Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomwe Zimayambitsa Kuchepa kwa Magazi, Zizindikiro Zake, Komanso Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Vutoli

Zomwe Zimayambitsa Kuchepa kwa Magazi, Zizindikiro Zake, Komanso Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Vutoli

 Beth anati: “Ndili wamng’ono ndinali ndi vuto la kuchepa kwa magazi. Ndinkafooka kwambiri, sindinkachedwa kutopa, mafupa anga ankapweteka ndiponso ndinkavutika kwambiri kuika maganizo anga pa zimene ndikuchita. Dokotala wanga anandipatsa mankhwala othandiza kuonjezera magazi m’thupi. Ndinamwa mankhwalawo komanso ndinayamba kudya zakudya zopatsa thanzi. Kenako ndinayamba kupeza bwino.”

 Anthu ambiri alinso ndi vuto ngati la Beth. Mogwirizana ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena, anthu 2 biliyoni, omwe ndi 30 peresenti ya chiwerengero cha anthu padziko lonse, ali ndi vuto la kuchepa kwa magazi. M’mayiko osauka, 50 peresenti ya azimayi oyembekezera komanso 40 peresenti ya ana omwe sanayambe sukulu ali ndi vuto la kuchepa kwa magazi.

 Vuto la kuchepa kwa magazi ndi loopsa kwambiri. Magazi a munthu akachepa kwambiri m’thupi akhoza kuyamba kudwala matenda a mtima komanso mtima ukhoza kusiya kugwira ntchito yake bwinobwino. Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena kuti m’mayiko ena vuto la kuchepa kwa magazi ndi limene “limachititsa 20 peresenti ya imfa za azimayi oyembekezera.” Anthu ambiri amakhala ndi vuto la kuchepa kwa magazi chifukwa cha kusowa kwa mchere wa m’thupi wotchedwa iron. Ana omwe amabadwa kwa azimayi omwe ali ndi vuto la kuchepa kwa magazi chifukwa chosowa iron m’thupi mwawo, amabadwa masiku asanakwane komanso amakhala ochepa thupi kwambiri. Ana omwe ali ndi vuto la kuchepa kwa magazi sakula mofulumira komanso amadwaladwala. Komatu n’zotheka kupewa komanso kuthana ndi vuto la kuchepa kwa magazi lomwe limayamba chifukwa cha kusowa kwa iron. a

Vuto la Kuchepa kwa Magazi

 Kuchepa magazi ndi matenda. Mwachidule, anthu amene ali ndi vutoli sakhala ndi maselo ofiira okwanira a magazi omwe akugwira ntchito yake bwinobwino. Zimenezi zimachitika pa zifukwa zosiyanasiyana. Ndipotu asayansi atulukira mitundu yoposa 400 ya vuto la kuchepa kwa magazi. Vuto la kuchepa kwa magazi likhoza kukhala la nthawi yochepa kapena nthawi yayitali, locheperako kapena lalikulu kwambiri.

N’chiyani Chimene Chimayambitsa Vutoli?

 Pali zinthu zitatu zimene zimayambitsa vutoli:

  •   Munthu akataya magazi, maselo ofiira amayamba kuchepa m’thupi.

  •   Thupi likamalephera kupanga maselo ofiira okwanira.

  •   Thupi likamaononga maselo ofiira.

 Anthu ambiri padziko lonse amakhala ndi vuto la kuchepa kwa magazi chifukwa chakuti ali ndi iron wochepa m’thupi. Iron akakhala wochepa, thupi limakanika kupanga pulotini wam’magazi wokwanira wotchedwa himogulobini. Pulotini ameneyu amapezeka m’maselo ofiira ndipo amachititsa kuti maselowa azitha kunyamula mpweya wa okosijeni.

Zizindikiro za Kuchepa kwa Magazi Komwe Kumayambika Chifukwa cha Kuchepa kwa Iron

 Vuto la kuchepa kwa magazi limayamba pang’onopang’ono ndipo nthawi zina wodwalayo sazindikira n’komwe. Ngakhale kuti zizindikiro zake zikhoza kukhala zosiyanasiyana, zina mwa zizindikiro za kuchepa kwa magazi komwe kumayamba chifukwa cha kuchepa kwa iron ndi izi:

  •   Kutopa kwambiri

  •   Kuzizidwa manja kapena mapazi

  •   Kufooka

  •   Khungu lachikasu

  •   Kupweteka kwa mutu komanso chizungulire

  •   Kupweteka pachifuwa, kuthamanga kwa mtima, kupuma movutikira

  •   Kuuma zikhadabo

  •   Kusafuna kudya, makamaka ana

  •   Kulakalaka kudya madzi oundana, starch, kapenanso dothi

Ndani Amene Angapezeke ndi Vutoli?

 Azimayi akhoza kukhala ndi vuto la kuchepa kwa magazi lomwe limayamba chifukwa chosowa iron chifukwa amataya magazi pa nthawi yosamba. Nawonso azimayi oyembekezera angapezeke ndi vutoli ngati sadya zakudya zomwe zili ndi vitamini B wokwanira.

 Makanda omwe amabadwa masiku osakwana kapena ochepa thupi kwambiri amene sapeza iron wokwanira akamayamwa kapena kumwa mkaka wochita kupanga.

 Ana omwe sadya zakudya zosiyanasiyana zopatsa thanzi.

 Anthu odya zamasamba zokhazokha omwe sadya zakudya zokhala ndi iron wokwanira.

 Anthu omwe amadwala matenda okhalitsa, monga amene ali ndi matenda a m’magazi, khansa, vuto la impso, zilonda za m’mimba, kapenanso matenda omwe amayambitsidwa ndi majelemusi.

Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Vutoli

 N’zosatheka kupewa kapena kuchiza mitundu ina ya vuto la kuchepa kwa magazi. Koma n’zotheka kupewa kapena kuchiza mitundu yomwe imayamba chifukwa cha kusowa kwa iron kapena mavitamini ngati munthu angamadye zakudya zopatsa thanzi zomwe zili ndi zinthu izi:

 Iron. Amapezeka mu nyama, nyemba, mphodza, komanso ndiwo zamasamba zobiriwira. b Kafukufuku akusonyeza kuti kugwiritsa ntchito ziwiya zophikira za chitsulo cha iron kukhoza kuwonjezera iron mu zakudya.

 Mavitamini othandiza kupanga maselo atsopano m’thupi. Amapezeka m’zipatso, ndiwo zamasamba zobiriwira, nsawawa zobiriwira, nyemba, tchizi, mazira, nsomba, mtedza wa almond, ndi mtedza. Mavitaminiwa amapezekanso mu zakudya monga buledi, cereal, pasta ndi mpunga. Anthu amathanso kupanga mavitamini othandiza kupanga maselo atsopano m’thupi ndipo amatchedwa folic acid kapena kuti vitamini B9.

 Vitamini B-12. Amapezeka mu nyama, zakudya zopangidwa kuchokera ku mkaka, cereal komanso zakudya zopangidwa kuchokera ku soya.

 Vitamini C. Amapezeka mu zipatso monga manachesi, malalanje ndi mandimu ndi zakumwa zopangidwa kuchokera ku zipatsozi, tsabola, broccoli, tomato, mavwende, komanso masitilobere. Zakudya zomwe zili ndi vitamini C zimathandiza kuti thupi lanu lizitha kutenga iron kuchokera ku zakudya.

 Zakudya zimasiyanasiyana potengera madera. Choncho muyenera kudziwa zakudya zimene zimapezeka m’dera lanu zomwe zimakhala ndi zinthu zofunikira m’thupi. Kudziwa zimenezi n’kofunika kwambiri ngati ndinu mzimayi, makamakanso ngati muli woyembekezera kapena mukufuna kukhala woyembekezera. Mukamasamalira thanzi lanu, mudzapewa kubereka mwana yemwe ali ndi vuto la kuchepa magazi. c

a Zomwe zafotokozedwa m’nkhani ino zokhudza zakudya komanso nkhani zina zachokera mu nkhani zofalitsidwa ndi a Mayo Clinic komanso m’buku la The Gale Encyclopedia of Nursing and Allied Health. Kaonaneni ndi a dokotala ngati mukuganiza kuti muli ndi vuto la kuchepa magazi.

b Musamamwe mankhwala oonjezera iron m’thupi kapena kumupatsa mwana wanu ngati simunauzidwe ndi adokotala. Iron akachuluka kwambiri m’thupi, amaononga chiwindi komanso kuyambitsa mavuto ena.

c Nthawi zina madokotala amathandiza anthu amene ali ndi vuto la kuchepa kwa magazi powaika magazi, koma a Mboni za Yehova salola kulandira thandizo limeneli.—Machitidwe 15:28, 29.