Pitani ku nkhani yake

Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo

Dziwani tanthauzo lenileni la mavesi komanso mawu ena odziwika bwino a m’Baibulo. Werengani mawuwo mu nkhani yake yonse ndi kudziwa zomwe zinachititsa kuti alembedwe. Mbaliyi, ikuthandizani kuti muzimvetsa mozama mawu a Mulungu pogwiritsa ntchito mawu am’munsi komanso malifalensi.

Kufotokoza Genesis 1:1​—“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi”

Kodi mawu oyamba a m’Baibulowa amanena mfundo ziwiri ziti zomwe ndi zoona komanso zofunika?

Kufotokoza Ekisodo 20:12​—“Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”

Mulungu analimbikitsa Aisiraeli kutsatira lamuloli powalonjeza zinthu zabwino.

Kufotokoza Yoswa 1:9​—“Ukhale Wolimba Mtima Ndipo Uchite Zinthu Mwamphamvu”

Kodi mungakhale bwanji olimba mtima n’kumachita zinthu mwamphamvu mukakumana ndi mavuto aakulu kwambiri?

Kufotokoza Salimo 23:4​—“Ndingakhale Ndiyenda M’chigwa cha Mthunzi wa Imfa”

Ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri, kodi Mulungu amateteza bwanji anthu ake?

Salimo 37:4​—“Udzikondweretsenso Mwa Yehova”

Kodi salimoli limatithandiza bwanji kuti tikhale anzeru komanso anthu amene Mulungu amasangalala nawo?

Kufotokoza Salimo 46:10​—“Khalani Chete, Ndipo Dziwani Kuti Ine Ndine Mulungu”

Kodi vesi limeneli limangotanthauza kukhala chete m’tchalitchi?

Kufotokoza Mlaliki 3:11​​—“Chilichonse Iye Anachipanga Chokongola Ndiponso pa Nthawi Yake”

Zinthu zokongola zimene Mulungu analenga zimaphatikizaponso zinthu zambiri. Kodi zimenezi zimakukhudzani bwanji?

Kufotokoza Yesaya 40:31​—“Anthu Odalira Yehova Adzapezanso Mphamvu”

N’chifukwa chiyani Malemba amayerekezera chiwombankhanga chouluka ndi munthu amene amalandira mphamvu zochokera kwa Mulungu?

Kufotokoza Yesaya 41:10​—“Usachite Mantha, Pakuti Ndili Nawe”

Yehova anagwiritsa ntchito mfundo zitatu pofuna kutsimikizira anthu ake okhulupirika kuti aziwathandiza.

Kufotokoza Yesaya 42:8​—“Ine ndine AMBUYE”

Kodi Mulungu anadzipatsa dzina lenileni liti?

Kufotokoza Mika 6:8​—“Uziyenda Modzichepetsa Ndi Mulungu Wako”

Vesili likufotokoza mwachidule zinthu zitatu zofunika zomwe Mulungu amayembekezera kuti tizichita.

Kufotokoza Mateyu 6:33​​—“Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba”

Kodi Yesu ankatanthauza kuti Akhristu sayenera kugwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo?

Kufotokoza Mateyu 6:34​—“Musadere Nkhawa za Mawa”

Yesu sankatanthauza kuti sitiyenera kukonzekera za m’tsogolo.

Kufotokoza Mateyu 11:28-30—“Bwerani Kwa Ine . . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

Kodi Yesu ankathandiza anthu omwe ankaponderezedwa kupeza mpumulo nthawi yomweyo?

Kufotokoza Maliko 1:15​—“Ufumu wa Mulungu Wayandikira”

Kodi Yesu ankatanthauza kuti Ufumu unali utayamba kale kulamulira?

Maliko 11:24 Kufotokoza​—“Zinthu Zilizonse Mukazipemphera Ndi Kuzipempha, Khulupirirani Kuti Mwazilandira”

Kodi malangizo a Yesu okhudza pemphero ndi chikhulupiriro angatithandize bwanji kupirira masiku ano?

Luka 1:37​—“Chifukwa Zimene Mulungu Wanena Sizilephereka”

Palibe chimene chingalepheretse Mulungu Wamphamvuyonse kukwaniritsa malonjezo ake. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

Kufotokoza Yohane 1:1​—“Pachiyambi Panali Mawu”

Lembali limatiuza zinthu zokhudza moyo wa Yesu Khristu asanabwere padzikoli.

Kufotokoza Yohane 3:16 ​—“Mulungu Anakonda Kwambiri Dziko”

Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti amakonda munthu aliyense payekha ndipo amafuna kuti tidzapeze moyo wosatha?

Kufotokoza Yohane 14:6​—“Ine Ndine Njira, Choonadi ndi Moyo”

N’chifukwa chiyani munthu amene akufuna kulambira Yehova ayenera kuzindikira udindo wofunika wa Yesu?

Kufotokoza Yohane 15:13​​—“Palibe Munthu Ali Nacho Chikondi Choposa Ichi”

Kodi otsatira a Yesu angasonyeze bwanji chikondi ngati chomwe Yesu anasonyeza?

Kufotokoza Yohane 16:33​—“Ndaligonjetsa Dziko”

Kodi mawu a Yesuwa amatsimikizira bwanji otsatira a Yesu kuti angakwanitse kusangalatsa Mulungu?

Kufotokoza Aroma 5:8​​—“Pamene Tinali Ochimwa, Khristu Anatifera”

Nthawi zambiri, maganizo ndi zochita za anthu ochimwafe zimakhala zosemphana ndi mfundo zachilungamo za Mulungu. Ndiye zingatheke bwanji kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu panopa n’kudzakhala ndi moyo wosatha?

Kufotokoza Aroma 10:13​—“Adzaitana pa Dzina la Ambuye”

Mulungu amapatsa munthu aliyense mwayi woti adzapulumuke n’kukhala ndi moyo wosatha, mosatengera dziko limene amachokera, mtundu wake, udindo wake kapena ndalama zimene ali nazo.

Aroma 12:12—“Kondwerani ndi Chiyembekezocho. Pirirani Chisautso. Limbikirani Kupemphera”

Kodi Akhristu angakwanitse bwanji kukhalabe okhulupirika ngakhale pomwe akuzunzidwa komanso kukumana ndi mavuto ena?

Kufotokoza Aroma 15:13​—“Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere.”

Kodi makhalidwe ngati chimwemwe ndi mtendere amagwirizana bwanji ndi chiyembekezo komanso mzimu woyera?

Kufotokoza Aefeso 3:20​—“[Mulungu] Amene Angathe Kuchita Zazikulu Kwambiri Kuposa Zonse Zimene Timapempha Kapena Kuganiza”

Kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphero a atumiki ake komanso kukwaniritsa zimene atumiki ake akuyembekezera?

Kufotokoza Afilipi 4:6, 7​—“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse”

Kodi ndi mitundu iti ya pemphero imene ingathandize anthu amene amalambira Mulungu kuti asamade nkhawa kwambiri komanso akhale ndi mtendere wamumtima?

Afilipi 4:8—“Zinthu zilizonse zoona, . . . pitirizani kuganizira zimenezi”

Kodi Akhristu ayenera kukhala ndi chizolowezi choganizira zinthu zotani?

Kufotokoza Afilipi 4:13​—“Ndimatha Kuchita Zonse Kudzera mwa Khristu”

Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani polemba kuti adzapeza mphamvu “pa zinthu zonse”?

Kufotokoza 2 Timoteyo 1:7​​—“Mulungu sanatipatse mzimu wamantha.”

Kodi Mulungu amathandiza bwanji munthu amene akuchita mantha kuti akwanitse kukhala wolimba mtima kuti achite zoyenera?

Aheberi 4:12 Kufotokozera​—“Mawu a Mulungu Ndi Amoyo Komanso Amphamvu”

Kodi mumalola kuti mawu a Mulungu azigwira ntchito pa moyo wanu? Nanga zimenezi zimasonyeza kuti ndinu munthu wotani?

1 Petulo 5:6, 7 Kufotokoza​—“Mudzichepetse Pamaso pa Mulungu Wamphamvu, . . . Tayani pa Iye Nkhawa Zanu Zonse”

Kodi “kutaya” nkhawa zathu kwa Mulungu kumatanthauza chiyani? Nanga kumabweretsa bwanji mtendere?

Chivumbulutso 21:1—“Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano”

Kodi Baibulo limapereka maumboni otani otithandiza kumvetsa bwino tanthauzo la vesili?