Pitani ku nkhani yake

Ulendo Wokalalikira kwa Anthu Okhala M’mphepete mwa Mtsinje wa Maroni

Ulendo Wokalalikira kwa Anthu Okhala M’mphepete mwa Mtsinje wa Maroni

 Mosiyana ndi anthu ambiri omwe amakhala m’matauni momwe mumakhala anthu pikitipikiti, anthu ena amakhala m’nkhalango ya Amazon ku South America. Anthuwa ndi a zikhalidwe, mitundu komanso zilankhulo zosiyanasiyana. Choncho mu July 2017, a Mboni za Yehova 13 ananyamuka pa ulendo wokalalikira kwa anthu okhala m’mphepete mwa Mtsinje wa Maroni ndi mitsinje ina yomwe imathera mumtsinjewu chakum’mawa kwake, m’dziko la French Guiana. Cholinga chawo chinali choti akauze anthu okhala m’mphepete mwa mtsinjewu uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo.

Kukonzekera Ulendowu

 Kutatsala mwezi umodzi kuti anyamuke, anthuwa anachita msonkhano wokonzekera ulendo wawo womwe unali wa masiku 12. A Winsley anati: “Tinafufuza za deralo ndi mbiri yake ndipo tinaganizira zimene tingachite pokonzekera ulendowu.” Aliyense anapatsidwa kontena yaikulu yosalowa madzi yoti adzaikemo nsalu yogonera yomangirira mumtengo komanso neti yoteteza ku udzudzu. Kuti akafike kumene akupita, anafunika kukwera ndege ziwiri komanso kuyenda kwa maola ambirimbiri pa maboti aang’ono.

A Claude ndi a Lisette

 Kodi abale ndi alongo omwe anasankhidwa anamva bwanji atavomerezedwa kukagwira nawo ntchitoyi? A Claude ndi a Lisette omwe ali ndi zaka za m’ma 60 anadzipereka kukagwira nawo ntchitoyi. A Claude anati: “Ndinasangalala kwambiri koma ndinali ndi mantha pang’ono. Ndinali nditamva zoti mumtsinjewu muli mathithi ambiri oopsa.” Nawonso a Lisette ankadera nkhawa zinthu zina. Iwo anati: “Sindinkadziwa kuti ndikakwanitsa bwanji kulankhula m’zinenero za anthu a mtundu wa Chiamerindiya.”

 A Mickaël ananenanso zofanana ndi zimenezi ndipo anati: “Sitinkadziwa zambiri zokhudza anthu a mtundu wa Chiwayana, choncho ndinafufuza pa intaneti kuti ndiphunzire mawu ena komanso ndidziwe momwe ndingaperekere moni m’chinenero chimenechi.”

 A Shirley, omwe anayenda limodzi ndi amuna awo a Johann paulendowu analemba mayina a zinenero zomwe zimalankhulidwa ndi anthu omwe amakhala m’mphepete mwa mtsinje wa Maroni. Iwo anati: “Tinapanga dawunilodi mavidiyo a zinenerozi pa webusaiti ya jw.org ndiponso tinapeza kabuku kophunzitsa mawu ofunika kwambiri a m’chinenero cha Chiwayana.”

Anakafika M’dera la Anthu a Mtundu wa Amerindiya

 Lachiwiri pa 4 July, abale ndi alongowa anakwera ndege ku Saint-Laurent du Maroni. Ulendowu unali wopita m’tawuni yaing’ono yotchedwa Maripasoula yomwe ili m’katikati mwa dziko la French Guiana.

 Kwa masiku 4, abalewa analalikira anthu omwe amakhala m’midzi yomwe ili m’mphepete mwa mtsinje wa Maroni. Iwo anakwera maboti aang’ono oyendera injini. Mmodzi mwa abalewa dzina lawo a Roland anati: “Tinaona kuti a Amerindiya ali ndi chidwi chachikulu ndi nkhani za m’Baibulo. Anali ndi mafunso ambiri ndipo ena ankafuna kuti tiziwaphunzitsa Baibulo.”

 M’mudzi wina, a Johann ndi a Shirley anakumana ndi banja lina lachinyamata lomwe wachibale wawo anali atangodzipha kumene. Iwo anati: “Tinawaonetsa vidiyo yakuti, A Native American Finds His Creator, ya pa JW Broadcasting. Banjali linakhudzidwa kwambiri litaonera vidiyoyi. Kenako anatipatsa adiresi ya imelo yawo kuti tizilumikizana nawo.”

 Kenako anafika kumudzi wina wakutali wotchedwa Antécume Pata. Mudziwu uli pafupi ndi mtsinje. Amfumu a m’mudzimu analola kuti a Mboniwa apachike nsalu zawo zogonera zija pamitengo ina yapafupi. Komanso, a Mboniwa anasamba mumtsinje ngati mmene anthu a m’mudzimu amachitira.

 Atachoka kumeneko, abale ndi alongowa anapita m’mudzi wina wotchedwa Twenké ndipo anapeza anthu ali pamaliro. A Éric omwe anatsogolera nawo pokonzekera ulendowu, anati: “Amfumu a m’mudzimu anatilola kuyenda m’makomo kuti tikatonthoze anamfedwa. Amfumuwo ndi banja lawo anayamikira kwambiri malemba omwe tinawawerengera m’Baibulo la Chiwayana. Komanso tinawaonetsa mavidiyo ofotokoza za lonjezo la m’Baibulo lokhudza kuuka kwa akufa.”

Anakafika ku Grand-Santi ndi ku Apatou

 Pa ulendowu, abale ndi alongowa anakafikanso kumunsi kwa mtsinjewu m’tawuni yaing’ono yotchedwa Grand-Santi pa ndege yomwe inayenda maminitsi 30 kuchokera ku Maripasoula. Pa tsiku Lachiwiri ndi Lachitatu, abalewa analalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu a m’deralo. Pa tsiku Lachinayi, a Mboniwa anayenda ulendo winanso kwa maola 5 ndi hafu kudutsa mumtsinje wa Maroni kupita m’mudzi wina wotchedwa Apatou.

Mtsinje wa Maroni ndi nkhalango ya Amazon, pakati pa Maripasoula ndi Grand-Santi

 Kutatsala tsiku limodzi kuti amalize ulendo wawowu, abalewa anayendera anthu a mtundu wa Maruni, omwe amakhala m’midzi ya m’nkhalango. Makolo a anthuwa anagwidwa ukapolo ku Africa n’kutengedwera ku South America pa nthawi yomwe dziko loyandikana nawo la Suriname linkalamulira. A Mboniwo anaitanira aliyense ku msonkhano umene unachitikira munkhalango, mu tenti yaikulu imene anaimanga kuti achitiremo msonkhanowo. A Claude anati: “Mitima yathu inasefukira ndi chimwemwe anthu ambiri atabwera, chifukwa tinali titawaitanira kumsonkhanoko m’mawa wa tsiku lomwelo.” A Karsten, omwe kanali koyamba kuti apite nawo paulendo ngati umenewu, anakamba nkhani ya onse m’chinenero cha Chiokani ya mutu wakuti “Kodi Moyo ndi Wokhawu?” Anthu 91 ochokera m’midzi yosiyanasiyana anabwera pamsonkhanowo.

“Ndife Okonzeka Kupitanso!”

 Pamapeto pa zonse, abale ndi alongowo anabwerera ku Saint-Laurent du Maroni. Onse ankachita kusowa chonena akaganizira mmene anthu a m’mphepete mwa mtsinje aja anawalandirira bwino. Anthuwo analandira mabuku ambiri ndipo anaonera mavidiyo ambiri a Mboni za Yehova.

 A Lisette anati: “Mawu akundisowa oti ndifotokozere chimwemwe chimene ndili nacho chifukwa chopita pa ulendo umenewu.” A Cindy nawonso anavomereza, ndipo anati: “Mwayi wopitanso utapezeka, ndingachonderere kuti ndipite nawo. Kuti munthu amvetse chimwemwe chimene tikumvachi, akungofunika kupita nawo basi!”

 Ulendowu unachititsa anthu ena amene anapita nawo kulakalaka kupitanso. “Ndife okonzeka kupitanso,” anatero a Mickaël. Panopa a Winsley anasamukira ku Saint-Laurent du Maroni. A Claude ndi a Lisette, omwe ali ndi zaka za m’ma 60, anasamukira ku Apatou.