Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Msonkhano Watsopano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Msonkhano Watsopano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

PAMSONKHANO wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, womwe unachitika pa 3 October, 2015, M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira analengeza za kusintha kwa misonkhano yathu. M’baleyu ananena kuti Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, Msonkhano wa Utumiki komanso Phunziro la Baibulo la Mpingo zalowedwa m’malo ndi msonkhano watsopano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. M’bale Morris ananenanso kuti Utumiki Wathu wa Ufumu ulowedwa m’malo ndi Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu yomwe izikhala ya masamba 8. Izikhala ndi ndandanda ya misonkhano komanso zithunzi zothandiza pophunzira Baibulo.

Msonkhano watsopanowu uli ndi mbali zitatu:

  1. Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu. Mbali imeneyi imayamba ndi nkhani ya 10 minitsi. M’bale amene amakamba nkhaniyi amafotokoza mfundo zochokera pa kuwerenga Baibulo kwa mlunguwo komanso zithunzi m’ndandandayo. Kenako, pamakhala kachigawo ka 8 minitsi komwe kamakhala ndi mutu wakuti, “Kufufuza Mfundo Zothandiza.” Kachigawoka kamakhala ka mafunso ndi mayankho ndipo anthu amafotokoza mfundo zomwe apeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlunguwo. Chigawo chimenechi chikatha pamabwera m’bale yemwe amawerenga Baibulo kwa 4 minitsi.

  2. Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki. Mbaliyi imakhala ndi zigawo zitatu. Abale ndi alongo amachita zitsanzo zosonyeza ulendo woyamba, ulendo wobwereza ndiponso phunziro la Baibulo.

  3. Moyo Wathu Wachikhristu. Mbali imeneyi imakhala ndi nkhani zomwe zingatithandize kuti tizitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. Chigawo chofunika kwambiri cha mbali imeneyi ndi Phunziro la Baibulo la Mpingo lomwe limakhala la mafunso ndi mayankho.

Abale ndi alongo padziko lonse akuyamikira kwambiri msonkhano watsopanowu. Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku Australia anati: “Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndi wabwino kwambiri. Nkhani zake ndi zokhudza mtima kwambiri komanso zitsanzo zake ndi zosavuta. Msonkhanowu ndi wosatopetsa chifukwa umakhala ndi mavidiyo, ana amatengapo mbali komanso nkhani zake zimakhala zazifupi ndiponso zosangalatsa.”

Akulu a mpingo wina wa ku Italy anati: “Msonkhano watsopanowu ukutithandiza kuti tizikonzekera bwino. Zimenezi zachititsa kuti tiziphunzitsa bwino mumpingo. Msonkhanowu ndi umboni wakuti Yehova akuphunzitsa anthu ake m’njira yabwino kwambiri. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 15 ananena kuti: ‘Poyamba zinkandivuta kumvetsera msonkhano wonse chifukwa ndinkatopa. Koma msonkhano watsopanowu ukundithandiza kuti ndizikonzekera bwino komanso ndizimvetsera bwinobwino mpaka kumaliza.’”

Banja lina la ku Austria linati: “Poyamba tinkavutika kwambiri kuwerenga Baibulo ndi mwana wathu wazaka 10 moti zinkakhala zovuta kuyankha pamisonkhano. Koma mbali ya Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu yatithandiza kuti tizipeza mfundo zoti tikayankhe. Panopa tonse timasangalala kuwerenga Baibulo mlungu uliwonse. Tikuonanso kuti msonkhanowu wathandiza kuti mwana wathu azikonda kwambiri Yehova.”

A Ines a ku Germany ananena kuti: “Msonkhano umenewu wandithandiza kuti ndizikonzekera komanso kuganizira kwambiri zimene ndikuphunzira. Poyamba ndikamaphunzira sindinkafufuza kwambiri. Ndikuona kuti panopa ndili pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Dziko la Satanali limachitsa kuti ndikhale wosasangalala komanso wotopa, koma misonkhanoyi imandipatsa mphamvu.”

Mipingo ya ku Solomon Islands ikusangalala kwambiri ndi msonkhano watsopanowu ndipo abale akuyesetsa kuti azipindula mokwanira. Mipingo yambiri ili m’madera akumidzi komwe kulibe magetsi ndiponso intaneti. Abale ambiri a m’mipingoyi alibe zinthu zambiri ndipo amangodalira ulimi. Ndiye kodi amapeza bwanji mavidiyo oti aonere pamisonkhano? Abale ndi alongo a mpingo wina wapachilumba cha Malaita anagwirizana zoti azigulitsa kokonati. Atapeza ndalama anagula chipangizo choonetsera mavidiyo choti akhoza kuchitchaja ndi mphamvu ya dzuwa. Kuti apeze mavidiyo a mwezi uliwonse, abale amapita kumadera ena komwe kuli intaneti ndipo amapanga dawunilodi mavidiyowo.

M’bale wina wa ku United States anati: “Kwa zaka zoposa 40 zapitazi ndakhala ndikuvutika kuwerenga komanso kukonzekera misonkhano. Ndinkafunika kuwerenga nkhani kangapo kuti ndiimvetse moti n’kufotokozera ena. Chifukwa cha vuto langali ndimaphunzira mosavuta ndikamaonera vidiyo kapena ndikamaona zithunzi. Choncho, ndikufuna kuthokoza abale a m’Bungwe Lolamulira chifukwa cha mavidiyo omwe akumaonetsedwa pamsonkhano watsopanowu komanso zithunzi zomwe zikumapezeka mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Mavidiyo ofotokoza mfundo zachidule za m’mabuku a m’Baibulo ndi othandizanso kwambiri. Zikuchita kuonekeratu kuti Yehova akudalitsa khama lanu poyesetsa kuthandiza anthu ake. Zikomo kwambiri.”

Malawi