Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Umoyo Wauzimu

Umoyo Wauzimu

Monga taonela m’nkhani yoyamba, anthu ambili amalemekeza Baibo monga buku lopatulika. Amaona kuti akaliŵelenga na kuseŵenzetsa uphungu wake, amalimbikitsidwa mwauzimu, ndipo amazindikila colinga ca moyo wawo.

Baibo imachulanso za anthu opanda “mzimu wa Mulungu.” (Yuda 18, 19) Anthu otelo, amaona zinthu mwakuthupi komanso amadalila maganizo awo. Koma anthu a maganizo auzimu, amalemekeza malamulo a Mulungu.—Aefeso 5:1.

CIYEMBEKEZO

MFUNDO YA M’BAIBO: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.” —Miyambo 24:10.

TANTHAUZO LAKE: Tikafooka, mphamvu zathu zotithandiza kulimbana na mavuto mu umoyo zimacepa. Koma kukhala na ciyembekezo kumatithandiza kupilila. Zingakhale zolimbikitsa kudziŵa kuti mavuto amene timakumana nawo amakhala akanthawi cabe, ndipo pambuyo pake zinthu zingasinthe n’kukhala bwino.

ZIMENE MUNGACITE: Yesetsani kuganizila zinthu zabwino zimene zidzacitika kutsogolo. M’malo mokhala na nkhawa pa zinthu zimene zingacitike kapena kuyembekezela kuti zinthu zonse mu umoyo zikhale bwino, citani zinthu mogwilizana na zolinga zanu. Ngakhale n’conco, nthawi zina “zinthu zosayembekezeleka” zimacitika ndithu. (Mlaliki 9:11) Koma kaŵili-kaŵili, zinthu zimayendako bwino kuposa mmene tinali kuganizila. Ndiye cifukwa cake Baibo imapeleka fanizo ili: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, cifukwa sukudziwa pamene padzacite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzacite bwino.”—Mlaliki 11:6.

MAYANKHO PA MAFUNSO OFUNIKA KWAMBILI MU UMOYO

MFUNDO YA M’BAIBO: “Ndithandizeni kukhala wozindikila . . . Mawu anu onse ndi coonadi.”—Salimo 119:144, 160.

TANTHAUZO LAKE: Baibo imapeleka mayankho pa mafunso amene pafupi-fupi aliyense amafunsa. Mwacitsanzo, imapeleka mayankho pa mafunso akuti,

  • Kodi anthufe tinacokela kuti?

  • N’cifukwa ciani tili na moyo?

  • N’ciani cimacitika munthu akamwalila?

  • Kodi moyo ni uno cabe umene ulipo?

Anthu ofika m’mamiliyoni kuzungulila dziko lonse, umoyo wawo wakhala wabwino mwa kumvetsetsa mayankho a m’Baibo pa mafunso amenewa komanso ena.

ZIMENE MUNGACITE: Yesetsani kudziŵelengela mwekha zimene Baibo imaphunzitsa. Ndipo pemphani wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kuimvetsetsa Baibo. Yendani pa webusaiti yathu ya jw.org, kapena mukabwele ku misonkhano yathu. Kungena ni mahala, ndipo aliyense ni wolandilidwa.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBO

Tambani vidiyo yopezeka pa jw.org, yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibo? Vidiyoyi ipezeka m’vitundu vopitilila 880

MUZIONA ZINTHU ZAUZIMU KUKHALA ZOFUNIKA

“Odala ndi anthu amene amazindikila zosowa zawo zauzimu.”​—MATEYU 5:3.

DZIŴANI ZAMBILI ZA MULUNGU AMENE ANALEMBA BAIBO.

‘Funani-funani Mulungu ndipo mudzamupezadi. Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.’​—MACHITIDWE 17:27.

ŴELENGANI NA KUSINKHA-SINKHA PA UTHENGA WA M’BAIBO.

“Amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, * ndipo amawelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku. . . . Zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.”​—SALIMO 1:2, 3.

^ ndime 23 Yehova ni dzina la Mulungu lopezeka m’Baibo.