Kalata Yoyamba ya Yohane 2:1-29

  • Yesu, nsembe yophimba machimo (1, 2)

  • Kusunga malamulo ake (3-11)

    • Lamulo lakale komanso latsopano (7, 8)

  • Chifukwa cholembera kalatayi (12-14)

  • Musamakonde dziko (15-17)

  • Tichenjere ndi wokana Khristu (18-29)

2  Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo. Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza wolungama,+ Yesu Khristu,+ amene ali ndi Atate.  Iye anakhala nsembe yophimba+ machimo athu.*+ Osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.+  Tingasonyeze kuti tikumudziwa ngati titapitiriza kusunga malamulo ake.  Munthu amene amanena kuti, “Ine ndikumudziwa,” koma nʼkumalephera kusunga malamulo ake ndi wabodza ndipo alibe choonadi mumtima mwake.  Koma aliyense wosunga mawu a Khristu, amasonyeza kuti amakondadi Mulungu.+ Chifukwa cha zimenezi, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+  Munthu amene amanena kuti ndi wogwirizana naye, ayenera kupitiriza kuyenda mmene iyeyo ankayendera.+  Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano. Koma ndikukulemberani lamulo lakale limene mwakhala nalo kuyambira pachiyambi.+ Lamulo lakaleli ndi mawu amene munawamva.  Komabe, ndikukulemberani lamulo latsopano limene Yesu ankalitsatira, limenenso inuyo mukulitsatira, chifukwa mdima ukupita ndipo kuwala kwenikweni kwayamba kale kuunika.+  Munthu amene amanena kuti ali mʼkuwala koma amadana+ ndi mʼbale wake, ndiye kuti adakali mumdima.+ 10  Amene amakonda mʼbale wake ndiye kuti ali mʼkuwala+ ndipo palibe chimene chingachititse kuti apunthwe. 11  Koma amene amadana ndi mʼbale wake ali mumdima ndipo akuyenda mumdimawo+ komanso sakudziwa kumene akupita+ popeza maso ake sakuona chifukwa cha mdimawo. 12  Ndikulembera inu ana anga okondedwa, popeza machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina lake.+ 13  Ndikulembera inu abambo, chifukwa mukumudziwa amene wakhala alipo kuyambira pachiyambi. Ndikulemberanso inu anyamata chifukwa mwagonjetsa woipayo.+ Ndikulembera inu ana okondedwa chifukwa mukuwadziwa Atate.+ 14  Ndikulembera inu abambo chifukwa mukumudziwa iye amene wakhalapo kuyambira pachiyambi. Ndikulembera inu anyamata chifukwa ndinu olimba+ ndipo mumakhulupirira mawu a Mulungu+ komanso mwagonjetsa woipayo.+ 15  Musamakonde dziko kapena zinthu zamʼdziko.+ Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.+ 16  Chifukwa chilichonse chamʼdzikoli, monga zimene thupi limalakalaka,+ zimene maso amalakalaka+ komanso kudzionetsera ndi zinthu zimene munthu ali nazo pa moyo wake,* sizichokera kwa Atate koma mʼdzikoli. 17  Kuwonjezera pamenepa, dzikoli likupita ndiponso chilichonse cha mʼdzikoli chimene anthu amalakalaka chikupita.+ Koma wochita zimene Mulungu amafuna adzakhala mpaka kalekale.+ 18  Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto. Munamva kuti wokana Khristu akubwera,+ ndipo panopa okana Khristu ambiri aonekera.+ Chifukwa cha zimenezi tikudziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto. 19  Amenewo anachoka pakati pathu, koma sanali mʼgulu lathu,*+ chifukwa akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe ndi ife. Koma anachoka kuti zidziwike kuti si onse amene ali mʼgulu lathu.+ 20  Inu munadzozedwa ndi mzimu wa Mulungu amene ndi woyera,+ ndipo nonsenu mukudziwa choonadi. 21  Ndakulemberani zimenezi, osati chifukwa chakuti simukudziwa choonadi+ koma chifukwa chakuti mukuchidziwa ndiponso chifukwa chakuti palibe bodza lililonse limene limachokera mʼchoonadi.+ 22  Kodi wabodza angakhalenso ndani kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?+ Ameneyu ndi wokana Khristu,+ yemwe amakana Atate komanso Mwana. 23  Aliyense amene amakana Mwana sangakhale pa ubwenzi ndi Atate.+ Koma amene amavomereza Mwana+ amakhalanso pa ubwenzi ndi Atate.+ 24  Koma inu, zimene munamva pachiyambi zikhalebe mumtima mwanu.+ Zimene munamvazo zikakhalabe mumtima mwanu, mudzapitirizanso kukhala ogwirizana ndi Mwana komanso Atate. 25  Ndipotu paja iye anatilonjeza moyo wosatha.+ 26  Ndakulemberani zinthu zimenezi zokhudza anthu amene akufuna kukusocheretsani. 27  Koma inuyo, Mulungu anakudzozani ndi mzimu wake+ ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu, moti simukufunikira wina aliyense woti azikuphunzitsani. Koma kudzozedwako kukukuphunzitsani zinthu zonse+ ndipo ndi koona osati konama. Monga mmene kudzozedwako kwakuphunzitsirani, pitirizani kukhala ogwirizana naye.+ 28  Tsopano inu ana anga okondedwa, khalanibe ogwirizana naye kuti akadzaonekera, tidzakhale ndi ufulu wa kulankhula.+ Komanso kuti tisadzachoke pamaso pake mwamanyazi pa nthawi ya kukhalapo* kwake. 29  Ngati mukudziwa kuti iye ndi wolungama, ndiye kuti mukudziwanso kuti aliyense wochita zinthu zabwino anabadwa kuchokera kwa Mulungu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anakhala njira yosangalatsira Mulungu.”
Kapena kuti, “komanso kulankhula modzitama zokhudza zinthu zimene munthu ali nazo.”
Kapena kuti, “sanali athu.”