Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni

3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni

BAIBO IMAFOTOKOZA ZA . . . Amuna na akazi okhulupilika amene anali “anthu monga ife tomwe,” ndipo anamvelapo mmene ife timamvela.—YAKOBO 5:17.

Tanthauzo Lake

M’Baibo muli nkhani zambili za amuna na akazi amene anavutikapo maganizo m’njila zosiyanasiyana. Pamene tiŵelenga nkhani zawo, tingapezemo wina amene anamvela mmene ife timamvela.

Mmene Zimenezi Zingatithandizile

Tonse timafuna kuti ena azitimvetsetsa. Zimenezi n’zofunika kwambili maka-maka ngati tikuvutika na matenda a maganizo. Tikamaŵelenga Baibo, timapezamo nkhani za anthu amene anali kuganiza na kumva mmene ife timamvela. Nkhanizi zimatithandiza kuzindikila kuti enanso anavutikapo mmene ife tikuvutikila. Ndipo timadziŵa kuti sindife tokha amene tikuvutika na nkhawa komanso maganizo osautsa.

  • M’Baibo muli mawu ambili okambidwa na anthu amene anasoŵa mtengo wogwila mpaka kutaya mtima. Kodi munaganizapo kuti, ‘Basi natopa nazo. Cili bwino kufa cabe’? Mose, Eliya, na Davide, nawonso anamvapo conco.—Numeri 11:14; 1 Mafumu 19:4; Salimo 55:4.

  • Baibo imatiuza za mayi wina dzina lake Hana, amene “anali wokhumudwa kwabasi” cifukwa analibe ana, ndipo anali kutonzedwa mwakhanza na mkazi mnzake.—1 Samueli 1:6, 10.

  • Baibo imatiuzanso za munthu wina, dzina lake Yobu, amene anamvapo mmene ife tingamvele. Ngakhale kuti anali na cikhulupililo colimba mwa Yehova, iye anasautsika mtima kwambili cifukwa ca mavuto, moti panthawi ina anati: “Moyo ndaukana. Sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Yobu 7:16.

Tikaona mmene anthu ochulidwa m’Baibo amenewa anakwanitsila kulimbana na nkhawa zawo, timapeza mphamvu zotithandiza kupilila mavuto athu.