Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mowa

Mowa

Kodi kumwa mowa n’kulakwa?

‘Vinyo amasangalatsa mtima wa munthu. Nkhope ya munthu imasalala ndi mafuta, komanso chakudya chimakhutiritsa mtima wa munthu.’Salimo 104:15.

ZIMENE ANTHU AMANENA

M’mayiko ambiri, anthu amaona kuti kumwa mowa si vuto ndipo amamwa mowa ngakhale pa nthawi ya chakudya. Koma m’mayiko ena amaletsa kumwa mowa. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amasiyana maganizo pa nkhani imeneyi? Anthu amaona zinthu mosiyana chifukwa cha kusiyana chikhalidwe, thanzi, chipembedzo komanso zinthu zimene zimawadetsa nkhawa.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo silimaletsa kumwa mowa koma limaletsa kuledzera komanso kumwa kwambiri mowa. (1 Akorinto 6:9, 10) Kuyambira kale kwambiri atumiki a Mulungu, amuna ndi akazi omwe, ankamwa vinyo yemwe amatchulidwa nthawi zoposa 200 m’Baibulo. (Genesis 27:25) Lemba la Mlaliki 9:7 limati: “Ukadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala.” Chifukwa chakuti vinyo amapangitsa kuti munthu azisangalala, nthawi zambiri ankamwedwa pakakhala zochitika zapadera, mwachitsanzo ukwati. Pa ukwati wina, Yesu Khristu anachita chozizwitsa chake choyamba pamene anasandutsa madzi kukhala “vinyo wabwino.” (Yohane 2:1-11) Nthawi zina, vinyo ankagwiritsidwanso ntchito ngati mankhwala.—Luka 10:34; 1 Timoteyo 5:23.

 Kodi Baibulo limanena kuti tizimwa vinyo kapena mowa wochuluka bwanji?

[Musakhale] akapolo a vinyo wambiri.”Tito 2:3.

DZIWANI IZI

Chaka chilichonse mabanja ambiri amakumana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa chakuti kholo limodzi kapena onse amamwa mowa kwambiri. Ngozi zambiri, makamaka za pamsewu zimachitika chifukwa chakumwa mowa kwambiri. Ndipo ngati munthu ali ndi chizolowezi chomwa mowa kwambiri, n’kupita kwa nthawi mowawo umatha kumuwononga ubongo, mtima, chiwindi komanso m’mimba.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu amafuna kuti tizidziletsa pa nkhani ya zakudya komanso zakumwa. (Miyambo 23:20; 1 Timoteyo 3:2, 3, 8) Mulungu sasangalala ndi munthu amene amadya komanso kumwa kwambiri. Baibulo limati: “Vinyo ndi wonyoza. Chakumwa choledzeretsa chimasokosera ndipo aliyense wosochera nacho alibe nzeru.”—Miyambo 20:1.

Njira imodzi imene mowa ungasocheretsere munthu ndi yakuti amayamba mosavuta kuchita makhalidwe oipa. Lemba la Hoseya 4:11, limati: “Vinyo wakale ndi vinyo wotsekemera zimawononga nzeru za munthu.” Munthu wina dzina lake John, anamvetsa tanthauzo la lemba limeneli nkhwangwa ili m’mutu. * Atakangana ndi mkazi wake, John anapita ku hotelo kumene anakaledzera koopsa kenako n’kuchita chigololo. Zimenezi zitachitika John anakhumudwa komanso kudziimba mlandu ndipo analonjeza kuti sadzachitanso. Ngati munthu amamwa mowa kwambiri akhoza kuwononga thanzi lake, kuchita makhalidwe oipa komanso kusokoneza ubwenzi wake ndi Mulungu. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti anthu amene amamwa mowa kwambiri sadzapeza moyo wosatha.—1 Akorinto 6:9, 10.

Kodi ndi nthawi iti imene munthu sayenera kumwa mowa?

“Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”Miyambo 22:3.

DZIWANI IZI

Buku lina linanena kuti “mowa uli ngati mankhwala osokoneza bongo” (World Book Encyclopedia). Choncho, nthawi zina munthu sayenera kumwa mowa ngakhale pang’ono.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nthawi zambiri anthu amakumana ndi mavuto ena chifukwa chomwa mowa pa nthawi yolakwika. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.” Choncho, pali nthawi yoti munthu sayenera kumwa mowa. (Mlaliki 3:1) Mwachitsanzo, m’mayiko ena munthu akakhala kuti sanakwanitse zaka zinazake saloledwa kumwa mowa. Nthawi zinanso, munthu amene wakhala akumwa mowa kwambiri ndipo akuyesetsa kuti asiye, sayenera kumwa mowa olo pang’ono. Ndipo nthawi zina munthu sayenera kumwa mowa ngati akumwa mankhwala omwe sagwirizana ndi mowa. Anthu ambiri amaonanso kuti ndi bwino kuti asamwe mowa akakhala kuti akufuna kupita kuntchito kapena akakhala kuntchitoko. Zimenezi zimathandiza kwambiri ngati amagwiritsira ntchito makina oti akhoza kuwavulaza. Anthu anzeru amayesetsa kusamalira thanzi lawo chifukwa amaona kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Salimo 36:9) Choncho, tikamatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani ya mowa, timasonyeza kuti timalemekeza mphatso ya moyo.

^ ndime 11 Dzina lasinthidwa.