Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi

Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi

Mwamuna wina dzina lake Joshua anati: “Ndinamva phokoso logonthetsa m’khutu ngati kuti kwaphulika bomba moti ndinatsala pang’ono kugwa. Kenako ndinangoona utsi, zitatero ofesi yonse inayamba kuyaka.”

Tikamawerenga nkhani munyuzi kapena kumvetsera pawailesi, sizachilendo kumva kuti kwinakwake kwachitika zauchigawenga, mphepo yamkutho, chivomezi kapenanso kuti ana asukulu aomberedwa. Komatu kungomva kapena kuwerenga chabe za ngozi inayake n’kosiyana kwambiri ndi kuti ngoziyo yakuchitikirani. Ndiye kodi mungatani ngozi isanachitike, ikamachitika kapenanso pambuyo poti yachitika?

ISANACHITIKE-MUZIKONZEKERA

PALIBE amene angapewe ngozi zadzidzidzi. Koma kuti tipulumuke, chofunika kwambiri ndi kukonzekera. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene tingakonzekere?

  • Muzikonzekeretsa maganizo anu. Muyenera kudziwa kuti ngozi zimachitika ndithu ndipo inuyo ndi anthu omwe mumawakonda mukhoza kukhudzidwa ndi ngozi inayake. Izi zikusonyeza kuti si nzeru kuyamba kukonzekera pambuyo poti ngoziyo yachitika kale.

  • Muzidziwiratu ngozi zimene zingachitike m’dera lanu. Muzidziwiratu kumene mungakabisale. Onetsetsani kuti nyumba yanu ndi yolimba komanso muyenera kudziwa ngati dera limene mukukhala lili lotetezeka. Komanso muzisamala ndi zinthu zimene zingayambitse moto mosavuta. Ngati n’zotheka mungaike alamu yokuchenjezani yomwe imalira moto ukangoyamba ndipo muzisintha mabatire ake pafupipafupi.

  • Muzikhala ndi zinthu zimene zingakuthandizeni pa nthawi ya ngozi. Pa nthawi ya ngozi madzi angasiye, magetsi angazime, mafoni angasiye kugwira ntchito komanso mafuta a galimoto angasowe. Choncho muzisunga chakudya, madzi ndipo ngati muli ndi galimoto muzisunga mafuta okwanira mugalimoto yanu. Muzisunganso zinthu zina zimene zingakuthandizeni pakachika ngozi.​—Onani bokosi lakuti “ Kodi Munasunga Zinthu Zimene Zingakuthandizeni?

    Kukonzekera n’kofunika kwambiri kuti munthu apulumuke

  • Muzikhala ndi manambala a foni a anzanu, kaya anzanuwo amakhala pafupi kapena kutali.

  • Muziyeserera mmene mungadzachitire kuti mudzapulumuke pa nthawi ya ngozi. Ngati muli m’nyumba, muyenera kudziwa kumene mungatulukire ngati patachitika ngozi yadzidzidzi. Muzifotokozeranso ana anu zimene angachite ngati kusukulu kwawo kutachitika ngozi yadzidzidzi. Muzikambirana ndi banja lanu malo amene mungapezane mosavuta m’deralo ngati zimenezi zitachitika. M’mayiko ena, akuluakulu a boma amalimbikitsa anthu kuti aziyeserera zimenezi limodzi ndi mabanja awo.

  • Muzikhala okonzeka kuthandiza anzanu, kuphatikizapo achikulire ndi olumala.

IKAMACHITIKA-MUZICHITA ZINTHU MOFULUMIRA

Joshua amene tamutchula poyamba uja ananena kuti: “Moto utayambika, anthu ambiri ankazengereza. Ena ankachedwa ndi kuzimitsa makompyuta pomwe ena ankakatunga madzi akumwa ndipo bambo wina anati, ‘Mwina tingodikira kaye.’” Ataona kuti anthuwo akuchita chidodo, Joshua anakuwa kuti: “Tiyeni tituluke pompano!” Atangotero anthu onse anasiya zomwe ankapanga m’maofesi awo n’kuyamba kumutsatira pamene amakatsika masitepe kuti akatuluke panja. Ndipo iye anapitiriza kukuwa kuti, “Wina akagwa m’dzutseni, tonse tituluka bwinobwino ndipo tipulumuka!”

  • Pakabuka moto. Muzigona pansi ndipo ngati n’kotheka muziyesetsa kutuluka mwachangu. Utsi umachititsa kuti munthu azivutika kuona ndipo anthu ambiri amafa chifukwa chobanika ndi utsi. Musamachedwe ndi kutulutsa katundu. Zimene zingachitike pa mphindi zochepa chabe zingapangitse kuti mupulumuke kapena mufe.

  • Pakachitika chivomezi. Muzibisala pamalo amene ndi otetezeka kapena pansi pa chinthu chomwe ndi cholimba kwambiri. Ngati mungakwanitse muziyesetsa kutuluka mofulumira n’kukaima chapatali chifukwa nyumbayo ikhoza kumagwedezekabe. Komanso ngati zingatheke muziyesetsa kupulumutsa anthu ena chifukwa nthawi zina ogwira ntchito yopulumutsa anthu pangozi amafika mochedwerapo.

  • Kukachitika tsunami. Madzi akangophwera mwadzidzidzi m’nyanja, muzichoka mofulumira n’kuthawira kumalo okwera chifukwa madziwo akamabwerera, kumachitika mafunde amphamvu komanso akuluakulu.

  • Kukachitika mphepo yamkuntho. Muzikabisala mofulumira pamalo otetezeka.

  • Madzi akasefukira. Musamakhale m’nyumba zimene mwalowa madzi osefukira. Musamayende kapena kuyendetsa galimoto pamadzi chifukwa akhoza kukhala ndi zinthu zonyansa komanso zinthu zomwe zingakuvulazeni. Zimenezi zingaphatikizepo zinyalala, maenje ndiponso mawaya a magetsi.

  • Kodi mukudziwa? Madzi akuya masentimita 60 okha amene akuyenda akhoza kukokolola galimoto. Ndipotu anthu ambiri amafa chifukwa choyendetsa galimoto pamadzi osefukira.

  • Ngati akuluakulu a boma alamula kuti anthu achoke m’dera lanulo, muyenera kuchoka mwansanga. Muzidziwitsa anzanu za kumene mwapita chifukwa mwina akhoza kuika moyo wawo pangozi pokufunafunani.

    Ngati akuluakulu a boma alamula kuti anthu achoke m’dera lanulo, muyenera kuchoka mwansanga

  • Kodi mukudziwa? Pa nthawi yangozi zadzidzidzi kutumizira ena mameseji kumakhala kodalirika kusiyana ndi kuwaimbira foni.

  • Akuluakulu a boma akalamula kuti anthu akhale m’nyumba zawo, muyenera kumvera. Ngati ngozi yake yachitika chifukwa cha mabomba kapena makemiko omwe ali ndi mpweya woipa, musamatuluke m’nyumba. Muzitsekanso mawindo, zitseko ndi malo aliwonse omwe pangalowere mpweya. Pakaphulika bomba la nyukiliya, muzipita m’chipinda chamkati choti mpweya wapoizoni wa bombalo sungafikemo. Muzimvetsera nkhani pa wailesi kapena pa TV ya m’dziko lanu. Muzikhalabe m’nyumba mpaka akuluakulu a boma atalengeza kuti ngoziyo yatha.

PAMBUYO POTI YACHITIKA-MUZIKHALA PAMALO OTETEZEKA

Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti mupewe matenda komanso zinthu zomwe zingakuvulazeni:

  • Ngati n’zotheka muzikakhala kunyumba kwa anzanu m’malo mokakhala kukampu.

  • Muziyesetsa kusamalira bwino malo amene mukukhala kuti azikhala aukhondo.

  • Muzivala zovala zodzitetezera mukamachotsa zinyalala ndi zinthu zowonongeka. Muzivala chipewa cholimba, magulovesi, chodzitetezera kufumbi komanso nsapato zolimba. Muzisamalanso ndi mawaya a magetsi komanso zinthu zomwe zatsala ndi moto.

  • Muziyesetsa kuchita zimene munkachita tsiku ndi tsiku. Ana anu asamaone kuti mukudandaula kwambiri ndipo muziwasonyeza kuti zinthu zonse zikhala bwino. Muzipeza nthawi yophunzitsa ana anu zinthu za kusukulu, kusewera nawo komanso muzichita kulambira kwa pabanja. Mukamamvetsera nkhani, maganizo anu asamakhale kwambiri pa zinthu zomvetsa chisoni. Ndipo mukakhala ndi nkhawa musamakwiyire anthu a m’banja lanu. Muzilola kuti ena akuthandizeni ndipo inunso muzithandiza anzanu.

    Pambuyo poti ngozi yachitika muziyesetsa kuchita zimene munkachita tsiku ndi tsiku

  • Muzidziwa kuti zinthu zambiri zingawonongeke pangoziyo. Cholinga chachikulu cha boma komanso anthu ena omwe amathandiza pakachitika ngozi, chimakhala kupulumutsa anthu osati kubwezeretsa zinthu zimene zawonongeka. Chofunika kwambiri kuti tikhale ndi moyo ndi madzi abwino, chakudya, zovala komanso malo ogona.​—1 Timoteyo 6:7, 8.

  • Muzidziwa kuti ngoziyo ingasokoneze maganizo anu ndipo muzifufuza thandizo. Nthawi zambiri zimenezi zingayambe kuonekera pambuyo pangoziyo. Zina mwa zizindikiro zake zingakhale kuda nkhawa, kuvutika maganizo, kulephera kugwira ntchito komanso kusowa tulo. Zikatere muyenera kufotokozera anzanu omwe angakuthandizeni.

Ngakhale kuti Joshua anapulumuka pangozi ya moto imene inachitika ku ofesi kwake, anzake ambiri sanapulumuke. Iye anathandizidwa ndi akulu mumpingo komanso akatswiri othandiza anthu ovutika maganizo. Joshua anati: “Iwo ananditsimikizira kuti chisoni chimene ndinkamva chinali umboni woti ndikuchira. Patadutsa miyezi 6 ndinasiya kulota zinthu zokhudza ngoziyo. Komabe panali zinthu zina zimene zinanditengera nthawi kuti ndisiye kuvutika nazo.”

Ngozi zadzidzidzi zimapangitsa anthu ena kuti ayambe kuganiza molakwika. Mwachitsanzo, ena amayamba kuimba Mulungu mlandu kuti ndi amene amachititsa zoipa. Pomwe ena monga Joshua amadziimba okha mlandu. Joshua ananena kuti, “Ndimangoona ngati pali zinthu zina zimene ndikanachita kuti ndipulumutse anthu ambiri. Komabe zimandilimbikitsa podziwa kuti posachedwapa Mulungu yemwe ndi wachilungamo adzachotsa zoipa zonse. Panopa ndimathokoza kuti ndili ndi moyo ndipo ndimachita zilizonse zimene ndingathe kuti ndiziusamalira.”​—Chivumbulutso 21:4, 5. *

^ ndime 33 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Mulungu walonjeza komanso chifukwa chake walola kuti anthu azivutika, werengani buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Mungathe kupanga dawunilodi bukuli pa jw.org/ny.