Pitani ku nkhani yake

Kodi Muli ndi Amishonale?

Kodi Muli ndi Amishonale?

Inde. Kulikonse kumene tili, anthu tonse a Mboni za Yehova timayesetsa kukhala ndi mtima waumishonale, kutanthauza kuti nthawi zonse timayesetsa kuuza ena zimene timakhulupirira.—Mateyu 28:19, 20.

Kuwonjezera pamenepa, anthu ena a Mboni nthawi zambiri amapita kapena kusamukira m’madera ena a m’dziko lawo lomwelo, kumene anthu ambiri sanamvepo uthenga wabwino wa m’Baibulo. Koma a Mboni ena amasamukira m’mayiko ena n’cholinga choti azikalalikira uthenga wabwino. Iwo amasangalala kuchita zimenezi chifukwa amathandiza pokwaniritsa ulosi umene Yesu ananena kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8.

Mu 1943, tinatsegula sukulu yophunzitsa anthu ntchito ya umishonale. Kuyambira m’chaka chimenecho, anthu a Mboni oposa 8,000 aphunzitsidwa kusukulu imeneyi, yomwe imadziwika ndi dzina lakuti Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo.