Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Achule Amene Amaswa Modabwitsa Kwambiri

Achule Amene Amaswa Modabwitsa Kwambiri

PALI mtundu winawake wa achule amene ankapezeka ku Australia ndipo amaswa modabwitsa kwambiri. Anthu ena amanena kuti kuchokera m’chaka cha 2002, achule amenewa sapezekanso. Chule wamkazi amameza mazira amene akumana kale ndi umuna ndipo amaswa ana m’mimba mwake. Anawo amakhala m’mimbamo kwa milungu 6 ndipo kenako amatuluka kudzera pakamwa.

Pofuna kuti mazira komanso tiana tisagayike limodzi ndi chakudya, chuleyu amasiya kudya komanso satulutsa asidi amene amathandiza kugaya zakudya. Mazirawo ndiponso tiana timatulutsa timadzi timene timathandiza kuti chuleyo asamatulutse asidi wothandiza kugaya zakudya.

Achule a mtundu umenewu amatha kuswa ana 24. Pofika nthawi yoti anawa atuluke, chuleyu amakhala akulemera kwambiri kuposa mmene analili poyamba. Kuti timvetse mmene kulemera kwake kumawonjezekera, tingayerekezere ndi mayi amene asanatenge pakati ankalemera makilogalamu 68 ndipo pofika nthawi yobereka akulemera makilogalamu 111. Chuleyu amalemedwa ndi anawa moti mimba yake imatamuka kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti popuma azigwiritsa ntchito timabowo ta pakhungu chifukwa mapapo ake amakhala atafinyika kwambiri.

Ikafika nthawi yoti ana ayambe kutuluka, pamatenga masiku angapo kuti ana onse atuluke. Koma chuleyu akaona kuti pali mavuto ena, amatha kutulutsa anawo mofulumira powasanza. Akatswiri ena ofufuza zinthu nthawi ina anaona chule akusanza ana 6 nthawi imodzi ndipo anawo anagwera patali, pafupifupi mita imodzi.

Anthu ena amanena kuti mtundu umenewu wa achule unachita kusintha kuchokera ku achule a mtundu wina. Zimenezi zikanakhala zoona, ndiye kuti achulewa akanafunika kusintha kwambiri mmene amaonekera komanso mmene thupi lawo limagwirira ntchito kuti azitha kuswa modabwitsa chonchi. Komatu katswiri wina wasayansi, yemwenso amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, dzina lake Michael J. Tyler ananena kuti: “Tikaganizira mmene achulewa amaswera modabwitsa, zimachita kuonekeratu kuti n’zosatheka kuti anachita kusintha kuchokera ku mtundu wina wa achule. Zingakhale zomveka kunena kuti pali winawake amene anachititsa kuti pakhale mtundu wa achule amenewa.” Anthu ena amaona kuti amene anachititsa zimenezi ndi Mlengi. *

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti achulewa aziswa ana modabwitsa chonchi, kapena palidi winawake amene anawalenga?

^ ndime 7 Charles Darwin analemba m’buku lake lina kuti: “Kuti mtundu wa nyama usinthe n’kukhala mtundu wina, zimachitika pang’onopang’ono komanso umangosintha pang’ono. Sizingatheke kuti mtundu winawake wa nyama ungosintha kamodzin’kamodzi n’kukhala mtundu wina.”