Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zimene Oŵelenga Amafunsa . . .

Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?

Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?

Inde, padziko lonse pali akazi ambili-mbili a Mboni za Yehova amene amaphunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Iwo amalalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Lemba ya Salimo 68:11 limanena kuti: “Yehova wapeleka lamulo, ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”

Komabe zimene akazi a Mboni za Yehova amacitazi n’zosiyana kwambili na zimene abusa aakazi amacita m’zipembedzo zina. Kodi zimasiyana bwanji?

Atsogoleli aakazi a zipembedzo zina, maka-maka zacikhristu, amakhala na udindo mumpingo ndipo amaphunzitsa anthu a mumpingomo. Koma akazi a Mboni za Yehova saphunzitsa mumpingo, koma amaphunzitsa anthu amene amawapeza akamalalikila kunyumba na nyumba komanso kumalo ena.

Kusiyana kwina pakati pa akazi a Mboni za Yehova na akazi a m’zipembedzo zina n’kwakuti, akazi a Mboni za Yehova sakhala atsogoleli mumpingo. Akazi a zipembedzo zina amakhala atsogoleli m’mipingo yawo n’kumapeleka malangizo kwa anthu a mumpingomo. Koma akazi a Mboni saphunzitsa mumpingo pokha-pokha ngati palibe mwamuna wobatizika. Amuna oikidwa okha ni amene amaphunzitsa mumpingo.—1 Timoteyo 3:2; Yakobo 3:1.

Baibo imasonyeza kuti amuna ni amene amayenela kukhala na udindo woyang’anila mumpingo. Taonani dongosolo limene mtumwi Paulo anafotokoza pamene anali kulembela kalata woyang’anila mnzake, dzina lake Tito. Iye anati: “Ndinakusiya ku Kerete kuti . . . uike akulu mumzinda uliwonse.” Paulo ananenanso kuti munthu woikidwayo “ayenela kukhala wopanda cifukwa comunenezela, mwamuna wa mkazi mmodzi.” (Tito 1:5, 6) Paulo anapelekanso malangizo ofanana na amenewa m’kalata yake imene analembela Timoteyo. Iye anati: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anila, akufuna nchito yabwino. Woyang’anila akhale wopanda cifukwa comunenezela, mwamuna wa mkazi mmodzi, . . . wotha kuphunzitsa.”—1 Timoteyo 3:1, 2.

N’cifukwa ciani amuna okha ni amene ayenela kupatsidwa udindo woyang’anila mumpingo? Paulo ananena kuti: “Sindikuvomeleza kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala na ulamulilo pa mwamuna, koma azikhala cete. Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa, kenako Hava.” (1 Timoteyo 2:12, 13) Conco zimene Mulungu anacita polenga mwamuna poyamba asanalenge mkazi, zikusonyeza kuti iye amafuna kuti amuna ndiye azikhala na udindo woyang’anila na kuphunzitsa mumpingo.

Amuna na akazi a Mboni za Yehova amatsatila citsanzo ca Mtsogoleli wawo, Yesu Khristu. Pofotokoza zimene Yesu anali kucita, Luka analemba kuti: “Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ni mzinda komanso mudzi ni mudzi. Ulendowu unali wokalalikila na kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” Kenako Yesu anatumiza otsatila ake kuti akagwile nchito yomweyi. Baibo imati iwowo “ananyamuka ndi kulowa m’delalo m’mudzi ndi mudzi. Iwo anali kulengeza uthenga wabwino.”—Luka 8:1; 9:2-6..

Masiku ano amuna na akazi a Mboni za Yehova amagwilanso ntchito imeneyi, yomwe Yesu analosela. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.