ndipo analakwitsa zinthu zina. Koma Asa sanacoke kwa Mulungu cifukwa mtima wake unali “wathunthu” kwa iye. (1 Mbiri 28:9) Mosiyana ndi Asa, Amaziya sanali wodzipeleka ndi mtima wonse kwa Yehova. Mwacitsanzo, iye atagonjetsa adani a Mulungu kunkhondo, anatenga milungu yawo ndi kuyamba kukailambila.—2 Mbiri 25:11-16.

3 Kutumikila Mulungu ndi “mtima wathunthu” kumatanthauza kudzipeleka kwa iye ndi mtima wonse kosalekeza. M’Baibo, liu lakuti “mtima” kaŵili-kaŵili limatanthauza munthu wamkati. Mtimawo umaphatikizapo zimene munthu amalaka-laka, maganizo ake, makhalidwe, maluso, ndi zolinga zake. Conco, munthu amene amatumikila Yehova na mtima wake wonse sacita zinthu mwaciphamaso. Salambila Yehova mwamwambo cabe. Nanga bwanji ife? Ngati tikhalabe odzipeleka kwa Mulungu ndi mtima wonse komanso mokhulupilika, ndiye kuti tikum’tumikila ndi mtima wathunthu, ngakhale kuti ndife opanda ungwilo.—2 Mbiri 19:9.

4. Kodi tsopano tidzakambilana ciani?

4 Kuti timvetsetse tanthauzo la kutumikila Mulungu ndi mtima wathunthu, tiyeni tikambilane za Asa ndi mafumu ena aciyuda, amene anatumikila Mulungu ndi mtima wonse. Mafumu amenewo ndi Yehosafati, Hezekiya, ndi Yosiya. Mafumu onse amenewa analakwitsapo zina-zake, koma Yehova anapitiliza kuwayanja. N’cifukwa ciani Mulungu anaona kuti iwo anam’tumikila ndi mtima wathunthu? Nanga ife tingatengele bwanji citsanzo cawo?

“ASA ANATUMIKILA YEHOVA NDI MTIMA WATHUNTHU”

5. Ni zinthu ziti zimene Asa anacita molimba mtima?

5 Asa anali mfumu yacitatu yaciyuda kucokela pamene ufumu wa Yuda unapatukana ndi ufumu wakumpoto wa Isiraeli wa mafuko 10. Iye anacotsa mafano ndi mahule aamuna a pakacisi m’dziko la Yuda. Anacotsanso ambuye ake aakazi, a Maaka, pa udindo wawo monga “mayi wa mfumu, cifukwa anapanga fano lonyansa kwambili.” (1 Maf. 15:11-13) Kuwonjezela apo, Asa analimbikitsa anthu “kuti afunefune Yehova Mulungu . . . ndi kutsatila cilamulo.” Inde, iye anayesetsa kupititsa patsogolo kulambila koona.—2 Mbiri 14:4.

6. Kodi Asa anacita ciani pamene Aitiyopiya anaukila dziko la Yuda?

6 Yehova anacititsa kuti m’dziko la Yuda mukhale mtendele m’zaka 10 zoyambilila za ulamulilo wa Asa. Pambuyo pake, Zera Mwitiyopiya anabwela kudzamenyana ndi Ayuda ali ndi asilikali 1,000,000 ndi magaleta 300. (2 Mbiri 14:1, 6, 9, 10) Kodi Asa anacita ciani? Anadalila Yehova. (Ŵelengani 2 Mbiri 14:11.) Poyankha pemphelo la Asa locokela pansi pa mtima, Mulungu anamuthandiza kugonjetsa kothelatu gulu lankhondo la Aitiyopiya. (2 Mbiri 14:12, 13) Nthawi zina cifukwa ca dzina lake, Yehova anali kuthandiza ngakhale mafumu amene anali osakhulupilika kwa iye. (1 Maf. 20:13, 26-30) Koma Asa, anadalila Mulungu, ndipo Yehova anayankha pemphelo lake. N’zoona kuti pambuyo pake Asa anacita zinthu mosaganiza bwino. Mwacitsanzo, anakapempha thandizo kwa mfumu ya Siriya m’malo modalila Yehova. (1 Maf. 15:16-22) Komabe, Mulungu atasanthula bwino-bwino mtima wa Asa, anaona kuti iye “anatumikila Yehova ndi mtima wathunthu masiku ake onse.” Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Asa pocita zabwino?—1 Maf. 15:14.

7, 8. Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Asa potumikila Yehova?

7 Aliyense wa ife ayenela kudzipenda kuti aone ngati ndi wodzipeleka ndi mtima wonse kwa Mulungu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimayesetsa kucita zinthu zokondweletsa Yehova, kuteteza kulambila koona, ndi kuteteza anthu a Mulungu ku zinthu zimene zingawaononge mwauzimu?’ Ganizilani za Asa. Iye anafunika kulimba mtima kuti acotse Maaka pa udindo wokhala “mayi wa mfumu” m’dziko lake. N’zoona kuti mumpingo sitingayembekezele kupeza munthu wocita zoipa ngati Maaka. Koma nthawi zina mungafunike kucita zinthu molimba mtima ngati Asa. Mwacitsanzo, bwanji ngati wina m’banja lanu kapena mnzanu wapamtima wacita chimo, ndipo wacotsedwa mumpingo cifukwa cosalapa? Kodi mungalimbe mtima na kuleka kuceza naye? Kodi mtima wanu ungakusonkhezeleni kucita ciani?

8 Mofanana ndi Asa, inunso mungaonetse kuti muli ndi mtima wathunthu mwa kudalila Mulungu na mtima wonse ngakhale pamene mukumana ndi citsutso cooneka ngati cosapililika. Mwina ena amakusekeni kapena kukunyozani kusukulu cifukwa cokana kucita zinthu zina monga Mboni ya Yehova. Mwinanso anzanu kunchito amakunyozani cifukwa copempha chuti kapena kulephela kusewenza ovataimu kuti mukacita zinthu zauzimu. Zikakhala conco, muyenela kupemphela kwa Mulungu ngati mmene Asa anacitila. Muyenela kudalila Yehova molimba mtima ndi kukhala wosasunthika pocita zinthu zimene muona kuti ndiye zoyenela ndi zanzelu. Kumbukilani kuti Mulungu analimbitsa Asa ndi kum’thandiza, ndipo inunso adzakulimbitsani.

9. Kodi tiyenela kukhala ndi zolinga ziti polalikila ndi mtima wathunthu?

9 Atumiki a Mulungu amayesetsa kuthandiza anthu ena. Asa analimbikitsa ena kulambila Yehova. Nafenso timathandiza ena ‘kufuna-funa Yehova.’ Yehova ayenela kuti amakondwela kwambili akaona kuti tiuzako anansi athu ndi anthu ena za iye. Amakondwela maka-maka ngati ticita zimenezi cifukwa comukonda ndi mtima wonse, komanso cifukwa cofuna kuti anthu akapeze moyo wosatha.

YEHOSAFATI ANAFUNA-FUNA YEHOVA

10, 11. Kodi tingatsatile bwanji citsanzo ca Yehosafati?

10 Yehosafati mwana wa Asa “anapitiliza kuyenda m’njila za Asa bambo ake.” (2 Mbiri 20:31, 32) Kodi Yehosafati anacita zotani? Mofanana ndi atate wake, Yehosafati analimbikitsa anthu kufuna-funa Yehova. Iye anakonza pulogilamu yophunzitsa anthu poseŵenzetsa “buku la cilamulo ca Yehova.” (2 Mbiri 17:7-10) Anakafika mpaka ku dela la lamapili la Efuraimu, mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli, kuti akalimbikitse anthu ‘kubwelela kwa Yehova.’ (2 Mbiri 19:4) Mfumu Yehosafati “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”—2 Mbiri 22:9.

11 Tonsefe tili na mwayi wogwila nawo nchito yaikulu yophunzitsa anthu, imene Yehova afuna kuti icitike masiku ano. Kodi mwezi uliwonse mumayesetsa kuphunzitsa anthu Mau a Mulungu ndi kuwalimbikitsa kuti ayambe kum’tumikila? Ngati mumayesetsa kucita zimenezi, mwa dalitso la Mulungu, mungathe kuyambitsa phunzilo la Baibo. Kodi mumapemphela kuti mupeze phunzilo la Baibo? Ngati ndi conco, mungafunike kulalikila mwakhama ngakhale pa nthawi imene anthu ambili amaona kuti ndi yopumula. Ndiponso mofanana ndi Yehosafati, amene anapita ku dela la Efuraimu kukathandiza anthu kuti ayambenso kulambila Yehova, ifenso tiyenela kuyesetsa kuthandiza anthu amene anazilala. Komanso, akulu mumpingo amapanga makonzedwe oyendela ndi kuthandiza anthu ocotsedwa a m’gawo la mpingo wawo, amene aoneka kuti analeka kucita macimo.

12, 13. (a) Kodi Yehosafati anacita ciani atakumana ndi vuto loopsa? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kuvomeleza kufooka kwathu ngati mmene Yehosafati anacitila?

12 Yehosafati anakhalabe wodzipeleka kwa Mulungu mofanana ndi Asa, atate wake. Pamene anaopsezedwa ndi gulu lankhondo lalikulu la adani, anadalila Mulungu. (Ŵelengani 2 Mbiri 20:2-4.) Yehosafati anacita mantha. Komabe, “anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.” M’pemphelo limene anapeleka, iye anavomeleza modzicepetsa kuti anthu ake ‘analibe mphamvu zotha kulimbana ndi khamu lalikulu’ limenelo. Anakambanso kuti iye ndi anthu ake sanali kudziŵa cocita. Yehosafati anadalila Yehova ndi mtima wonse, ndipo anati: “Maso athu ali pa inu.”—2 Mbiri 20:12.

13 Nthawi zina, ifenso mofanana ndi Yehosafati tingasoŵe cocita, ngakhale kucita mantha kumene cifukwa ca mavuto amene takumana nawo. (2 Akor. 4:8, 9) Koma kumbukilani kuti Yehosafati anavomeleza pa gulu la Aisiraeli kuti iye ndi anthu ake analibe mphamvu. (2 Mbiri 20:5) Anthu amene amatsogolela pa zinthu zauzimu m’banja angatengele citsanzo ca Yehosafati. Ayenela kupempha Yehova kuti awatsogolele ndi kuwapatsa mphamvu kuti apilile mavuto amene akumana nawo. Musacite manyazi kupeleka mapemphelo ocondelela pamodzi ndi a m’banja lanu. Mukatelo, iwo adzaona kuti mumadalila Yehova. Kumbukilani kuti Mulungu anathandiza Yehosafati; inunso adzakuthandizani.

HEZEKIYA ANAPITILIZA KUCITA ZOYENELA

14, 15. Kodi Hezekiya anaonetsa bwanji kuti anadalila Mulungu ndi mtima wonse?

14 Mfumu Hezekiya nayenso “anapitiliza kumamatila Yehova.” Mosiyanako ndi Yehosafati, Hezekiya anafunika kupewa kutengela citsanzo coipa ca atate wake, amene anali kulambila mafano. Hezekiya “anacotsa malo okwezeka, kugwetsa zipilala zopatulika, ndi kudula mzati wopatulika. Iye anaphwanyaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga” cifukwa masiku amenewo, anthu anali kuilambila. Iye anali wodzipeleka ndi mtima wonse kwa Yehova cakuti “anapitiliza kusunga malamulo amene Yehova analamula Mose.”—2 Maf. 18:1-6.

15 Hezekiya anadalila Yehova ndi mtima wonse ngakhale pamene ufumu wamphamvu padziko lonse wa Asuri, unaukila dziko la Yuda ndi kuopseza kuti udzawononga Yerusalemu. Senakeribu, Mfumu ya Asuri, anatonza Yehova ndi kuopseza Hezekiya n’colinga cakuti angodzipeleka m’manja mwawo. Komabe, pemphelo limene Hezekiya anapeleka linaonetsa kuti anadalila Yehova ndi mtima wake wonse kuti adzawapulumutsa. (Ŵelengani Yesaya 37:15-20.) Mulungu anayankha pemphelo lake mwa kutumiza mngelo amene anapha asilikali 185,000 a Asuri.—Yes. 37:36, 37.

16, 17. Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Hezekiya potumikila Mulungu?

16 Patapita nthawi, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa. Iye anapempha Yehova kuti am’kumbukile popeza anayenda mokhulupilika pamaso pake. (Ŵelengani 2 Mafumu 20:1-3.) Malinga n’zimene Malemba amakamba, tidziŵa kuti masiku ano, Mulungu sangatalikitse moyo wathu kapena kuticilitsa mozizwitsa. Komabe, mofanana ndi Hezekiya, aliyense wa ife angauze Yehova m’pemphelo kuti: “Ndinayenda pamaso panu mokhulupilika ndiponso ndi mtima wathunthu.” Kodi mumakhulupilila kuti Yehova ndi wokonzeka kukucilikizani pamene mudwala ndi kuti ali na mphamvu yocita zimenezo?—Sal. 41:3.

17 Kuganizila citsanzo ca Hezekiya kuyenela kutilimbikitsa kuleka ciliconse cimene cingasokoneze ubale wathu ndi Mulungu, kapena kutilepheletsa kuika zinthu zauzimu patsogolo. Mwacitsanzo, sitifuna kutengela anthu a m’dzikoli amene amaseŵenzetsa Intaneti potamanda anthu ena mopambanitsa ngati kuti ndi milungu. Si kulakwa kuti Akhristu azisangalala poceza ndi acibale kapena anzawo pa Intaneti. Koma anthu ambili m’dzikoli amathela nthawi yoculuka akuceza pa intaneti, ndipo amaceza ndi anthu amene sawadziŵa ngakhale pang’ono. Ena amawononga nthawi yoculuka kuona mapikica a anthu amenewo kapena kuŵelenga nkhani zokhudza anthuwo. Kucita zimenezi n’kutaya nthawi ndi zinthu zopanda phindu. Mkhristu angayambe kunyada akaona kuti anthu ambili amakonda mapikica ndi zinthu zina zimene iye amaika pa intaneti. Angafike pokhumudwa akaona kuti anthuwo aleka kuona zinthu zakezo. Ganizilani citsanzo ca Paulo, Akula ndi Purisikila. Kodi muganiza kuti iwo akanakhalapo, sembe akutangwanika tsiku lililonse kuika mapikicha pa intaneti, kapena kuona zimene anthu ena amene si Mboni aikapo? Baibo imakamba kuti Paulo anali ‘kutanganidwa kwambili ndi nchito yolalikila Mau a Mulungu.’ Ndipo Purisikila ndi Akula anaseŵenzetsa nthawi yawo ‘kufotokozela [ena] njila ya Mulungu molondola.’ (Mac. 18:4, 5, 26) Conco tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimapewa kutamanda anthu ena mopambanitsa kapena kuseŵenzetsa nthawi yoculuka pa zinthu zosafunika kweni-kweni?’—Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.

YOSIYA ANASUNGA MALAMULO A YEHOVA

18, 19. Kodi mufuna kutengela Yosiya m’njila ziti?

18 Mfumu Yosiya, mdzukulutubzi wa Hezekiya, nayenso anasunga malamulo a Yehova “ndi mtima wake wonse.” (2 Mbiri 34:31) Akali wacicepele, iye “anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide,” ndipo pamene anakwanitsa zaka 20, anayamba kucotsa zinthu zokhudzana ndi kulambila mafano mu Yuda. (Ŵelengani 2 Mbiri 34:1-3.) Yosiya anayesetsa kucita zinthu zokondweletsa Mulungu kuposa mafumu ambili a Yuda. Nthawi ina, anthu atapeza buku la Cilamulo, limene liyenela kuti linalembedwa mwacindunji ndi Mose, analiŵelenga pamaso pa Yosiya. Atamva mau a m’Cilamuloco, Yosiya anaona kuti afunika kucita zinthu zina zambili kuti akwanilitse cifunilo ca Mulungu. Iye analimbikitsa anthu kutumikila Yehova. Zotulukapo zake zinali zakuti m’masiku ake onse, anthuwo “sanasiye kutsatila Yehova.”—2 Mbiri 34:27, 33.

19 Mofanana ndi Yosiya, acicepele ayenela kuyamba kuphunzila za Yehova akali aang’ono. Mwina Yosiya anaphunzitsidwa za cifundo ca Mulungu ndi Mfumu Manase italapa. Inu acicepele, muzigwilizana ndi acikulile okhulupilika a m’banja lanu ndi a mumpingo kuti mudziŵe zinthu zabwino zimene Yehova wawacitila. Komanso kumbukilani kuti kuŵelenga Malemba kunamukhudza mtima Yosiya ndipo kunamulimbikitsa kucitapo kanthu. Inunso mukamaŵelenga Mau a Mulungu, mudzalimbikitsidwa kucita zinthu zimene zidzawonjezela cimwemwe canu ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Mudzalimbikitsidwanso kuthandiza ena kufuna-funa Mulungu. (Ŵelengani 2 Mbiri 34:18, 19.) Cinanso, kuphunzila Baibo kudzakuthandizani kudziŵa zinthu zina zimene mufunika kuwongolela potumikila Mulungu. Mukadziŵa zimenezo, mufunika kucitapo kanthu ngati mmene Yosiya anacitila.

TUMIKILANI YEHOVA NDI MTIMA WATHUNTHU

20, 21. (a) Kodi mafumu anayi amene takambilana afanana m’mbali ziti? (b) Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambilana ciani?

20 Kodi taphunzila ciani pa zimene takambilana zokhudza mafumu anayi aciyuda amene anatumikila Yehova ndi mtima wathunthu? Iwo anali acangu ndi odzipeleka pocita cifunilo ca Mulungu. Sanaleke kucita cifunilo ca Mulungu. Anapitiliza kutumikila Mulungu ngakhale pamene anayang’anizana ndi adani oopsa. Ndipo cofunika kwambili n’cakuti anali kutumikila Yehova ndi zolinga zabwino.

21 Monga tidzaonela m’nkhani yotsatila, mafumu onse anayi amenewa analakwitsapo zinthu zina. Koma pamene Mulungu anawafufuza, anaona kuti mitima yawo inali yathunthu kwa iye. Nafenso ndife opanda ungwilo. Koma kodi Yehova akatifufuza, amaona kuti tikum’tumikila ndi mtima wathunthu? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.