Onani zimene zilipo

Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?

Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?

Yankho la m’Baibo

 Iyai. Baibo sikamba kuti ndalama n’zoipa, kapenanso kuti n’zimene zimabweletsa mavuto. Zimene anthu ambili amakonda kukamba zakuti “ndalama ndiye muzu wa zoipa zonse” si zoona, ndipo zimangoonetsa kuti samvetsa zimene Baibo imakamba. Baibo imati “kukonda ndalama ndi muzu wa zoipa zonse.”—1 Timoteyo 6:10.

 Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya ndalama?

 Baibo imakamba kuti ndalama tikamazigwilitsa nchito mwanzelu, zikhoza kutithandiza komanso ‘kutiteteza.’ (Mlaliki 7:12) Kuwonjezela apo, Baibo imayamikila anthu amene amathandiza anzawo, zimene zingaphatikizepo kuwapatsa ndalama.—Miyambo 11:25.

 Komabe, imaticenjezanso kuti tisamakonde kwambili ndalama. Imati: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” (Aheberi 13:5) Apa mfundo ni yakuti tiziona ndalama moyenela, ndipo tipewe kumangofuna-funa cuma. Tizikhala okhutila na zinthu zimene timafunikila, monga cakudya, zovala, komanso pogona.—1 Timoteyo 6:8.

 N’cifukwa ciyani Baibo imati kukonda ndalama n’koipa?

 Anthu a umbombo sadzapeza moyo wosatha. (Aefeso 5:5) Cifukwa cake n’cakuti umbombo ni mbali ya kulambila mafano kapena kulambila konyenga. (Akolose 3:5) Cina, anthu a umbombo kambili amaphwanya mfundo za m’Baibo kuti apeze zimene akufuna. Miyambo 28:20 imakamba kuti munthu “woyesetsa kuti apeze cuma mofulumila, sadzapitiliza kukhala wosalakwa.” Iye angafike ngakhale pocita zinthu zoipa, monga ciphuphu, kulanda zinthu za ena mokakamiza, cinyengo, kuba anthu n’kukawasunga, kapena kupha anthu.

 Olo kuti kukonda ndalama sikungacititse anthu kukhala na makhalidwe oipa, kumakhala na zotulukapo zina zoipa. Baibo imati: “Anthu ofunitsitsa kulemela, amagwela m’mayeselo ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambili zowapweteketsa.”—1 Timoteyo 6:9.

 Kodi timapindula bwanji na malangizo a m’Baibo pa nkhani ya ndalama?

 Tikamapewa kuphwanya mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino pa nkhani ya ndalama, tidzadzisungila ulemu ndipo Mulungu adzakondwela nafe komanso adzaticilikiza. Mulungu analonjeza anthu amene amayesetsa kumukondweletsa kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheberi 13:5, 6) Iye amatitsimikizilanso kuti “munthu wocita zinthu mokhulupilika adzapeza madalitso ambili.”—Miyambo 28:20.