1 Samueli 17:1-58

  • Davide anagonjetsa Goliyati (1-58)

    • Goliyati ankanyoza Aisiraeli (8-10)

    • Davide anadzipereka kukamenyana ndi Goliyati (32-37)

    • Davide anamenya nkhondo mʼdzina la Yehova (45-47)

17  Ndiyeno Afilisiti+ anasonkhanitsa asilikali awo* kuti akamenye nkhondo. Anasonkhana ku Soko+ mʼdera la Yuda ndipo anamanga msasa wawo pakati pa Soko ndi Azeka+ ku Efesi-damimu.+  Sauli ndi asilikali a Isiraeli anasonkhana nʼkumanga msasa mʼchigwa cha Ela,+ ndipo anakonzeka kuti amenyane ndi Afilisiti.  Afilisitiwo anali paphiri kumbali ina ndipo Aisiraeli analinso paphiri kumbali ina. Pakati pawo panali chigwa.  Ndiyeno kumsasa wa Afilisiti kunatuluka ngwazi,* dzina lake Goliyati,+ wa ku Gati.+ Iye anali wamtali pafupifupi mamita atatu.*  Anavala chipewa chakopa* ndi chovala chamamba achitsulo. Kopa wa chovala chamambachi+ anali wolemera pafupifupi makilogalamu 57.*  Iye anavalanso zoteteza miyendo zakopa komanso anakolekera nthungo+ yakopa kumsana kwake.  Mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtengo wogwiritsa ntchito powomba nsalu,+ ndipo mutu wachitsulo wa mkondowo unali wolemera makilogalamu pafupifupi 7.* Munthu womunyamulira chishango chake ankayenda patsogolo pake.  Kenako iye anaima nʼkuyamba kufuulira asilikali a Isiraeli+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwera nʼkuyalana kuti mumenye nkhondo? Ine ndabwera kudzamenyera nkhondo Afilisiti ndipo inu ndinu antchito a Sauli. Ndiye sankhani munthu woti amenyane nane ndipo abwere kuno.  Ngati angathe kumenyana nane nʼkundipha, ndiye kuti tidzakhala antchito anu. Koma ngati ndingamugonjetse mpaka kumupha, inuyo mudzakhala antchito athu ndipo muzititumikira.” 10  Mfilisitiyo anapitiriza kunena kuti: “Ine ndikunyoza asilikali a Isiraeli+ lero. Ndipatseni munthu woti ndimenyane naye!” 11  Sauli ndi Aisiraeli onse atamva mawu a Mfilisitiwa anachita mantha kwambiri. 12  Davide anali mwana wa Jese wa ku Efurata+ ku Betelehemu,+ ku Yuda. Jese+ anali ndi ana aamuna 8+ ndipo mʼmasiku a Sauli, Jese anali atakalamba. 13  Ana atatu aakulu a Jese anapita ndi Sauli kunkhondo.+ Woyamba kubadwa dzina lake anali Eliyabu,+ wachiwiri anali Abinadabu+ ndipo wachitatu anali Shama.+ 14  Davide anali wamngʼono kwambiri+ pa onse ndipo ana atatu aakulu a Jese anatsatira Sauli. 15  Davide ankapita kwa Sauli kenako nʼkubwerera ku Betelehemu kukaweta nkhosa+ za bambo ake. 16  Kwa masiku 40, Mfilisiti uja ankabwera mʼmawa ndi madzulo kudzanyoza Aisiraeli. 17  Kenako Jese anauza mwana wake Davide kuti: “Tenga tirigu wokazinga uyu wokwana muyezo umodzi wa efa* ndi mikate 10, ndipo upite nazo mofulumira kwa azichimwene ako kumsasa. 18  Utengenso mapisi 10 awa a tchizi* ukapatse mtsogoleri wa gulu la anthu 1,000. Ukafufuzenso kuti azichimwene ako ali bwanji, ndipo akakupatse chizindikiro chosonyeza kuti ali bwino.” 19  Ana a Jesewo anali ndi Sauli komanso amuna ena onse a Isiraeli mʼchigwa cha Ela+ kuti amenyane ndi Afilisiti.+ 20  Choncho Davide anadzuka mʼmamawa ndipo nkhosa zake anasiyira munthu wina. Iye analongedza katundu wake nʼkunyamuka mogwirizana ndi zimene bambo ake anamuuza. Atafika mumsasa, anapeza asilikali akupita kumalo omenyera nkhondo kwinaku akufuula. 21  Ndiyeno asilikali a Aisiraeli anayangʼanizana ndi asilikali a Afilisiti pokonzekera nkhondo. 22  Nthawi yomweyo, Davide anasiya katundu wake kwa munthu amene ankasamalira katundu, ndipo anathamangira kumalo omenyera nkhondo. Atafika, anayamba kufunsa ngati azichimwene ake ali bwino.+ 23  Pamene ankalankhula ndi asilikaliwo, ngwazi ija inatulukira kuchokera pakati pa asilikali a Afilisiti. Dzina la ngwaziyo linali Goliyati,+ Mfilisiti wa ku Gati. Iye anayamba kulankhula mawu omwe aja amene analankhula poyamba,+ ndipo Davide nayenso anamva. 24  Asilikali onse a Isiraeli ataona Goliyati, anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kuthawa.+ 25  Ndiyeno asilikali a Isiraeli anayamba kunena kuti: “Mukumuona munthu akubwera apoyo? Iye amabwera kudzanyoza Aisiraeli.+ Munthu amene angamenyane naye nʼkumupha, mfumu idzamʼpatsa chuma chochuluka komanso mwana wake wamkazi.+ Kuwonjezera pamenepo, nyumba ya bambo ake a munthuyo idzasiya kupereka zinthu zimene Aisiraeli ayenera kupereka kwa mfumu.” 26  Davide anayamba kufunsa asilikali amene anali naye pafupi kuti: “Kodi munthu amene angaphe Mfilisitiyu nʼkuchititsa kuti Aisiraeli asiye kunyozedwa amupatsa chiyani? Kodi Mfilisiti wosadulidwa ameneyu ndi ndani kuti azinyoza asilikali a Mulungu wamoyo?”+ 27  Anthuwo anamuuzanso zimene anamuuza poyamba paja. Kenako anati: “Munthu amene angaphe Mfilisiti ameneyu amʼchitira zimenezi.” 28  Eliyabu+ mchimwene wake wamkulu wa Davide atamva Davideyo akulankhula ndi anthuwo, anapsa naye mtima kwambiri. Iye anati: “Wabwera kudzatani kuno? Nanga nkhosa zochepa zija wasiyira ndani kuchipululu?+ Ine ndikudziwa bwino kuti ndiwe wodzikuza komanso uli ndi maganizo olakwika. Iweyo wabwera kuno kuti udzaone mmene nkhondo ikuyendera.” 29  Davide anayankha kuti: “Kodi ndalakwa chiyani? Inetu ndangofunsa.” 30  Atatero, anachokapo nʼkupita kwa munthu wina ndipo anafunsanso funso lomwe lija.+ Anthu anamuyankhanso chimodzimodzi ngati poyamba paja.+ 31  Anthu anamva zimene Davide ananena ndipo anakauza Sauli. Choncho Sauli anaitanitsa Davide. 32  Davide anauza Sauli kuti: “Aliyense asachite naye mantha.* Ine mtumiki wanu ndipita kukamenyana naye Mfilisiti ameneyu.”+ 33  Koma Sauli anauza Davide kuti: “Sungapite kukamenyana ndi Mfilisiti ameneyu chifukwa ndiwe mwana.+ Mfilisitiyu wakhala akumenya nkhondo kuyambira ali mnyamata.” 34  Davide anauza Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala mʼbusa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwera mkango+ komanso chimbalangondo ndipo chilombo chilichonse chinagwira nkhosa. 35  Zitatero, ndinatsatira chilombocho nʼkuchimenya, ndipo ndinapulumutsa nkhosa mʼkamwa mwake. Chitayamba kundilusira ndinachikoka ubweya* nʼkuchipha. 36  Ine mtumiki wanu ndinapha zilombo ziwiri zonsezi, mkango komanso chimbalangondo. Mfilisiti wosadulidwayu akhalanso ngati chimodzi mwa zilombo zimenezi, chifukwa wanyoza asilikali a Mulungu wamoyo.”+ 37  Davide anawonjezera kuti: “Yehova amene anandipulumutsa mʼkamwa mwa mkango ndi mʼkamwa mwa chimbalangondo andipulumutsanso mʼmanja mwa Mfilisiti ameneyu.”+ Sauli anauza Davide kuti: “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.” 38  Choncho Sauli anamuveka Davide zovala zake. Anamuveka chipewa chakopa komanso chovala chamamba achitsulo. 39  Kenako Davide anamangirira lupanga pazovala zake. Koma atanyamuka kuti azipita, analephera kuyenda chifukwa zovalazo sanazizolowere. Davide anauza Sauli kuti: “Sinditha kuyenda nazo zovala zimenezi chifukwa sindinazizolowere.” Atatero, Davide anavula zovalazo. 40  Ndiyeno anatenga ndodo mʼmanja mwake nʼkusankha miyala 5 yosalala yakumtsinje.* Iye anaika miyalayi mʼchikwama chake cha kubusa ndipo ananyamulanso gulaye*+ mʼmanja mwake. Kenako anayamba kupita kumene kunali Mfilisiti uja. 41  Mfilisiti uja ankayandikira kumene kunali Davide. Patsogolo pake panali munthu amene ankamunyamulira chishango chake. 42  Mfilisitiyo ataona Davide, anayamba kumuderera komanso kumunyoza chifukwa ankangooneka kuti ndi kamnyamata kooneka bwino.+ 43  Choncho iye anafunsa Davide kuti: “Kodi ine ndine galu+ kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Atatero, anatemberera Davide mʼdzina la milungu yake. 44  Iye anauzanso Davide kuti: “Tangoyerekeza kubwera kuno, ndipereka mnofu wako kwa mbalame zamumlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire.” 45  Davide anayankha Mfilisitiyo kuti: “Iwe ukubwera kudzamenyana ndi ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo,+ koma ine ndikubwera kudzamenyana nawe mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wamunyoza.+ 46  Lero Yehova akupereka mʼmanja mwanga,+ ndipo ndikupha nʼkukudula mutu. Lero ndipereka mitembo ya asilikali amʼmisasa ya Afilisiti kwa mbalame zamumlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire. Anthu onse apadziko lapansi adzadziwa kuti Aisiraeli ali ndi Mulungu.+ 47  Ndipo onse amene asonkhana panowa adziwa* kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo,+ chifukwa Yehova ndiye mwini nkhondo,+ ndipo nonsenu akuperekani mʼmanja mwathu.”+ 48  Mfilisiti uja anayamba kupita kumene kunali Davide. Nayenso Davide anayamba kuthamanga mofulumira kupita kumalo omenyera nkhondo kuti akakumane naye. 49  Davide anapisa dzanja mʼchikwama chake nʼkutenga mwala. Kenako anauponya ndi gulaye moti unamenya Mfilisiti uja pamphumi nʼkuloweratu mʼmutu mwake, ndipo anagwa pansi chafufumimba.+ 50  Choncho Davide anagonjetsa Mfilisitiyo pogwiritsa ntchito gulaye ndi mwala. Iye anamugwetsa nʼkumupha ngakhale kuti Davide analibe lupanga mʼmanja mwake.+ 51  Kenako Davide anathamanga nʼkukaima pambali pake. Atatero anasolola lupanga la Mfilisitiyo+ mʼchimake nʼkumudula mutu pofuna kutsimikizira kuti wafadi. Afilisiti ataona kuti ngwazi yawo yamphamvu ija yafa, anayamba kuthawa.+ 52  Zitatero, asilikali a Aisiraeli ndi Yuda anayamba kufuula ndipo anathamangitsa Afilisiti kuyambira kuchigwa+ mpaka kumageti a mzinda wa Ekironi.+ Mitembo ya Afilisiti amene anaphedwa inali mbwee mʼnjira monse kuchokera ku Saaraimu+ mpaka kukafika ku Gati mpaka ku Ekironi. 53  Aisiraeli atabwerako kothamangitsa Afilisiti, anapita kumsasa wa Afilisiti kukatenga zinthu za Afilisitiwo. 54  Kenako Davide anatenga mutu wa Mfilisiti uja nʼkupita nawo ku Yerusalemu koma zida za Mfilisitiyo anaziika mutenti yake.+ 55  Pa nthawi imene Davide ankapita kukakumana ndi Mfilisiti uja, Sauli anafunsa Abineri,+ mkulu wa asilikali, kuti: “Abineri, kodi ameneyu ndi mwana wa ndani?”+ Abineri anayankha kuti: “Ndithu mfumu muli apa,* ine sindikudziwa.” 56  Atatero mfumuyo inati: “Ufufuze kuti mnyamata ameneyu ndi mwana wa ndani.” 57  Choncho Davide atangofika kuchokera komwe anapha Mfilisiti, Abineri anamutenga nʼkupita naye kwa Sauli, mutu wa Mfilisiti+ uja uli mʼmanja. 58  Ndiyeno Sauli anamufunsa kuti: “Mnyamata iwe, kodi bambo ako ndi ndani?” Davide anayankha kuti: “Ndine mwana wa mtumiki wanu Jese,+ wa ku Betelehemu.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “misasa yawo.”
Kutanthauza “msilikali woimira gulu lake lankhondo amene ankalimbana ndi msilikali woimira gulu la adani awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 6 ndi chikhatho chimodzi.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “chamkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masekeli 5,000.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “masekeli 600.” Onani Zakumapeto B14.
Pafupifupi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Tchizi ndi chakudya chopangidwa kuchokera ku mkaka.
Kapena kuti, “asataye mtima.”
Kapena kuti, “munsagwada.” Mʼchilankhulo choyambirira, “ndevu.”
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.
Kapena kuti, “yakuchigwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mpingo wonsewu udziwa.”
Kapena kuti, “Ndikulumbira pali moyo wanu mfumu.”