Pitani ku nkhani yake

Kodi Munthu Wachuma Komanso Lazaro Anali Ndani?

Kodi Munthu Wachuma Komanso Lazaro Anali Ndani?

Yankho la M’Baibulo

 Munkhani ina yomwe Yesu ananena, anatchula za munthu wina wolemera komanso za Lazaro. (Luka 16:19-31) Munkhaniyo, anthu awiriwa ankaimira magulu awiri a anthu omwe ndi: (1) atsogoleri achipembedzo chachiyuda omwe anali onyada, komanso (2) anthu wamba omwe anali odzichepetsa ndipo anamvetsera uthenga wa Yesu.

Zimene zili munkhaniyi

 Kodi Yesu ananena zotani zokhudza munthu wolemera ndi Lazaro?

 Mu Luka chaputala 16, Yesu ananena za anthu awiri omwe zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wawo.

 Mwachidule izi ndi zomwe Yesu ananena: Munthu wina wolemera ankakhala moyo wofewa. Ndipo panalinso munthu wina wopemphapempha dzina lake Lazaro, ankakhala pageti la munthu wina wolemera ndi cholinga choti azipatsidwa nyenyeswa za chakudya zomwe zinkagwa patebulo la munthu wolemera uja. Patapita nthawi, Lazaro anamwalira ndipo angelo anamutenga kupita naye kwa Abulahamu. Kenako munthu wolemera uja nayenso anamwalira n’kuikidwa m’manda. Munkhaniyi, ngakhale kuti anthu awiriwa anamwalira, koma akufotokozedwa ngati kuti ankadziwa zomwe zikuchitika. Tikutero chifukwa nkhaniyi imafotokoza kuti munthu wolemerayu atamwalira, anayamba kuzunzika m’moto wolilima ndipo ankapempha Abulahamu kuti atume Lazaro kuti amuziziritseko lilime pomudonthezera madzi akuchala. Koma Abulahamu anakana zomwe munthu wolemerayu anamupempha ponena kuti tsopano zochitika pa moyo wa anthu awiriwo zasinthiratu. Abulahamu ananenanso kuti pakati pa anthuwo panali phompho lalikulu moti sizikanakhala zotheka kuwoloka phompholo kupita mbali ina.

 Kodi nkhaniyi inachitikadi?

 Ayi. Nkhaniyi linali fanizo lomwe Yesu ananena pofuna kuphunzitsa mfundo inayake. Akatswiri a Baibulo nawonso amavomereza kuti nkhaniyi ndi fanizo chabe. Mwachitsanzo, mawu a pakamutu m’Baibulo la Luther’s la mu 1912, amanena kuti nkhaniyi ndi fanizo. Komanso mawu am’munsi m’Baibulo la Katolika la Jerusalem, amafotokoza za nkhaniyi kuti “linali fanizo lofotokozedwa ngati nkhani koma sinkhani yonena za anthu enieni omwe anakhalako m’mbuyomu.”

 Kodi m’fanizoli Yesu ankaphunzitsa zomwe zimachitikira anthu akafa? Kodi ankatanthauza kuti anthu ena akamwalira amakazunzidwa kumoto, komanso kuti Abulahamu ndi Lazaro ali kumwamba? Mfundo zingapo zomwe zili m’munsimu, zikusonyeza kuti zimenezi sizingakhale zoona.

 Mwachitsanzo:

  •   Ngati zilidi zoona kuti munthu wolemera uja anali m’moto wolilima, kodi madzi ongotengeredwa kunsonga ya chala cha Lazaro sakanauma ndi motowo?

  •   Ngati zikanathekadi kumudonthezera madziwo, kodi akanakhaladi madzi okwanira kuthetsera ludzu munthu yemwe ali m’moto weniweni?

  •   Kodi zikanatheka bwanji kuti Abulahamu akhale ali kumwamba, pomwe panthawi imene Yesu ankafotokoza fanizoli, ananena momveka bwino kuti “palibe munthu amene anakwera kumwamba?”​—Yohane 3:13.

 Kodi nkhaniyi ikusonyeza kuti ndi zoona kuti Mulungu amawotcha anthu kumoto?

 Ayi. Ngakhale kuti nkhaniyi linali fanizo chabe, anthu ena amati nkhaniyi imasonyeza kuti anthu abwino amapita kumwamba ndipo anthu oipa amakazunzidwa ku moto wa ku gehena. a

 Kodi maganizo amenewa ndi omveka? Ayi.

 Chiphunzitso chakuti anthu oipa amakawotchedwa kumoto, chimatsutsana ndi zomwe Baibulo limanena pa nkhani ya zomwe zimachitika munthu akamwalira. Mwachitsanzo, Baibulo silinena kuti anthu abwino onse akamwalira amakasangalala kumwamba komanso kuti anthu oipa amakazunzidwa kumoto. Koma limanena kuti: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.”​—Mlaliki 9:5.

 Kodi nkhaniyi imatanthauza chiyani?

 Nkhaniyi inkasonyeza kuti zochitika pa moyo wa magulu awiri a anthu enaake zinkayembekezeka kusintha kwambiri.

 N’zodziwikiratu kuti munthu wolemera wotchulidwa m’fanizoli akuimira atsogoleri achipembedzo chachiyuda omwe anali “okonda kwambiri ndalama.” (Luka 16:14) Atsogoleriwa anamva zomwe Yesu anaphunzitsa koma sanagwirizane ndi uthenga wake. Komanso atsogoleriwa ankanyoza anthu wamba.​—Yohane 7:49.

 Lazaro akuimira anthu wamba omwe ankanyozedwa ndi atsogoleri achipembedzo chachiyuda. Komabe anthuwa anamvetsera ndi kulandira uthenga wa Yesu.

 Zochitika pa moyo wa magulu awiriwa zinasintha kwambiri.

  •   Atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankaganiza kuti akudalitsidwa ndi Mulungu. Kenako anakhala ngati afa pamene Mulungu anawakana limodzi ndi kapembedzedwe kawo chifukwa choti anakana kulandira uthenga wa Yesu. Ndipo atsogoleriwa ankazunzika kapena kuti kusowa mtendere ndi uthenga umene Yesu ndi ophunzira ake ankalalikira.​—Mateyu 23:29, 30; Machitidwe 5:29-33.

  •   Anthu wamba omwe ankanyalanyazidwa ndi atsogoleri achipembedzo kwa nthawi yaitali, tsopano anayamba kudalitsidwa. Ambiri analandira uthenga wa m’Malemba womwe Yesu anaphunzitsa ndipo anapindula nawo kwambiri. Tsopano anali ndi mwayi wosangalala kwamuyaya ndi madalitso ochokera kwa Mulungu.​—Yohane 17:3.

a Mabaibulo ena amanena kuti munthu wolemerayu atamwalira, anapita ku “Gehena.” Komabe mawu a Chigiriki oyambirira omwe anagwiritsidwa ntchito pa Luka 16:23 ndi akuti “Hade” ndipo amatanthauza manda a anthu onse.