Mboni za Yehova Padziko Lonse

Croatia

  • Zagreb, Croatia​—Akugawira magazini a Nsanja ya Olonda mumsewu wotchedwa Ilica Street

  • Ku Rovinj m’dziko la Croatia​—Akuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

  • Mu mzinda wa Zagreb ku Croatia—Akugawira kapepala ka Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?

  • Mu mzinda wa Zagreb ku Croatia—Akulalikira uthenga wopatsa chiyembekezo umene umapezeka m’Baibulo

  • Pula, Croatia​—Akugawira kapepala kakuti Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo? pafupi ndi bwalo lamasewero la ku Rome.

  • M’tawuni ya Kaštel Gomilica, ku Dalmatia, Croatia—Akugawira kabuku kofotokoza Baibulo kwa munthu wogwira ntchito kudoko pa nthawi yake yopuma

Mfundo Zachidule—Croatia

  • 4,038,000—Chiwerengero cha anthu
  • 4,687—Chiwerengero cha Mboni za Yehova
  • 57—Mipingo
  • Pa anthu 870 alionse pali wa Mboni za Yehova m’modzi

NKHANI

A Mboni Anachita Nawo Chionetsero cha Mabuku Pamwambo Wodziwika Kwambiri ku Croatia

A Mboni za Yehova anachita nawo chionetsero chamabuku ku Croatia. Mwambowu unachitika pa 11 mpaka pa 16 November 2014 ndipo unali wa nambala 37. Anthu a m’mayiko osiyanasiyana anapita kukaonetsa mabuku awo.