Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KHALANI MASO!

Zimene Zinacitikila Mboni za Yehova pa Cipululutso ca Nazi—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Zimene Zinacitikila Mboni za Yehova pa Cipululutso ca Nazi—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Pa January 27, 2023, anthu ambili adzacita Mwambo wa Padziko Lonse Wokumbukila Cipululutso ca Ulamulilo wa Nazi. Nkhanza zopululutsa anthu zimene zinacitika zaka zoposa 75 zapitazo, zingakupangitseni kufunsa modabwa kuti ‘N’cifukwa ciyani Mulungu analolela anthu kupululutsidwa mwankhaza cotelo?’

 Ayuda ambili anavutika koopsa m’nyengo ya Cipululutso imeneyi. Mamiliyoni anaphedwa mwankhanza mwa ndondomeko yocita kukonza. Panalinso magulu ena a anthu omwe anazuzidwa na kuphedwa pa Cipululutso cimeneci. Limodzi la maguluwo linali Mboni za Yehova. Iwo anazunzidwa na kuphedwa cifukwa ca cikhulupililo cawo cozikika m’Baibo.

“Ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino”

 Anthu ambili amada nkhaŵa kuti mwina Cipululutso monga ca ulamulilo wa Nazi cingadzacitikenso. Bwino lake n’lakuti Baibo imalonjeza tsogolo labwino pamene mavuto otelewa sadzacitikanso.

  •   “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizila zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watelo Yehova.”—Yeremiya 29:11. a

 Lonjezo limeneli lidzakwanilitsidwa Mulungu akadzacotsapo anthu oipa na mavuto onse: Posacedwa Mulungu adzacita zotsatilazi;

  •   Adzacotsapo amene amapweteka anzawo.—Miyambo 2:22.

  •   Adzacilitsa onse amene akukumana na mavuto.—Chivumbulutso 21:4.

  •   Adzaukitsa onse amene anamwalila kuti adzakhale na moyo padziko lapansi.—Yohane 5:28, 29.

 Ikhulupilileni Baibo na ciyembekezo cotonthoza cimene imapeleka. Kuti mudziŵe cifukwa cake, tikupemphani kuti muyambe kuphunzila Baibo kwaulele na Mboni za Yehova.

a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.