Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mukufuna Kubwereranso Kunyumba?

Kodi Mukufuna Kubwereranso Kunyumba?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Pali mawu omwe amati “kwanu n’kwanu m’thengo mudalaka njoka.” Izi n’zoona chifukwa achinyamata ambiri omwe amachoka pakhomo pa makolo awo kuti akadziimire paokha, amabwereranso zinthu zikathina. Kodi inunso mukukumana ndi mavuto moti mukufuna kubwerera kwanu?

Achinyamata ambiri amalephera kubwereranso pakhomo pa makolo awo zinthu zikavuta. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Sarah * ananena kuti: “Nditayamba kukhala ndekha ndinkadziona kuti ndine munthu wamkulu chifukwa sindinkadaliranso aliyense. Koma nditabwereranso kunyumba ndinayamba kudzionanso ngati kamwana.” Mnyamata wina dzina lake Richard ananenanso zofanana ndi zimenezi. Ananena kuti: “Sindinkafuna kubwereranso kunyumba. Ndinkaona kuti ndikabwereranso ndioneka ngati wolephera.”

Kodi nanunso mukukumana ndi zimenezi? Nkhaniyi ikhoza kukuthandizani kuti zinthu ziyambenso kukuyenderani.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Mavuto a zachuma. Achinyamata ambiri amene achoka pakhomo pa makolo awo amakhumudwa akaona kuti zikuwavuta kukhala paokha. Richard amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Zinkangokhala ngati ndikulandirira ndalama m’matumba obooka.” Mtsikana wina dzina lake Shaina, yemwe anachoka pakhomo pa makolo ake ali ndi zaka 24 n’kubwereranso patangotha chaka ndi hafu, ananena kuti: “Zinkandivuta kugwiritsa ntchito bwino ndalama. Pamene ndinkachoka kwathu n’kuti ndilibe ndalama, ndipo pamene ndinkabwerera n’kuti ndili ndi ngongole zambiri.” *

Kusowa kwa ntchito. Ntchito ikatha, chilichonse chimasokonekera ngakhale zitakhala kuti munthu anakonzekera bwino kuti adziimire payekha. Shaina anati: “Nditamaliza maphunziro anga a zachipatala ndinalowa bungwe linalake lomwe linandithandiza kupeza ntchito kudera lakumudzi. Koma kenako ntchitoyi inandithera ndipo zinthu zinasokonekera kwambiri chifukwa sindikanathanso kupeza ntchito ina yogwirizana ndi maphunziro anga.”

Zimene umayembekezera zikalephereka. Achinyamata ena akangoyamba kugwira ntchito amaganiza zokakhala paokha asanakonzekere bwinobwino. Amaganiza kuti azidzagwira ntchito yabwino koma amadabwa akazindikira kuti zimene amayembekezera sizinachitike. Ndiyeno amazindikira mochedwa kuti kudziimira paokha si nkhani yamasewera.

ZIMENE MUNGACHITE

Auzeni makolo anu kuti mukufuna kubwerera. Zinthu zina zimene mukufunika kukambirana ndi makolo anu ndi monga zoti mudzakhala pakhomopo kwa nthawi yaitali bwanji, ndalama zomwe muzidzapereka pogulira zinthu zofunika zapakhomo, ntchito zina zomwe muzigwira pakhomo komanso zimene muchite kuti muzadziimirenso panokha. Ndiye kaya muli ndi zaka zingati, muyenera kukumbukira kuti mukubwereranso pakhomo pa makolo anu ndipo mudzafunika kutsatira malamulo a makolo anuwo.—Lemba lothandiza: Ekisodo 20:12.

Muzigwiritsa ntchito ndalama mwanzeru. Buku lina linanena kuti: “Kuti munthu aliyense zimuyendere pa nkhani za ndalama, zimadalira kuti amagwiritsa ntchito bwanji ndalama zomwe amapeza . . . Chinanso chofunika kwambiri ndi kuyesetsa kuti usamangogula zinthu chifukwa choti waziona.”—Lemba lothandiza: Luka 14:28.

Muzipempha anthu ena kuti akuthandizeni maganizo. Makolo anu komanso anthu ena achikulire akhoza kukuthandizani kudziwa mmene mungamasungire ndalama, kukonza bajeti ndiponso kulipira mabilu. Mtsikana wina, dzina lake Marie, ananena kuti: “Ndinkafunika kuphunzira kuti ndizigwiritsa ntchito bwino ndalama zomwe ndinkapeza. Mnzanga wina anandithandiza kuti ndisamangowononga ndalama pa zinthu zosafunika kwenikweni. Ndinadabwa kwambiri nditaona kuti ndalama zanga zambiri zinkathera pa zinthu zosafunika. Ndinaphunziranso kuti ndisamangogula zinthu mwachisawawa koma ndizilola kuti zina zindidutse.”—Lemba lothandiza: Miyambo 13:10.

Muzikumbukira kuti ntchito iliyonse imakhala yosangalatsa ngati munthu akuigwira mwaluso komanso moikirapo mtima

Yesetsani kuti mupezenso ntchito. M’malo momangokhala, mungachite bwino kumafufuza ntchito ina. Komano mukamachita zimenezi, m’pofunika kusamala chifukwa anthu ena amalimbikitsa anzawo kuti azifufuza ntchito yakumtima kwawo. Maganizo amenewa amachititsa kuti munthu asapeze ntchito. Choncho m’malo mosakasaka ntchito yakumtima kwanu, mungachite bwino kukhala wokonzeka kulembedwa ntchito iliyonse imene ingapezeke. Muzikumbukira kuti ntchito iliyonse imakhala yosangalatsa ngati munthu akuigwira mwaluso komanso moikirapo mtima. Muzikumbukira kuti mukhoza kumasangalalabe ndi ntchito yanu ngakhale itakhala kuti si imene munkafuna.

^ ndime 5 Tasintha mayina m’nkhaniyi.

^ ndime 8 Achinyamata ambiri omwe ali kukoleji ku United States amakumana ndi mavuto ngati amenewa. Mwachitsanzo, lipoti la m’nyuzipepala ina linanena kuti achinyamata ambiri akamamaliza maphunziro awo amakhala ali ndi ngongole ya ndalama pafupifupi madola 33,000.—The Wall Street Journal.