Wolembedwa ndi Luka 4:1-44

  • Mdyerekezi anayesa Yesu (1-13)

  • Yesu anayamba kulalikira ku Galileya (14, 15)

  • Yesu anakanidwa ku Nazareti (16-30)

  • Zimene zinachitika musunagoge ku Kaperenao (31-37)

  • Apongozi a Simoni ndi anthu ena anachiritsidwa (38-41)

  • Gulu la anthu linapeza Yesu ali kwayekha (42-44)

4  Kenako Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo mzimuwo unamutenga nʼkumuyendetsa malo osiyanasiyana mʼchipululu+  kwa masiku 40, kumene ankayesedwa ndi Mdyerekezi.+ Pa masiku amenewo sanadye chilichonse ndipo masikuwo atatha, anamva njala.  Mdyerekezi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.”  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.’”+  Choncho anapita naye pamalo okwera ndipo anamuonetsa maufumu onse apadziko lapansi mʼkanthawi kochepa.+  Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine+ ndipo ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndingakonde kumupatsa.  Ndiye ngati inuyo mungandilambire kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.”  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+  Kenako anapita naye ku Yerusalemu ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi* nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi kuchokera pano.+ 10  Paja Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu, kuti akutetezeni,’ 11  ndipo ‘Adzakunyamulani mʼmanja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala.’”+ 12  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wanu musamamuyese.’”+ 13  Choncho Mdyerekeziyo atamaliza mayesero onsewo, anamusiya mpaka nthawi ina yabwino.+ 14  Tsopano Yesu anabwerera ku Galileya+ atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu. Ndipo mbiri yake yabwino inamveka paliponse mʼmadera onse ozungulira. 15  Komanso anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo anthu onse ankamulemekeza. 16  Kenako anapita ku Nazareti+ kumene anakulira. Mogwirizana ndi chizolowezi chake pa tsiku la Sabata, analowa mʼsunagoge+ nʼkuimirira kuti awerenge Malemba. 17  Ndiyeno anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya. Iye anatambasula mpukutuwo nʼkupeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18  “Mzimu wa Yehova* uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu osauka. Anandituma kudzalengeza za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina komanso zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale pa ufulu,+ 19  ndi kudzalalikira za chaka chovomerezeka kwa Yehova.”*+ 20  Atatero anapinda mpukutuwo nʼkuubwezera kwa wotumikira mmenemo ndipo anakhala pansi. Maso a anthu onse amene anali mʼsunagogemo anali pa iye nʼkumamuyangʼanitsitsa. 21  Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”+ 22  Zitatero onse anayamba kumutamanda komanso anadabwa ndi mawu ogwira mtima amene anatuluka pakamwa pake,+ moti ankanena kuti: “Kodi si mwana wa Yosefe ameneyu?”+ 23  Atamva zimenezi iye anawauza kuti: “Mosakayikira mudzagwiritsa ntchito pa ine mawu akuti, ‘Wochiritsa iwe, dzichiritse wekha. Zinthu zambiri zimene tinamva kuti unachita ku Kaperenao,+ uzichitenso kwanu kuno.’” 24  Iye ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneri amene amalandiridwa kwawo.+ 25  Mwachitsanzo, ndithu ndikukuuzani kuti: Munali akazi ambiri amasiye mu Isiraeli mʼmasiku a Eliya, pamene kumwamba kunatsekedwa kwa zaka zitatu ndi miyezi 6 ndipo mʼdziko lonse munali njala yaikulu.+ 26  Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akazi amenewo. Mʼmalomwake anatumizidwa kwa mkazi wamasiye ku Zarefati mʼdziko la Sidoni.+ 27  Ndiponso munali akhate ambiri mu Isiraeli mʼnthawi ya mneneri Elisa. Komabe palibe aliyense wa iwo amene anayeretsedwa,* koma Namani wa ku Siriya.”+ 28  Tsopano anthu onse amene ankamvetsera zinthu zimenezi mʼsunagogemo anakwiya kwambiri.+ 29  Iwo ananyamuka ndipo mwamsangamsanga anamutulutsira kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phiri pamene panali mzinda wawo, kuti akamuponye kuphedi. 30  Koma iye anangodutsa pakati pawo nʼkumapita.+ 31  Kenako anapita ku Kaperenao, mzinda wa ku Galileya. Ndipo ankawaphunzitsa pa tsiku la Sabata.+ 32  Kumeneko anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa ankalankhula mosonyeza kuti ali ndi ulamuliro. 33  Ndiyeno mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu, chiwanda chonyansa, ndipo anafuula mwamphamvu kuti:+ 34  “Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu!”+ 35  Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye.” Choncho chiwandacho chinagwetsa munthuyo pansi pakati pawo, kenako chinatuluka mwa iye osamuvulaza. 36  Ataona zimenezi anthu onse anadabwa kwambiri ndipo anayamba kukambirana kuti: “Taonani, mawu ake ndi amphamvu kwambiri! Chifukwa akutha kudzudzula mizimu yonyansa mwa ulamuliro ndi mphamvu ndipo mizimuyo ikutulukadi.” 37  Choncho mbiri yake inapitiriza kufalikira paliponse mʼmidzi yonse yozungulira. 38  Atatuluka mʼsunagogemo, anakalowa mʼnyumba ya Simoni. Pa nthawiyo apongozi aakazi a Simoni ankadwala malungo aakulu,* choncho anamupempha kuti awathandize.+ 39  Ndiyeno anaima pamene mayiwo anagona nʼkuwachiritsa ndipo malungowo anatheratu. Nthawi yomweyo mayiwo anadzuka nʼkuyamba kuwatumikira. 40  Koma pamene dzuwa linkalowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa poika manja ake pa iwo.+ 41  Ziwanda nazonso zinatuluka mwa anthu ambiri zikufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”+ Koma iye anadzudzula ziwandazo ndipo sanazilole kuti zilankhule+ chifukwa zinkamudziwa kuti ndi Khristu.+ 42  Kutacha, anachoka nʼkupita kumalo kopanda anthu.+ Koma gulu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anamupempha kuti asachoke. 43  Koma iye anawauza kuti: “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.”+ 44  Choncho anapita kukalalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malo okwera kwambiri a kachisi.”
Kapena kuti, “amene anachiritsidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kutentha thupi.”