Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | CÉLINE GRANOLLERAS

Katswiri wa Impso Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Katswiri wa Impso Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Céline Granolleras ndi dokotala wa ku France wa matenda a impso. Atagwira ntchito ya udokotala kwa zaka 20, Céline anazindikira kuti kuli Mlengi amene amatikonda. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake komanso za ntchito yake.

Tiuzeni mmene munakulira.

Banja lathu linasamuka kuchoka ku Spain kupita ku France ndili ndi zaka 9. Makolo anga anali a Katolika koma ineyo ndinasiya kukhulupirira kuti kuli Mulungu ndili ndi zaka 16. Ndinkaona kuti chipembedzo chilibe phindu lililonse pamoyo wa munthu. Munthu akandifunsa kuti ndiye moyo unayamba bwanji ngati kulibe Mulungu, ndinkayankha kuti: “Panopa asayansi sanapezebe yankho, koma ndikukhulupirira kuti adzalipeza.”

N’chifukwa chiyani munayamba kuphunzira za matenda a impso?

Ndinkaphunzira pasukulu yophunzitsa zachipatala ya Montpellier ku France. Pulofesa wina anandiuza kuti ndizikagwira nawo ntchito ku dipatimenti ina yoona za mankhwala a matenda a impso. Ntchitoyi inkaphatikizapo kufufuza zinthu zina komanso kusamalira odwala. Ntchito imeneyi ndi imene ndinkaifuna kuyambira kalekale. Mu 1990, ndinapanga nawo kafukufuku wa mankhwala ena ake (EPO) omwe amathandiza kuti mafupa azipanga maselo a magazi. Mankhwalawa amatha kupangidwa ndi asayansi komanso impso zathu zimatulutsa timadzi tofanana ndi mankhwala amenewa. Pa nthawi imeneyi anthu anali atangoyamba kumene kuchita kafukufuku wamtundu umenewu.

N’chiyani chinakuchititsani kuyamba kuganizira za Mulungu?

Mu 1979, mwamuna wanga, Floréal, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Koma ine sindinkachita nazo chidwi chifukwa zachipembedzo zinali zitanditopetsa ndili mwana. Komabe, mwamuna wanga komanso ana anga anakhala a Mboni ndipo pafupifupi anzathu onse analinso a Mboni. Mmodzi mwa anzangawa, dzina lake  Patricia, anandiuza kuti ndiziyesa kupemphera. Iye anandiuza kuti: “Ngati kumwamba kuli Mulungu, uona wekha zimene zitachitike ukapemphera. Koma ngati kulibe Mulungu, palibe chimene chitachitike.” Patadutsa zaka zingapo, ndinayamba kuganizira cholinga cha moyo ndipo ndinakumbukira mawu amene Patricia anandiuza. Kenako ndinayamba kupemphera kuti ndidziwe cholinga cha moyo.

N’chiyani chinakupangitsani kuti muziganizira cholinga cha moyo?

Zigawenga zitaphulitsa nyumba ziwiri zazitali ku America za World Trade Center, ndinayamba kuganizira kwambiri chifukwa chake anthu ambiri amachita zoipa. Ndinayamba kuganiza kuti: ‘Zimene anthu okonda kwambiri chipembedzo chawo akuchita zikhoza kutibweretsera mavuto aakulu. Koma a Mboni za Yehova ndi anthu amtendere komanso sachita zinthu monyanyira. Amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limanena. Mwina ndiyese kuphunzira Baibulo kuti ndidziwe zimene limaphunzitsa.’ Kenako, ndinayamba kuwerenga Baibulo pandekha.

Popeza ndinu dokotala, kodi sizinakuvuteni kukhulupirira kuti kuli Mulungu?

Ayi. Ndinkagoma kwambiri ndi mmene thupi lathu linapangidwira. Mwachitsanzo, n’zochititsa chidwi kwambiri kuona mmene impso zimathandizira kuti munthu azikhala ndi maselo ofiira okwanira m’magazi.

N’chifukwa chiyani mukutero?

Ndinazindikira kuti Mulungu ndi amene analenga thupi lodabwitsa chonchi

Maselo ofiira a m’magazi ndi amene amanyamula mpweya umene timapuma. Munthu akataya magazi ambiri ndiye kuti mpweya umachepanso m’thupi mwake. Ndiye chimene chimachitika n’chakuti, mpweya ukachepa m’thupi, impso zathu zimatulutsa timadzi tina tomwe timathandiza kuti thupi lathu lipange maselo ofiira ambiri. Maselo ofiira akachuluka ndiye kuti m’thupinso mukhala mpweya wokwanira. Zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri. Koma chodabwitsa n’chakuti, zinanditengera zaka 10 chiphunzirireni zimenezi ndisanazindikire kuti Mulungu ndi amene analenga thupi lodabwitsa chonchi.

Ndiye chinachitika n’chiyani mutayamba kuwerenga Baibulo?

Ndinali nditawerengapo kale mabuku ambiri ofotokoza za mbiri yakale komanso mabuku ena otchuka. Koma nditangoyamba kuwerenga Baibulo ndinaona kuti linali losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse. Malangizo ake anali othandiza kwambiri moti ndinkachita kuoneratu kuti silinalembedwe ndi munthu. Ndinachitanso chidwi kwambiri ndi Yesu. Ndinaphunzira kuti analidi munthu weniweni, anali ndi anzake ocheza nawo komanso ankamva mmene anthufe timamvera. Chifukwa chakuti sindinkafuna kugwiritsa ntchito mabuku a Mboni, ndinkati ndikakhala ndi funso ndinkafufuza m’mabuku ena.

Munkafufuza zinthu ngati ziti?

Ndinayamba kufufuza m’mabuku ofotokoza za mbiri yakale . . . Pamapeto pake ndinazindikira kuti zimene Baibulo linalosera zinachitikadi ndendende

Mwachitsanzo, ndinafufuza za ulosi wa m’Baibulo wonena za chaka chimene Yesu ankayenera kubatizidwa. Ulosiwo unafotokoza kutalika kwa nthawi imene idzadutse kuchokera m’chaka cha 20 cha ulamuliro wa Aritasasita, mfumu ya Perisiya, kufikira pamene Yesu amayenera kudzaonekera monga Mesiya. * Ndimakonda kufufuza zinthu chifukwa ndi mbali ya ntchito yanga. Ndinayamba kufufuza m’mabuku ofotokoza za mbiri yakale kuti ndione nthawi imene Aritasasita analamulira komanso nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake padziko lapansi. Pamapeto pake ndinazindikira kuti zimene Baibulo linalosera zinachitikadi ndendende ndipo zimenezi zinanditsimikizira kuti linachokeradi kwa Mulungu.

^ ndime 19 Onani tsamba 197 mpaka 199 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.