Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 1 2021 | Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Moyo Wosangalala

Tonsefe timafuna kukhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala. Tiyeni tione ngati n’zotheka kupeza nzeru zomwe zingatithandize kukhala ndi moyo woterewu.

 

Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Moyo Wosangalala

Mulungu Wamphamvuyonse amatipatsa nzeru zomwe zingatithandize kukhala ndi moyo wosangalala panopa, komanso m’tsogolo.

Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Banja Losangalala

Kodi amuna, akazi, makolo komanso ana angatani kuti azisangalala m’banja?

Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendere Ndi Anzathu

Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kuti tizikhalabe mwamtendere ndi anthu ena?

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Okhutira

Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kukhala ndi moyo wosangalala komanso wokhutira?

N’chifukwa Chiyani Timavutika, Kukalamba Komanso Kufa?

Onani zinthu 4 zimene zimachititsa kuti tizivutika, kukalamba komanso kufa.

Zimene Mlengi Wathu Amatiphunzitsa Zimatipatsa Chiyembekezo

Tiyeni tione malonjezo ena osangalatsa amene amatitsimikizira za zinthu zimene zichitike posachedwapa.

Tikamudziwa Bwino Mlengi Wathu Timafuna Kukhala Anzake

Kodi Baibulo limatiuza ndi zinthu ziti zokhudza Mulungu zimene zingakuchititseni kuti mumudziwe bwino komanso mukhale mnzake?

Mukhoza Kupeza Nzeru

Nzeru za Mulungu mukhoza kuzipeza, ndipo iye akukupemphani kuti inunso zikuthandizeni. Kodi muvomera?

Kodi mukufuna kudziwa zambiri?

Ngati ndi choncho, pali mavidiyo, makatuni, zochitika pa moyo wa anthu ena komanso nkhani zimene zingakuthandizeni kusankha bwino zochita komanso kukhala ndi moyo wabwino.