Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amadziwa Mmene Mumamvera?

Kodi Mulungu Amadziwa Mmene Mumamvera?

ZIMENE CHILENGEDWE CHIMATIPHUNZITSA PA NKHANIYI

Munthu amene amadziwa mmene wina akumvera amayerekezera kukhala munthu winayo n’kuona mmene akanamvera zikanakhala kuti zikuchitikira iyeyo. Katswiri wina woona za matenda a maganizo, dzina lake Dr. Rick Hanson, ananena kuti “aliyense analengedwa kuti azitha kuchita zimenezi.”

TAGANIZIRANI MFUNDO IYI: N’chifukwa chiyani Mulungu anatilenga kuti tizitha kumva mmene wina akumvera mosiyana ndi zinyama? Baibulo limanena kuti Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26) Popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, timatha kusonyeza makhalidwe abwino amene iye ali nawo. Choncho anthu akamayesetsa kuthandiza ena chifukwa chokhudzidwa mtima, amakhala akusonyeza mmene Mlengi wathu Yehova amachitira.​—Miyambo 14:31.

BAIBULO LIMASONYEZA KUTI MULUNGU AMADZIWA MMENE TIMAMVERA

Mulungu amatimvera chisoni ndipo sasangalala akamaona tikuvutika. Aisiraeli ankazunzidwa koopsa pamene anali kuukapolo ku Iguputo ndipo ankafunikanso kupirira zaka 40 m’chipululu. Pofotokoza mmene Yehova ankamvera poona zimenezi, Baibulo limati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” (Yesaya 63:9) Onani kuti Yehova sankangodziwa za mavuto amene ankakumana nawowa. Iyenso ankavutika moti ankamva mmene iwo ankamvera. Iye anati: “Ndikudziwa bwino zowawa zawo.” (Ekisodo 3:7) Ananenanso kuti: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.” (Zekariya 2:8) Anthu ena akamatizunza, nayenso Mulungu amavutika.

Komabe nthawi zina tikhoza kumadziimba mlandu komanso kumaona kuti si ife oyenerera kusonyezedwa chikondi ndi Mulungu. Zimenezi zikachitika, ndi bwino kumakumbukira kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Mulungu amatidziwa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziwira. Amadziwa zimene zikutichitikira, maganizo athu komanso mmene tikumvera. Ndipo tikamavutika nayenso amavutika nafe limodzi.

Tizidalira Mulungu kuti azititonthoza, kutipatsa nzeru komanso kutithandiza popeza iye amasamalira anthu amene akukumana ndi mavuto

Malemba awa amatitsimikizira mfundo imeneyi

  • “Mudzaitana ndipo Yehova adzakuyankhani. Mudzafuula popempha ndipo iye adzayankha kuti, ‘Ndikumva lankhulani!’”​—YESAYA 58:9.

  • “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova. ‘Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.’”​—YEREMIYA 29:11, 12.

  • “Sungani misozi yanga m’thumba lanu lachikopa. Kodi misozi yanga sili m’buku lanu?”​—SALIMO 56:8.

MULUNGU AMACHITA NAFE CHIDWI, AMATIMVETSA KOMANSO AMADZIWA MMENE TIMAMVERA

Kodi kuzindikira mfundo yoti Mulungu amadziwa mmene timamvera kungatithandize bwanji kupirira mavuto amene tikukumana nawo? Taganizirani zimene zinachitikira Maria. Iye anati:

“Zinali zowawa komanso zokhumudwitsa kwambiri pamene mwana wanga wa zaka 18 anamwalira atadwala khansa kwa zaka ziwiri. Ndinkaona kuti zimene zinachitikazi si zachilungamo moti ndinakwiyira Yehova kuti sanamuchiritse.”

“Patadutsa zaka 6, mnzanga wina wa mumpingo anabwera kwathu ndipo anandimvetsera pamene ndinkamuuza kuti ndimaona kuti Yehova sandikonda. Iye sanandidule mawu pamene ndinkamufotokozera zimenezi. Ndipo nditamaliza anatchula mfundo ya palemba la 1 Yohane 3:19, 20. Lembali limati: ‘Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.’ Kenako anandifotokozera kuti Yehova amamvetsa mavuto amene tikukumana nawo. Zimenezi zinandikhudza mtima kwambiri.”

“Ngakhale anandiuza zimenezi sizinali zophweka kuti ndisiye kumukwiyira Mulungu. Kenako ndinawerenga lemba la Salimo 94:19, lomwe limati: ‘Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.’ Zinkangokhala ngati lembali analembera ineyo. N’kupita kwa nthawi, ndinayamba kumva bwino ndikamalankhula ndi Yehova n’kumamuuza nkhawa zanga chifukwa ndinkadziwa kuti amandimvetsera.”

N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu amatimvetsa komanso amadziwa mmene tikumvera. Koma nanga n’chifukwa chiyani timakumana ndi mavuto? Kodi Mulungu amakhala akutilanga chifukwa cha machimo athu? Kodi pali zimene Mulungu wakonza kuti athetse mavutowa? Mafunso amenewa ayankhidwa munkhani zotsatirazi.