Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Amapanga Mapemphero Pamodzi ndi Azipembedzo Zina?

Kodi a Mboni za Yehova Amapanga Mapemphero Pamodzi ndi Azipembedzo Zina?

A Mboni za Yehova timakonda kukambirana Mawu a Mulungu ndi anthu azipembedzo zina. Koma sitipanga mapemphero kapena kulambira nawo limodzi. Baibulo limanena kuti Akhristu oona ali ngati ziwalo zomwe ‘zimalumikizana bwino komanso kuchita zinthu mogwirizana’ ndipo amachita zimenezi chifukwa chokhulupirira mfundo zofanana. (Aefeso 4:16; 1 Akorinto 1:10; Afilipi 2:2) Ndi zoona kuti Akhristu oona amafunika kukondana komanso kukhululukirana. Koma chofunika kwambiri n’kukhulupirira mfundo zoona zochokera m’Baibulo. A Mboni za Yehovafe timaona kuti pakanapanda mfundo zimenezi, bwenzi chikhulupiriro chathu chili chopanda ntchito.​—Aroma 10:2, 3.

Baibulo limanena kuti zipembedzo zikamapanga mapemphero limodzi, zimakhala ngati nyama ziwiri zosiyana zomwe zamangidwa m’goli limodzi. Kuchita zimenezi kungawononge chikhulupiriro cha Mkhristu. (2 Akorinto 6:14-17) N’chifukwa chake Yesu sanalole kuti ophunzira ake azipanga mapemphero ndi a zipembedzo zina. (Mateyu 12:30; Yohane 14:6) Chilamulo cha Mose nachonso chinkaletsa Aisiraeli kuti azipanga mapemphero ndi anthu a mitundu ina. (Ekisodo 34:11-14) Pa nthawi ina, Aisiraeli okhulupirika anakana kuti anthu azipembedzo zina awathandize kumanga nyumba ya Mulungu chifukwa zimenezi zikanachititsa kuti ayambe kugwirizana ndi anthu azipembedzo zina.​—Ezara 4:1-3.

Kodi a Mboni za Yehova amakambirana nkhani za m’Baibulo ndi anthu a m’zipembedzo zina?

Inde. M’chaka cha 2023, tinathera maola 1,791,490,713 tikulankhula ndi anthu a zipembedzo zina zokhudza Mawu a Mulungu. Mofanana ndi mtumwi Paulo, a Mboni za Yehovafe timafuna kucheza ndi “anthu ochuluka” kuti tidziwe zimene amaganiza komanso zimene amakhulupirira. (1 Akorinto 9:19-22) Tikamakambirana ndi anthu, timayesetsa kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo oti tizikhala ‘aulemu kwambiri’ kwa anthu amene timawalalikira.​—1 Petulo 3:15.