Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Chimene Chimachititsa Kuti Dzombe Lisamawombane Pouluka

Chimene Chimachititsa Kuti Dzombe Lisamawombane Pouluka

DZOMBE limauluka m’magulu ndipo nthawi zina limauluka lokwana 80 miliyoni pa gulu limodzi. Komatu dzombeli siliwombana. Kodi chinsinsi chake chagona pati?

Taganizirani izi: Pakati pa maso a dzombeli pamakhala maselo amene amatumiza uthenga ku ubongo. Dzombe likatsala pang’ono kuwombana ndi linzake, maselowa amatumiza uthenga kumapiko ndi miyendo ndipo izi zimapangitsa kuti dzombelo lichite zinthu mwachangu kuti lisawombane ndi linalo. Uthengawu umayenda mofulumira kwambiri moti inuyo mukaphethira kamodzi, maselowa amakhala atatumiza mauthenga ka 5.

Potengera maso komanso maselo a dzombeli, asayansi apanga loboti imene imatha kuzindikira chinthu chimene chili pafupi pake n’kuchizemba kuti zisawombane. Asayansiwa apanga lobotili pogwiritsa ntchito pulogalamu inayake yapakompyuta. Pofuna kuchepetsa kuwombana kwa magalimoto, akatswiri a sayansi akugwiritsa ntchito luso limeneli n’kumapanga magalimoto okhala ndi loboti yothandiza kuti galimotoyo izizindikira mwachangu kuti yatsala pang’ono kuwombana ndi inzake. Pulofesa wina, wa pa yunivesite ya Lincoln ku United Kingdom, dzina lake Shigang Yue ananena kuti: “Pali zambiri zimene tingaphunzire kuchokera ku tizilombo ting’onoting’ono monga dzombe.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti dzombe likhale ndi maselo omwe amatumiza uthenga mofulumira chonchi, kapena pali winawake amene anawapanga?