Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zothandiza Anthu Omwe Achitiridwa Nkhanza Zosiyanasiyana

Mfundo Zothandiza Anthu Omwe Achitiridwa Nkhanza Zosiyanasiyana

Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linati: “Padziko lonse lapansi azimayi akumachitiridwa nkhanza ndipo zafala kwambiri ngati mmene matenda amafalikira. M’pofunika kuchitapo kanthu mwansanga kuti vutoli lithe.” Bungweli linanenanso kuti pafupifupi 30 peresenti ya “azimayi onse omwe anakwatiwa kapena ali ndi chibwenzi, mwamuna wawo anawamenyapo kapenanso kuwachitira nkhanza zokhudza kugonana.” Komanso lipoti lina la bungwe la UN linanena kuti m’chaka china chaposachedwapa, azimayi 137 padziko lonse ankaphedwa tsiku lililonse ndi mwamuna wawo kapena munthu wina wa m’banjamo. a

Kafukufuku akhoza kusonyeza kukula kwa nkhanza zosiyanasiyana koma sangafotokoze mavuto onse omwe munthu aliyense yemwe wachitidwa nkhanzazo wakumana nawo komanso mmene akumvera mumtima mwake.

Kodi mwachitiridwapo nkhanza? Kapena mukudziwa za munthu wina yemwe anachitiridwapo nkhanza? Ngati zili choncho, onani mfundo za m’Baibulo zotsatirazi ndipo zikuthandizani.

 Munthu wina akakuchitirani nkhanza, wolakwa si inuyo

 N’zotheka kupeza thandizo

 Sikuti muli nokha

 Nkhanza zidzatha

 Kodi mungathandize bwanji munthu yemwe wachitiridwa nkhanza?

 Munthu wina akakuchitirani nkhanza, wolakwa si inuyo

Zimene Baibulo limanena: “Aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.”—Aroma 14:12.

Kumbukirani kuti: Munthu yemwe wakuchitirani nkhanzayo wapalamula mlandu.

Ngati mwamuna wanu amakuimbani inuyo mlandu chifukwa cha nkhanza zimene iyeyo amakuchitirani, akulakwitsa. Akazi amafunika kukondedwa osati kuchitiridwa nkhanza.—Akolose 3:19.

Munthu amene amachita nkhanza nthawi zina akhoza kumachita zimenezi chifukwa choti ali ndi vuto la m’maganizo, anakulira m’banja lomwe anthu ake ankachita zachiwawa kapena chifukwa chomwa mowa mwauchidakwa. Kaya zitakhala kuti zifukwa zake ndi zimenezo, akuyenerabe kudzayankha mlandu kwa Mulungu chifukwa za zochita zakezo. Ndipotu akufunika kuyesetsa kusintha khalidwe lakelo.

 N’zotheka kupeza thandizo

Zimene Baibulo limanena: ‘Aphungu akachuluka zolingalira zimakwaniritsidwa.’—Miyambo 15:22.

Kumbukirani izi: Ngati mukuona kuti muli pachiopsezo ndipo simukudziwa zochita, anthu ena akhoza kukuthandizani.

N’chifukwa chiyani mungafunike kuthandizidwa ndi anthu ena? Ngati mwachitiridwa nkhanza mukhoza kumangoganiza zinthu zambirimbiri. Mungavutike kusankha zoyenera kuchita chifukwa choti simukudziwa kuti ndi mfundo ziti zomwe zingakuthandizeni. Mwachitsanzo mungamaganize kuti:

  • Ndingatani kuti ndikhale otetezeka?

  • Nanga bwanji za anawa?

  • Ndizikwanitsa bwanji kupeza ndalama?

  • Nanga bwanji za chikondi changa kwa mwamuna kapena mkazi wanga?

  • Ngati atasintha khalidwe lakeli, kodi ndingomukhululukira?

Mwachibadwa, zimenezi zikhoza kukusokonezani ndipo simungadziwe zoyenera kuchita. Koma kodi ndi ndani amene angakuthandizeni?

Mnzanu wodalirika kapena munthu wina wa m’banja lanu akhoza kukuthandizani kuti maganizo anu akhale m’malo. Mungayambe kumva bwino ngati mutauza munthu wina yemwe amakuganizirani.

Mukaimba foni pa manambala apadera ochitira lipoti za nkhanza zosiyanasiyana mukhoza kuthandizidwa nthawi yomweyo. Anthu omwe amagwira ntchito zothandiza anthu kudzera pa manambalawa angakuuzeni zoyenera kuchita kuti mukhale otetezeka. Ngati munthu yemwe akukuchitirani nkhanzayo wavomereza kulakwa kwake ndipo akufuna kusintha khalidwe lakelo, kudzera pa manambala amenewo akhoza kuuzidwa zoyenera kuchita.

Anthu ena othandiza pa zochitika zamwadzidzidzi akhoza kukuthandizani ngati mukufuna kuthandizidwa mwamsanga. Anthuwa angakhale madokotala, manesi kapena akatswiri ophunzitsidwa bwino.

 Sikuti muli nokha

Zimene Baibulo limanena: “Yehova b ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.

Kumbukirani izi: Mulungu akulonjeza kukuthandizani.

Yehova amakuderani kwambiri nkhawa. (1 Petulo 5:7) Iye amamvetsa mmene mumamvera mumtima mwanu komanso zimene mukuganiza. Angathe kukutonthozani kudzera m’Mawu ake, omwe amapezeka m’Baibulo. Ndipotu amafuna kuti muzimuuza nkhawa zanu m’pemphero. Mukamapemphera, muzimupempha kuti akupatseni nzeru ndi mphamvu kuti muthe kulimbana ndi mavuto anuwo.—Yesaya 41:10.

 Nkhanza zidzatha

Zimene Baibulo limanena: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”—Mika 4:4.

Kumbukirani izi: M’Baibulo muli lonjezo lakuti m’tsogolomu aliyense azidzakhala pakhomo pake mwamtendere.

Yehova Mulungu yekha ndiye amene adzathetseretu mavuto onse amene tikukumana nawo. Baibulo limati: “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Pa nthawiyo, sitidzakumbukiranso zoipa zonse m’malomwake tizidzangoganizira zinthu zabwino zokhazokha. (Yesaya 65:17) Apatu Baibulo likusonyeza kuti muzidzakhala mwamtendere m’tsogolomu.

a Ngakhale kuti nkhaniyi ikufotokoza za azimayi amene akuchitiridwa nkhanza koma mfundo zambiri zikukhudzanso nkhanza zomwe amuna amachitiridwa.

b Baibulo limasonyeza kuti dzina lenileni la Mulungu ndi Yehova.