Pitani ku nkhani yake

ERITREA

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Boma la Eritrea likuika m’ndende a Mboni za Yehova komanso anthu ena popanda kuwazenga mlandu ndiponso pa zifukwa zosadziwika. Ena mwa omangidwawa ndi amuna a Mboni za Yehova omwe amakana kulowa usilikali potsatira zomwe amakhulupirira. Komabe, anthu ambiri, kuphatikizapo amayi, ana komanso achikulire, amamangidwa chifukwa chochita zokhudzana ndi chipembedzo kapena pa zifukwa zosadziwika.

Pa 25 October 1994, pulezidenti Afewerki analamula kuti a Mboni si nzikanso za dzikolo chifukwa choti sanamenyere nawo ufulu wodzilamulira mu 1993, komanso amakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira. Komabe akuluakulu a boma la Eritrea asanakhazikitse lamulo loti anthu azilowa usilikali, ankapereka ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali. A Mboni ambiri ankagwira nawo ntchito zimenezi m’maulamuliro osiyanasiyana pa nthawiyo. Ndipotu akuluakulu a bomawo ankapereka masetifiketi kwa anthu akamaliza kugwira ntchito zimenezi ndipo ankawayamikira pa ntchito yomwe agwira. Koma chifukwa cha lamulo limene pulezidenti anaperekalo, asilikali anayamba kuika m’ndende, kuzunza komanso kuchitira nkhanza a Mboni za Yehova, powakakamiza kuti asamatsatire zimene amakhulupirira.

A Mboni Ena Anafera M’ndende

A Mboni okwana 4 anafera m’ndende ku Eritrea ndipo achikulire ena atatu, chifukwa chokhala mozunzika m’ndende, anamwalira atangotulutsidwa kumene.

Mu 2018, a Mboni awiri anafa atawasamutsira kundende ya Mai Serwa. A Habtemichael Tesfamariam anafa ali ndi zaka 76 pa 3 January, ndipo a Habtemichael Mekonen anafa ali ndi zaka 77 pa 6 March. Akuluakulu a boma la Eritrea anaika m’ndende anthu awiriwa mu 2008 popanda kuwazenga mlandu.

Mu 2011 ndi 2012, a Mboni awiri anafa chifukwa chochitiridwa nkhanza zoopsa kundende ya Meitir. A Misghina Gebretinsae, azaka 62, anafa mu July 2011 chifukwa choikidwa m’malo otentha kwambiri olangilako anthu omwe amawatchula kuti “pansi pa nthaka.” Nawonso a Yohannes Haile, azaka 68, anafa pa 16 August 2012, atakhala mozunzika kwambiri m’ndende kwa zaka 4. A Mboni ena atatu achikulire, omwe ndi a Kahsai Mekonnen, a Goitom Gebrekristos ndi a Tsehaye Tesfariami anafa atangotulutsidwa m’ndende ya Meitir chifukwa chokhala mozunzika.

Boma la Eritrea Likunyalanyaza Zimene Mabungwe Omenyera Ufulu wa Anthu Akunena

Boma la Eritrea likupitirizabe kuphwanya mfundo zokhudza ufulu wa anthu zomwe mayiko ena amayendera. Mabungwe akuluakulu omenyera ufulu akhala akudzudzula dziko la Eritrea pa nkhani yophwanya ufulu wa anthu, ndipo akulimbikitsa dzikoli kuti likonze zinthu.

Mu 2014, nthambi ya United Nations yoona za ufulu wa anthu, inalandira lipoti lapadera lokhudza mmene zinthu zilili pa nkhani ya ufulu wa anthu ku Eritrea. Lipotili linalimbikitsa akuluakulu a boma kuti alemekeze ufulu wa anthu “mogwirizana ndi mfundo zimene mayiko ena amayendera” komanso kuti “asamazunze akaidi ndipo azionetsetsa kuti akupereka mankhwala kwa anthu amene akufunikira thandizo. . . ndiponso azitsatira mfundo zimene mayiko ena amayendera, asanamange anthu.” Mu 2015, nthambiyi inalamula boma la Eritrea kuti “lipereke ufulu kwa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.”

M’chaka cha 2016, bungwe lofufuza za ufulu wa anthu ku Eritrea linanena kuti akuluakulu a boma anapalamula “mlandu wophwanya ufulu wa anthu” popeza “ankazunza” a Mboni za Yehova ndiponso anthu ena “chifukwa cha chipembedzo chawo komanso mtundu wawo.”

Mu 2017, bungwe la akatswiri pa nkhani ya ufulu komanso kusamalira ana, linadandaula kuti ngakhale kuti pali malamulo oteteza ufulu, “ana a Mboni za Yehova” sapatsidwa ufulu ndipo amachitiridwa nkhanza. Bungweli linapempha kuti dziko la Eritrea “lizizindikira komanso kupereka Ufulu wa Maganizo, Chikumbumtima komanso Chipembedzo kwa ana mosatengera chipembedzo kapena mtundu wawo.”

Mu 2018, bungwe la ku Africa loona za ufulu wa anthu linanena kuti dziko la Eritrea “likonze mwamsanga vuto lonyalanyaza ufulu wa anthu amene amangidwa, kuphatikizapo . . . a Mboni za Yehova,” ndipo bungweli linapempha kuti anthu afufuze za a Mboni amene anafera m’ndende. Linanenanso kuti dziko la Eritrea liyenera kulola a Mboni za Yehova “kukhalabe ndi ufulu wa unzika m’dzikoli.”

Mu May 2019, Bungwe la United Nations Loona za Ufulu wa Anthu linalimbikitsa dziko la Eritrea kuti lizipereka ufulu wa chipembedzo komanso wokhala ndi zikhulupiriro kwa anthu ndiponso “limasule anthu onse amene anamangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira, kuphatikizapo a Mboni za Yehova.” Bungweli linapemphanso kuti dziko la Eritrea “lizilola anthu kukana usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira ndipo liziwapatsa ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali.”

Sizikudziwika Kuti Adzatulutsidwa Liti

A Paulos Eyasu, a Isaac Mogos ndi a Negede Teklemariam akhala ali m’ndende kuyambira pa 17 September 1994, chifukwa chokana usilikali. Anthu enanso 10, akhala ali m’ndende kwa zaka zoposa 10.

A Mboni ena akhala akuikidwa monga akaidi m’mabokosi akuluakulu achitsulo, pomwe ena akuikidwa m’nyumba zamiyala kapena zachitsulo zomwe hafu yake ili m’nthaka.

Mu July 2017, a Mboni onse am’ndende ya Meitir anasamutsidwa kupita kundende ya Mai Serwa, pafupi ndi mzinda wa Asmara. Pa 30 November 2017, a Mboni onse 13 omwe anali m’ndende ya Sawa, kuphatikizapo a Paulos Eyasu, a Isaac Mogos ndi a Negede Teklemariam, anasamutsidwa kupita kundende ya Mai Serwa.

A Mboni ambiri aamuna akumangidwa ndipo zikuoneka kuti sangatulutsidwe mpaka atamwalira kapena atatsala pang’ono kumwalira. Popeza kuti palibe malamulo kapenanso ndondomeko zomwe anthuwa angatsatire kuti atulutsidwe m’ndende, zili ngati agamulidwa kuti akakhale m’ndende kwa moyo wawo wonse.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 16 April 2020

    A Mboni okwana 52 anaikidwa m’ndende.

  2. 6 March 2018

    A Habtemichael Mekonen, azaka 77, anamwalira atawasamutsira kundende ya Mai Serwa.

  3. 3 January 2018

    A Habtemichael Tesfamariam, azaka 76, anamwalira atawasamutsira kundende ya Mai Serwa.

  4. July 2017

    A Mboni onse am’ndende ya Meitir anawasamutsira kundende ya Mai Serwa pafupi ndi Asmara.

  5. 25 July 2014

    A Mboni ambiri amene anamangidwa pa 14 April anamasulidwa, koma anthu 20 amene anamangidwa pa 27 April sanamasulidwe.

  6. 27 April 2014

    A Mboni 31 anamangidwa atasonkhana n’kumaphunzira Baibulo.

  7. 14 April 2014

    A Mboni oposa 90 anamangidwa akuchita mwambo wapachaka wokumbukira imfa ya Khristu.

  8. 16 August 2012

    A Yohannes Haile, azaka 68, anamwalira chifukwa chokhala mozunzika m’ndende.

  9. July 2011

    A Misghina Gebretinsae, azaka 62, anamwalira chifukwa chokhala mozunzika m’ndende.

  10. 28 June 2009

    Apolisi analowa m’nyumba ya a Mboni pa nthawi imene ankachita msonkhano wa chipembedzo ndipo anamanga a Mboni onse 23 amene anali pamalowo, azaka zoyambira ziwiri mpaka 80.

  11. 28 April 2009

    Apolisi anasamutsira a Mboni za Yehova onse kundende ya Meitir, kupatulapo munthu mmodzi.

  12. 8 July 2008

    Apolisi anayamba kuyenda nyumba ndi nyumba komanso malo ogwirirako ntchito posakasaka a Mboni ndipo anamanga anthu 24, omwe ambiri mwa iwo anali oti amapezera mabanja awo zofunika pa moyo.

  13. May 2002

    Boma linaletsa magulu achipembedzo onse amene sanalole kutsogoleredwa ndi zipembedzo 4, zimene bomalo linavomereza.

  14. 25 October 1994

    Pulezidenti anapereka lamulo lonena kuti a Mboni za Yehova si nzikanso za Eritrea komanso kuti alibe ufulu monga nzika zadzikolo.

  15. 17 September 1994

    A Paulos Eyasu, a Isaac Mogos ndi a Negede Teklemariam anamangidwa popanda kuimbidwa mlandu uliwonse ndipo adakali m’ndende mpaka pano.

  16. M’ma 1940

    Magulu oyambirira a Mboni za Yehova anakhazikitsidwa ku Eritrea.