Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Ntchito Yomasulira Buku Lofunika Kwambiri

Ntchito Yomasulira Buku Lofunika Kwambiri

1 JANUARY 2021

 ”Ndakhala ndikuliyembezera kwa zaka 19.” Kodi m’bale wathuyu ankayembekezera chiyani? Ankayembekezera Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chibengali. Mofanana ndi m’baleyu, anthu ambiri amasangalala akalandira Baibulo la Dziko Latsopano m’chinenero chawo. Kodi munayamba mwaganizirapo mmene ntchito yomasulira komanso kusindikiza Mabaibulo imayendera?

 Choyamba, abale ndi alongo oti agwire ntchito yomasulirayi amasankhidwa potsatira malangizo ochokera ku Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku ya Bungwe Lolamulira. Kodi ntchito yomasulira Baibulo imatenga nthawi yaitali bwanji? M’bale Nicholas Ahladis wa m’Dipatimenti Yothandiza Omasulira ku Warwick, New York anati: “Pali zinthu zambiri zimene zimafunika kuziganizira ntchito yomasulira isanayambike. Pamafunika kuganizira kuti pafunika omasulira angati, mmene chilankhulocho chilili, kusiyana kwa chilankhulocho m’madera osiyanasiyana komanso mmene anthu amene akaliwerenge amaonera chikhalidwe cha anthu omwe anakhalapo pa nthawi imene Baibulo linkalembedwa. Pomwe kumasulira Baibulo m’chinenero chamanja, kumatenga nthawi yaitali kwambiri kuposa pamenepa.”

 Sikuti pamangofunika omasulira okha kuti Baibulo limasuliridwe. Pamafunikanso abale ndi alongo ena ochokera m’madera osiyanasiyana amene amathandiza kuwerenga zomwe zamasuliridwazo kuti aone ngati zili zomveka bwino. Nthawi zina, amakhala ochokera m’mayiko osiyanasiyana ndipo amagwira ntchitoyi mongodzipereka. Ndemanga za abale ndi alongowa zimathandiza kuti Baibulo limasuliridwe molondola, momveka bwino, ndiponso kuti likhale lothandiza kwambiri. M’bale amene amagwira ntchito yophunzitsa omasulira Baibulo ku South Africa anafotokoza kuti “omasulira amaona kuti ali ndi udindo waukulu kwambiri kwa Yehova komanso kwa anthu amene amawerenga Mawu ake.”

 Ntchito yomasulira ikatha, Baibulo limasindikizidwa. Kuti zimenezi zitheke, pamafunikira kugwiritsa ntchito zinthu zosachepera 10. Zina mwa zinthuzi ndi mapepala, inki, zikuto, zomatira, zokongoletsera ndi maliboni. Mu 2019, ndalama zoposa madola 20 miliyoni a ku America, zinagwiritsidwa ntchito pogulira zinthu zimenezi kuti asindikize Mabaibulo. M’chaka chimenechi, abale ndi alongo anathera maola oposa 300,000 posindikiza komanso kutumiza Mabaibulo m’mayiko osiyanasiyana.

“Baibulo ndi buku lofunika kwambiri pa zinthu zonse zimene timatulutsa”

 N’chifukwa chiyani timagwiritsa ntchito nthawi komanso ndalama zochuluka chonchi pa ntchito imeneyi? M’bale Joel Blue yemwe amagwira ntchito m’dipatimenti yoyang’anira ntchito yosindikiza mabuku padziko lonse anati: “Baibulo ndi buku lofunika kwambiri pa zinthu zonse zimene timatulutsa. Choncho timafuna kuti lizioneka m’njira yomwe ingachititse anthu kulemekeza Mulungu amene timamulambira ndiponso uthenga umene timalalikira.”

 Kuwonjezera pa Baibulo la Dziko Latsopano losindikizidwa, timapanganso Mabaibulo a anthu omwe ali ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, Baibulo la Dziko Latsopano la anthu omwe ali ndi vuto losaona likupezeka m’zinenero 10. Pamafunika maola 8 kuti Baibulo limodzi lokha lotereli lipangidwe ndipo lili m’mavoliyumu ambiri omwe amafunika kuwaika pashelefu yotalika mamita osachepera 2.3. Timasindikizanso Mabaibulo apadera oti akaidi azigwiritsa ntchito m’ndende. Mabaibulo amenewa amakhala ndi zikuto zofewa zofanana ndi mapepala.

 Baibulo la Dziko Latsopano limathandiza anthu ambiri omwe amaliwerenga. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinkachitika mumpingo wa anthu olankhula Chikiluba womwe uli m’dera la Tombe ku Democratic Republic of the Congo. Dera la Tombe lili pamtunda wamakilomita oposa 1,700 kuchokera kulikulu la dzikoli. M’derali a Mboni anali ndi Baibulo limodzi lokha lomwe linali m’chinenero cha Chikiluba chovuta kumva komanso chachikale. Abale ndi alongo ankabwerekana Baibulo limodzi limeneli akafuna kukonzekera misonkhano. Koma kuyambira mu August 2018, Baibulo la Dziko Latsopano la Chikiluba lathunthu komanso lomwe linamasuliridwa mogwirizana ndi mmene anthu amalankhulira panopa, linayamba kupezeka m’mipingo yonse.

 Pofotokoza za Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso la m’chinenero chake cha Chijeremani, mlongo wina anati: “Panopa ndinasiya kumangowerenga Baibulo mwamwambo. M’malomwake, ndikamawerenga ndimafunitsitsa nditadziwa zambiri pa nkhani yomwe ndikuwerengayo.” Mkaidi wina analemba kuti: “Ndinapatsidwa Baibulo la Dziko Latsopano ndipo likundithandiza kusintha moyo wanga. Baibuloli landithandiza kuti ndiziwamvetsa bwino kwambiri Mawu a Mulungu kuposa kale. Ndikufuna kudziwa zambiri zokhudza a Mboni za Yehova komanso zimene ndingachite kuti ndikhale wa Mboni.”

 Anthu onse amene amawerenga Baibulo la Dziko Latsopano amayamikira zopereka zimene zimathandizira pa ntchito yomasulira komanso kusindikiza Baibuloli. Anthu amapereka ndalama zothandizira pa ntchito yapadziko lonse imeneyi kudzera pa donate.mt711.com. Tikukuyamikirani kwambiri chifukwa chopereka mowolowa manja.