Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Anthu Akusiya Zipembedzo Zawo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Akusiya Zipembedzo Zawo?

Bambo ena a ku Turkey, dzina lawo a Gaffar, ankadabwa ndi zimene ankaphunzira kuchipembedzo chawo zoti Mulungu adzawotcha anthu kumoto. Nawonso akazi awo, dzina lawo a Hediye, anayamba kukayikira chipembedzo chawo ali ndi zaka 9. Mayiwa anati: “Kutchalitchi kwathu ankatiphunzitsa kuti Mulungu analemberatu chilichonse chimene chimachitika pa moyo wa munthu. Ndiye popeza ndinali wamasiye, ndinkaona kuti Mulungu si wachilungamo moti ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndinamulakwira chiyani Mulungu?’ Zimenezi zinkandipweteka kwambiri moti nthawi zambiri ndinkalira usiku wonse. Pamene ndinkakwanitsa zaka 15, ndinkangopita kutchalitchi mwamwambo chabe.”

KODI nanunso munakhumudwa ndi chipembedzo chanu ndipo munasiya kupemphera? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. M’mayiko ambiri chiwerengero cha anthu opemphera chayamba kuchepa moti tsogolo la zipembedzo likukayikitsa. Mwachitsanzo taonani mmene zinthu zasinthira m’mayiko otsatirawa.

Kodi Vuto Lagona Pati?

Anthu ambiri akumaona kuti zipembedzo zawagwiritsa fuwa la moto. Akumati akaganizira zimene anthu opemphera akuchita, akumakhumudwa kwambiri. Mwachitsanzo, anthu opemphera ndi amene akumakhala patsogolo kuchita zachiwawa komanso kupha anzawo. M’malo moti akhale zitsanzo zabwino, akuluakulu a zipembedzo akumachita khalidwe la chiwerewere mopanda manyazi m’pang’ono pomwe. Ndiyeno anthu akaona zimenezi, akumaganiza zongodula phazi. Koma panopa tiyeni tione zifukwa zinanso zimene zikuchititsa kuti anthu asiye kupita ku zipembedzo zawo.

  • Mayiko ambiri akutukuka: Lipoti la bungwe lina linanena kuti, “Munthu akayamba kulemera amaiwala Mulungu.” (Global Index of Religion and Atheism) Zimenezi n’zoona chifukwa m’mayiko ambiri omwe zinthu zikuyenda bwino, anthu ambiri akusiya kupemphera. Pulofesa wina wa zachuma, dzina lake John V. C. Nye, anati: “M’mayiko ena anthu ndi olemera kwambiri moti chuma chawo chikumaposa cha mafumu omwe anali olemera kwambiri zaka 200 zapitazo.”

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Baibulo linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza,’ anthu adzakhala okonda ndalama ndiponso okonda zosangalatsa kuposa Mulungu komanso anthu anzawo. (2 Timoteyo 3:1-5) Munthu wina wolemba Baibulo ankadziwa kuti nthawi zina kukhala ndi chuma kumapangitsa munthu kuiwala Mulungu. Choncho anapempha Yehova Mulungu kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma . . . kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani.”—Miyambo 30:8, 9.

  • Anthu sakusangalala ndi makhalidwe komanso miyambo ya zipembedzo zawo: Anthu ambiri, makamaka achinyamata, akumaona kuti kupemphera n’kutaya nthawi. Koma pali anthu enanso omwe ayamba kukayikira zipembedzo zawo. Munthu wina wa ku Scotland, dzina lake Tim Maguire, anati: “Anthu ambiri asiya kupemphera chifukwa akhumudwa ndi zimene zipembedzo zawo zikuchita. Akuona kuti atsogoleri a zipembedzo zawo, omwe amayenera kukhala zitsanzo zabwino, ndi amenenso ali atambwali otheratu.”

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti m’masiku otsiriza kudzabwera aneneri onyenga. Koma kodi aneneri onyengawa akanawadziwa bwanji? Anawauza kuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.” (Mateyu 7:15-18) “Zipatso zopanda pake” zimenezi ndi monga kulowerera ndale komanso kulimbikitsa makhalidwe oipa monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (Yohane 15:19; Aroma 1:25-27) M’malo mophunzitsa Mawu a Mulungu, aneneri onyengawa amangokhalira kuphunzitsa zinthu za m’mutu mwawo komanso kuchita miyambo yachikunja. (Mateyu 15:3, 9) Komatu Yesu anawauza kuti adyetse nkhosa zake. (Yohane 21:17) Ndiye m’malo mophunzitsa anthu mawu a Mulungu, akumangowamata phula m’maso.

  • Atsogoleri ambiri a zipembedzo ndi adyera: Lipoti lina linanenanso kuti, anthu ambiri akusiya kupemphera chifukwa akuona kuti nkhani yaikulu m’zipembedzomu ikumangokhala perekaniperekani. (Pew Research Center) Kuwonjezera pamenepa, atsogoleri ambiri a zipembedzo akukhala moyo wofewa kwambiri, chonsecho nkhosa zawo zili mu umphawi wadzaoneni. Mwachitsanzo, mumzinda wina ku Germany muli Akatolika ambiri osauka. Koma Bishopu wawo ndi wolemera kwambiri moti anthu akumudzudzula chifukwa akuona kuti amawadyera masuku pamutu. Lipoti linanso linanena kuti ku Nigeria, “kuli anthu 100 miliyoni omwe amasowa ndi ya mchere yomwe, koma abusa a matchalitchi awo amachita kusambira mu ndalama.”

    ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu sitichita nawo malonda.” (2 Akorinto 2:17) Pa nthawi imene Paulo ankalemba mawu amenewa, n’kuti ali ndi udindo waukulu kwambiri mumpingo. Koma m’malo momangodikira kuti anthu azimupatsa ndalama, Paulo ankagwira ntchito mwakhama. Ankachita zimenezi kuti asapatse ena chintchito choti azimusamalira. (Machitidwe 20:34) Zimene ankachitazi zikusonyeza kuti ankamvera zimene Yesu ananena zoti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:7, 8.

Zimenezi n’zimenenso a Mboni za Yehova amachita. Amagawira anthu mabuku, magazini, timapepala komanso zinthu zina zofotokoza mfundo za m’Baibulo kwaulere. Komanso samatolera chakhumi kapena kuyendetsa mbale ya chopereka. Ndalama zimene amayendetsera ntchito yawo zimakhala zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.—Mateyu 6:2, 3.

Baibulo Linaneneratu Kuti Anthu Ambiri Adzasiya Kupemphera

Zaka zapitazo, palibe amene ankalota kuti zimenezi zingachitike. Komatu Mulungu ananeneratu m’Baibulo kuti anthu adzasiya kupita kuzipembedzo zawo. Anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa ponena za zipembedzo zonse zabodza. Ananena kuti zipembedzozi zili ngati “hule” ndipo anazitchula ndi dzina lakuti, “Babulo Wamkulu.”—Chivumbulutso 17:1, 5.

M’pake kuti anazitchula kuti “hule,” chifukwa hule sakhala ndi mwamuna mmodzi. Nazonso zipembedzozi zimanena kuti zimalambira Mulungu yekha basi, chonsecho zimagwirizana kwambiri ndi atsogoleri andale kuti zikhale ndi mphamvu komanso kuti zipeze chuma. N’chifukwa chake lemba la Chivumbulutso 18:9 limanena kuti: ‘Mafumu a dziko lapansi anachita naye dama.’ Dzina lakuti “Babulo Wamkulu” ndi loyenereranso, chifukwa linachokera ku dzina la mzinda wakale wa Babulo. Anthu a mumzindawu ankakhulupirira zinthu zabodza komanso ankachita zamizimu. Nazonso zipembedzozi zimatchedwa Babulo Wamkulu chifukwa zimaphunzitsa zinthu zabodza monga Utatu, kukhulupirira mizimu komanso zoti mzimu umapitirizabe kukhala ndi moyo munthu akafa. *Yesaya 47:1, 8-11.

Mzinda wakale wa Babulo unali wotetezeka kwambiri chifukwa unazunguliridwa ndi mtsinje wa Firate. Ndiye Amedi ndi Aperisi anaphwetsa mtsinjewu ndipo anadutsa bwinobwino n’kulanda mzindawu popanda wolimbana naye. (Yeremiya 50:1, 2, 38) Tangoganizani, asilikaliwa analanda mzindawo usiku umodzi wokha basi.—Danieli 5:7, 28, 30.

Zipembedzo zabodza zomwe ndi Babulo Wamkulu zilinso “pamadzi ambiri.” Baibulo limanena kuti madzi amenewa ‘akuimira mitundu ya anthu komanso makamu.’ (Chivumbulutso 17:1, 15) Ndiyeno linaneneratu kuti madziwa adzauma ndipo zimenezi zidzasonyeza kuti Babulo Wamkulu watsala pang’ono kuwonongedwa. (Chivumbulutso 16:12; 18:8) Koma kodi Babulo Wamkuluyu adzawonongedwa ndi ndani? Adzawonongedwa ndi olamulira a dzikoli. Zimenezi zingaoneke zosatheka chifukwa panopa a zipembedzo ndi olamulira a dzikoli, ali khethekhethe. Koma mofanana ndi Babulo wakale, yemwe ankaoneka ngati wosagonjetseka, Babulo Wamkuluyu adzawonongedwa ndithu, ndipo olamulirawa adzamutembenukira poyerayera n’kumuwononga.—Chivumbulutso 17:16, 17. *

Kuphwa kwa madzi komwe kunachitika ku Babulo wakale, kukuimira kuchoka kwa anthu m’Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zabodza

“Tulukani Mwa Iye”

Monga taonera, Babulo Wamkulu yemwe akuimira zipembedzo zonse zabodza, awonongedwa posachedwapa. Choncho Mulungu akuchenjeza anthu kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.” (Chivumbulutso 18:4) Apatu n’zoonekeratu kuti Mulungu akufuna kuthandiza anthu a mitima yabwino omwe akupusitsidwa ndi zipembedzo zabodza kuti asakumane ndi tsoka limeneli.

A Gaffar komanso a Hediye, omwe tawatchula kumayambiriro aja, anamvera chenjezo limeneli. A Gaffar asanaphunzire Baibulo, ankalambira Mulungu chifukwa choopa kuti adzawawotcha kumoto. Koma ataphunzira Baibulo ananena kuti: “Ndinasangalala kwambiri nditazindikira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi komanso kuti amafuna tizimumvera chifukwa chomukonda, osati chifukwa cha mantha.” (1 Yohane 4:8; 5:3) Nawonso a Hediye, mtima unakhala pansi atadziwa kuti si Mulungu amene anapangitsa kuti akhale amasiye komanso kuti sanalemberetu zonse zimene zidzachitike pa moyo wawo. Anasangalalanso kwambiri atawerenga lemba la Yakobo 1:13, lomwe limanena kuti Mulungu sayesa munthu ndi zinthu zoipa. Choncho a Gaffar komanso a Hediye, atazindikira kuti ali m’chipembedzo chabodza, anathawa m’Babulo Wamkulu n’kulowa m’chipembedzo choona.—Yohane 17:17.

Ndiyetu anthu onse amene akutuluka m’Babulo Wamkulu, n’kuyamba ‘kulambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi,’ akuchita zinthu mwanzeru kwambiri. (Yohane 4:23) Posachedwapa, anthu amenewa adzasangalala kukhala ‘m’dziko lapansi lodzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.’—Yesaya 11:9.

Popeza Mulungu “sanganame,” sitikukayikira kuti zipembedzo zonse zabodza zidzawonongedwa. (Tito 1:2) Koma chipembedzo choona chidzakhalapo mpaka kalekale.

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yonena za Babulo Wamkulu, zomwe zimachitika munthu akamwalira, kukhulupirira mizimu komanso nkhani zina, werengani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.mt711.com/ny.

^ ndime 18 Onani nkhani yakuti, “Zimene Baibulo Limanena—Kodi Dzikoli Lidzathadi?” patsamba 14.