Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Kuyamba Kuchita Zinthu Mwamtendere

N’zotheka Kuyamba Kuchita Zinthu Mwamtendere

N’zotheka Kuyamba Kuchita Zinthu Mwamtendere

NGAKHALE kuti anthufe mwachibadwa timaganiza zolakwika, koma munthu amachita kuphunzira khalidwe lachiwawa. Ndi mmenenso zilili ndi munthu amene amachita zinthu mwamtendere. Koma kodi ndani amene angatiphunzitse kuchita zinthu mwamtendere? Ndi Mlengi wathu amene ali ndi nzeru zopanda malire. Onani mfundo zotsatirazi komanso malangizo opezeka m’Baibulo:

1 “Usasirire munthu wachiwawa.” (Miyambo 3:31) Dziwani kuti munthu wanzeru ndi amene ali ndi makhalidwe ngati kudziletsa komanso kufatsa. Lemba la Miyambo 16:32 limati: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.” Munthu wosakwiya msanga amakhala ngati denga lolimba lomwe silingasasuke ngakhale litaombedwa ndi mphepo yamphamvu. Amati munthu wina akamuputa, amayankha modekha zomwe “zimabweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Koma munthu wosachedwa kupsa mtima amakwiya ngakhale pa zinthu zazing’ono.—Miyambo 25:28.

2 Muzisankha bwino anthu ocheza nawo. Lemba la Miyambo 16:29 limati: “Munthu wachiwawa amakopa mnzake.” Koma Baibulo limatiuzanso kuti: “Woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” (Miyambo 13:20) Choncho, tikamacheza ndi anthu okonda mtendere omwe ndi ofatsa komanso odziletsa, ifenso tikhoza kutengera makhalidwe amenewo.

3 Muzikonda anthu kuchokera pansi pamtima. Lemba la 1 Akorinto 13:4-7 limafotokoza bwino zimene chikondi chimachita. Limanena kuti: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima, . . . sichikwiya. Sichisunga zifukwa. . . . Chimakwirira zinthu zonse, . . . chimapirira zinthu zonse.” Yesu ananena kuti, munthu amene amatsanzira chikondi cha Mulungu amakondanso ngakhale adani ake.—Mateyu 5:44, 45.

4 Muzikhulupirira kuti Mulungu adzathana ndi anthu oipa. Baibulo limati: “Musabwezere choipa pa choipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Okondedwa, musabwezere choipa. . . . Pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.’” (Aroma 12:17-19) Tikamakhulupirira Mulungu komanso zimene amalonjeza, timakhala ndi mtendere wamumtima womwe anthu opanda chikhulupiriro sangaumvetse.—Salimo 7:14-16; Afilipi 4:6, 7.

5 Muziyembekezera kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzabweretse mtendere weniweni. Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba limene posachedwapa lidzawonongeratu anthu oipa onse n’kuyamba kulamulira dziko lonse lapansi. (Salimo 37:8-11; Danieli 2:44) Mu ufumu umenewu, “wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.”—Salimo 72:7.

Mfundo za m’Baibulo zimenezi zathandiza anthu ambiri kuyamba kuchita zinthu mwamtendere. Mmodzi mwa anthu amenewa ndi Salvador Garza.