Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA

Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa​—Zimene Mungachite Panopa

Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa​—Zimene Mungachite Panopa

Pali malangizo ambirimbiri othandizira anthu omwe aferedwa ndipo ena amakhala othandiza kuposa ena. Mwina zimenezi zili choncho chifukwa monga tinafotokozera poyamba paja, anthufe timasonyeza chisoni mosiyanasiyana. Choncho zomwe zingakhale zothandiza kwa wina sizingakhale zothandizanso kwa wina.

Komabe pali mfundo zina zomwe anthu ambiri anaziona kuti n’zothandiza. Mfundozi ndi zomwe kawirikawiri akatswiri othandiza anthu omwe aferedwa, amapereka ndipo zimagwirizana kwambiri ndi mfundo za m’Baibulo.

1: MUZICHEZA NDI ACHIBALE KOMANSO ANZANU

  • Akatswiri ena amaona kuti njira imeneyi ndi yabwino kwambiri ukafuna kuchepetsa chisoni. Komabe nthawi zina mungaone kuti ndi bwino kungokhala panokha. Mwinanso anthu ena akamakuthandizani mungamamve ngati akungokutopetsani. Umu ndi mmenenso ena amamvera.

  • Musaganize kuti mukufunika kukhala limodzi ndi anzanu nthawi zonse. Komanso sibwino kuwathamangitsa chifukwa nthawi ina mudzafuna thandizo lawo. Choncho muziwauza mwaulemu zimene mukufuna ndi zimene simukufuna pa nthawiyo.

  • Muyenera kugawa bwino nthawi yokhala ndi anzanu komanso yochita zinthu panokha mogwirizana ndi mmene mukumvera.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Awiri amaposa mmodzi . . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.”​—Mlaliki 4:9, 10.

2: MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI KOMANSO KUCHITA MASEWERA OLIMBITSA THUPI

  • Zakudya za magulu onse zingakuthandizeni kuti muthe kupirira mukakhala ndi chisoni. Muzidya zipatso, ndiwo zamasamba komanso zakudya zokhala ndi mapulotini.

  • Muzimwa madzi ambiri komanso zakumwa zina zopatsa thanzi.

  • Mukaona kuti simukulakalaka kudya, muzingodya pang’ono koma pafupipafupi. Mukhozanso kupempha a dokotala kuti akupatseni mankhwala othandiza kubwezeretsa zofunika m’thupi. *

  • Muziyenda mwandawala kapena kuchita masewera enaake olimbitsa thupi kuti muchepetseko nkhawa. Nthawi zina kuchita masewera olimbitsa thupi kungakupatseni mpata woganizira za womwalirayo kapenanso zinthu zina.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”​—Aefeso 5:29.

3: MUZIGONA MOKWANIRA

  • Nthawi zonse kugona mokwanira n’kofunika kwambiri makamaka kwa anthu amene aferedwa. Tikutero chifukwa chisoni chimapangitsa munthu kumva kutopa mwachilendo.

  • Musamamwe kwambiri khofi kapena mowa chifukwa zakumwa zimenezi zimachititsa kuti munthu azisowa tulo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”​—Mlaliki 4:6.

4: MUZIUZA ENA MMENE MUKUMVERA

  • Muzikumbukira kuti anthufe timamva chisoni mosiyanasiyana. Ndiyeno mumafunika kudziwa njira yomwe ingakuthandizeni inuyo.

  • Anthu ena akakhala ndi chisoni amaona kuti amamvako bwino akauza ena mmene akumvera. Pomwe ena amaona kuti imeneyi si njira yabwino. Koma akatswiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Mukaona kuti mukufunika kuuza winawake mmene mukumvera koma mukukayikakayika, mukhoza kuyamba ndi kufotokoza zinthu zing’onozing’ono kwa mnzanu yemwe mumamudalira.

  • Anthu ena amaona kuti kulira kumawathandiza kuti achepetseko chisoni pamene ena sachita kufunika kuti alire kwambiri.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu.”​—Miyambo 14:10.

5: MUZIPEWA ZINTHU ZOMWE ZINGAWONONGE THANZI LANU

  • Anthu ena akaferedwa amaganiza kuti kumwa mowa kwambiri komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kungawachepetsere nkhawa. Komatu zimenezi zimawononga thanzi lawo. Mtendere womwe amapezawo umangokhala wa kanthawi kochepa koma pamapeto pake zimawabweretsera mavuto aakulu. Choncho mukakhala ndi nkhawa muzipeza njira zabwino zomwe zingakuthandizeni.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.”​—2 Akorinto 7:1.

6: MUZIPEZA NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZINA

  • Ena amaona kuti zimakhala zothandiza kuti pa nthawi imene ayamba kumva kwambiri chisoni, azichita zinazake zomwe zingawachititse kuti asamaganizire kwambiri za malemuyo.

  • Mukhozanso kuchepetsako nkhawa mukamacheza ndi anzanu, kupeza anthu atsopano ocheza nawo, kuphunzira zinthu zatsopano komanso kuchita zinthu zina zosangalatsa.

  • Nthawi ikamadutsa zinthu zimasintha ndipo mudzaona kuti mwayamba kuiwalako moti zikhoza kumakutengerani kanthawi kuti muyambirenso kuganizira za womwalirayo. Zikatere ndiye kuti chisoni chanu chayamba kuchepa.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . Nthawi yolira ndi nthawi yoseka. Nthawi yolira mofuula ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.”​—Mlaliki 3:1, 4.

7: MUZICHITA ZINTHU MMENE MUNKACHITIRA POYAMBA

  • Musachedwe kuyambanso kuchita zinthu ngati kale.

  • Mukayambiranso kugona pa nthawi imene munkagona poyamba, kugwira ntchito komanso kuchita zinthu zina zomwe munkachita, sizingakuvuteni kuti muyambirenso kuzolowera.

  • Mukamatanganidwa ndi kuchita zinthu zofunika, mudzachepetsa chisoni chanu.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pakuti zowawa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukira kawirikawiri, chifukwa Mulungu woona akuchititsa kuti mtima wake uzisangalala.”​—Mlaliki 5:20.

8: MUSAMAPUPULUME POSANKHA ZOCHITA PA NKHANI ZIKULUZIKULU

  • Anthu ambiri amene amasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu wokondedwa wawo atangomwalira kumene, amadzanong’oneza bondo.

  • Ngati n’kotheka muzidikira kaye kuti padutse nthawi yokwanira musanasamuke, kusintha ntchito yomwe munkagwira, kuwononga kapena kupatsa ena katundu wa malemuyo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”​—Miyambo 21:5.

9: MUZIKUMBUKIRA MALEMUYO

  • Anthu ambiri omwe anaferedwa, amamvako bwino akamachita zinthu zomwe zimawathandiza kukumbukira womwalirayo.

  • Zikhozanso kukuthandizani ngati mutasunga zithunzi komanso zinthu zina kuti muzikumbukirabe malemuyo. Mungakhalenso ndi buku loti muzilembamo nkhani zomwe mukufuna kuti muzizikumbukira.

  • Mungasungenso zinthu zomwe zingamakukumbutseni zinthu zabwino zokhudza malemuyo kuti mudzazione nthawi ina mtima ukadzakhala m’malo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kumbukirani masiku akale.”​—Deuteronomo 32:7.

10: MUTHA KUCHOKAPO KWA MASIKU ANGAPO

  • Mukhoza kukonza zoti mukapitidweko mphepo kwinakwake.

  • Ngati simungakwanitse kupita kwinakwake kwa masiku angapo, mukhoza kungochita zinthu zina zoti musangalale nazo kwa tsiku limodzi kapena awiri. Mwina mungapite kunyanja kapena kukaona malo enaake.

  • Ndipotu ngakhale kungochita zinthu zina zosiyana ndi zomwe mumachita nthawi zonse, kungakuthandizeni kuchepetsako chisoni.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”​—Maliko 6:31.

11: MUZITHANDIZA ANTHU ENA

  • Muzikumbukira kuti nthawi iliyonse imene mukuthandiza ena, nanunso mumasangalala.

  • Mungayambe ndi kuthandiza anthu enanso omwe akhudzidwa ndi imfa ya wokondedwa wanuyo, monga achibale ndi anzanu.

  • Mukathandiza ena komanso kuwalimbikitsa pa nthawi yomwe muli ndi chisoni, zingakuthandizeni kuti muyambirenso kusangalala.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

12: MUZIONANSO BWINO ZIMENE MUMACHITA

  • Mukaferedwa, mumakhala ndi mpata woganizira zinthu zofunika kwambiri.

  • Muzipezeraponso mwayi woganizira zimene mumachita pa moyo wanu.

  • Ngati n’kotheka sinthani zina ndi zina zomwe mumachita.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero, chifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Chotero munthu amene ali moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake.”​—Mlaliki 7:2.

Kunena zoona, sizingatheke kuti chisoni chanu chidzatheretu. Komabe anthu ambiri amene okondedwa awo anamwalira, anapeza umboni woti kutsatira mfundo zoyenera monga zomwe zili m’nkhaniyi kumawathandiza kuti azisangalala. Ndipotu si kuti nkhaniyi yafotokoza njira zonse zomwe munthu angatsatire kuti achepetseko chisoni. Koma ngati mutayesa kugwiritsa ntchito mfundo zomwe zafotokozedwazi, mukhoza kuona kuti chisoni chanu chayamba kuchepa n’kuyambiranso kukhala osangalala.

^ ndime 13 Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu thandizo la mankhwala.