Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBO IMASINTHA ANTHU

N’nali Kuopa Imfa

N’nali Kuopa Imfa
  • CAKA COBADWA: 1964

  • DZIKO: ENGLAND

  • MBILI: MAYI WACICEPELE KOMANSO WOSAMVELA

MBILI YANGA

N’nabadwila m’tauni yokhala na anthu ambili yochedwa Paddington, mumzinda wa London, ku England. N’nali kukhala na amayi, na azikulu anga atatu. Atate sitinali kukhala nawo nthawi zambili cifukwa anali cakolwa.

Pamene n’nali mwana, amayi ananiphunzitsa kupemphela usiku uliwonse. N’nali na kabaibo kakang’ono kokhala na buku la Masalimo cabe. Ndipo n’napanga matyuni kuti niziyimba nyimbo za Masalimo. Nikumbukila kuti tsiku lina n’naŵelenga mau m’buku linalake amene sanali kucoka m’maganizo mwanga. Mau amenewo anali akuti: “Tsiku lina dziko lidzatha.” Tsiku limenelo n’nakangiwa kugona usiku wonse. N’nali kungoganizila za tsogolo langa. N’nali kuganiza kuti: ‘Moyo uyenela kukhala na colinga. N’cifukwa ciani nili na moyo?’ N’nali kuopa imfa kwambili.

Conco, n’nayamba kucita cidwi ndi zamizimu. N’nayesa kukamba na anthu akufa, n’nali kupita kumanda pamodzi na anzanga a kusukulu, ndiponso tinali kutamba mafilimu ocititsa mantha. Tinali kuona kuti zinali zosangalatsa olo kuti zinali zocititsa mantha.

N’nayamba khalidwe losamvela nili na zaka 10 cabe. N’nayamba kupepa fwaka ndipo posapita nthawi, cinakhala cizoloŵezi canga. Pambuyo pake, n’nayamba kupepanso camba. N’tafika zaka 11, n’nayamba kumwa mowa. Ngakhale kuti sunali kunikomela, n’nali kuukonda cifukwa n’nali kuledzela nawo. N’nali kukondanso nyimbo ndi kuvina. Conco, n’nali kupita ku mapati na ku manaitikilabu nthawi iliyonse imene nafuna. N’nali kucoka panyumba usiku mwakazembela ndi kubwelelako m’mamaŵa kukali mdima. Cifukwa colema, nthawi zambili n’nali kulova kusukulu. Ndipo ngati napita kusukulu, n’nali kumwa mowa atica akatuluka m’kalasi.

N’nafeluka mayeso otsiliza pa sukulu. Poyamba amayi sanali kudziŵa bwino za khalidwe langa. Koma nitafeluka, anadziŵa ndipo anakhumudwa ngako. Tinakangana kwambili cakuti ine n’nathawa panyumba. Kwa kanthawi ndithu, n’nali kukhala na cisumbali canga, dzina lake Tony. Iye anali wosamvela malamulo, anali kugulitsa mankhwala osokoneza ubongo ndiponso anali na mbili yakuti anali wankhanza ngako. Posakhalitsa, n’nakhala na mimba ndipo n’nabeleka mwana wamwamuna nili na zaka 16 cabe.

MMENE BAIBO INASINTHILA UMOYO WANGA

N’nakumana na Mboni za Yehova koyamba pamene n’nali kukhala m’nyumba za boma zokhala azimayi wosakwatiwa ndi ana awo akhanda. Kumeneko, ananipatsa cipinda kuti nizikhalamo. Azimayi aŵili a Mboni za Yehova anali kubwela nthawi zonse kukaphunzitsa Baibo anzanga ena. Tsiku lina, n’napezekapo pamene azimayiwo anali kuphunzitsa anzangawo. Colinga canga cinali cakuti nionetse kuti zimene a Mboniwo anali kuphunzitsa n’zabodza. Koma iwo anayankha mafunso anga onse moleza mtima komanso momveka bwino kucokela m’Baibo. Anali okoma mtima ndi odekha, ndipo izi zinanicititsa cidwi kwambili. Conco, n’navomela kuti aziniphunzitsa Baibo.

Posakhalitsa, n’naphunzila mfundo ina m’Baibo imene inasintha umoyo wanga. Kuyambila nili mwana, n’nali kuopa imfa. Koma zinthu zinasintha n’taphunzila za ciukililo cimene Yesu anali kuphunzitsa. (Yohane 5:28, 29) N’naphunzilanso kuti Mulungu amanikonda. (1 Petulo 5:7) Maka-maka mau a pa Yeremiya 29:11, ananikhudza mtima kwambili. Mauwo amati: “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizila zokupatsani mtendele osati masoka, kuti mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watelo Yehova.” Conco n’nayamba kukhulupilila kuti n’zotheka ine kudzakhala na moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi.—Salimo 37:29.

Mboni za Yehova zinanionetsa cikondi ceni-ceni. N’tapezeka pamisonkhano yawo kwa nthawi yoyamba, n’nasangalala ngako. Aliyense anali waubwenzi. (Yohane 13:34, 35) Izi zinali zosiyana kwambili na mmene zinalili kuchechi kwathu. A Mboni za Yehova ananilandila mosasamala kanthu za mmene umoyo wanga unalili. Anali kunimvetsela na kunithandiza pa zinthu zambili. N’namvela monga kuti nili m’banja lalikulu lokondana kwambili.

N’taphunzila Baibo, n’nazindikila kuti nifunika kusintha zina na zina paumoyo wanga kuti nikhale na makhalidwe abwino amene Mulungu afuna. Koma zinanivuta ngako kuti nileke kupepa fwaka. Komanso n’nazindikila kuti nyimbo zina zinali kunicititsa kukhala na cilako-lako cofuna kukoka camba. Conco, n’naleka kumvetsela nyimbo zimenezo. Pofuna kupewa kukhala woledzela, n’naleka kupita ku mapati na ku manaitikilabu, cifukwa nikapita kumeneko n’nali kukakamizika kumwa mowa kwambili. Kuwonjezela apo, n’nayesetsa kupeza anzanga ena amene n’naona kuti anganithandize kukhala na khalidwe labwino.—Miyambo 13:20.

Panthawiyo, nayenso Tony anali kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Iye ataona kuti a Mboni za Yehova ayankha mafunso ake mwa kuseŵenzetsa Baibo, anazindikila kuti wapeza coonadi. Conco anasintha umoyo wake. Analeka khalidwe losamvela malamulo, kugwilizana ndi anthu aciwawa, ndi kukoka camba. Kuti tikondweletse Yehova, tonse tinaona kuti tifunika kusintha khalidwe lathu loipa kuti tilele bwino mwana wathu. Conco, mu 1982, tinakwatilana.

Masiku ano, sinilephelanso kugona usiku cifukwa coopa zamtsogolo kapena imfa”

Nikumbukila kuti nthawi ina n’nali kufufuza m’magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani * nkhani za anthu amene anakwanitsa kusintha umoyo wawo monga mmene ine n’nafuna kucitila. N’taŵelenga nkhanizo, n’nalimbikitsidwa kwambili. N’naona kuti nifunika kupitiliza kuyesa-yesa kuti nisinthe. Nthawi zonse n’nali kupemphela kwa Yehova kuti apitilize kunithandiza. Ine na Tony tinabatizika monga Mboni za Yehova mu July 1982.

MAPINDU AMENE NAPEZA

Kukhala pa ubwenzi na Yehova Mulungu kunapulumutsa moyo wanga. Ndipo ine na Tony taona kuti Yehova wakhala akutithandiza panthawi zovuta. Taphunzila kudalila Mulungu panthawi zovuta, ndipo taona kuti nthawi zonse Iye wakhala akuthandiza ndi kulimbitsa banja lathu.—Salimo 55:22.

Nimakondwela kuona kuti n’nathandiza ana anga kudziŵa Yehova ngati mmene ine nacitila. Komanso nimakondwela poona kuti adzukulu anga nawonso akuphunzila za Mulungu.

Masiku ano, sinilephelanso kugona usiku cifukwa coopa zamtsogolo kapena imfa. Ine na Tony ndife otangwanika na nchito yoyendela ndi kulimbikitsa mipingo yosiyana-siyana ya Mboni za Yehova mlungu uliwonse. Pamodzi ndi abale a m’mipingoyi, timagwila nchito yophunzitsa ena kuti ngati aonetsa cikhulupililo mwa Yesu, adzapeza moyo wamuyaya.

^ par. 17 Ofalitsidwa na Mboni za Yehova.