Pitani ku nkhani yake

Kodi Yesu Anaukitsidwa ndi Thupi Lotani?

Kodi Yesu Anaukitsidwa ndi Thupi Lotani?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limanena kuti Yesu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.”​—1 Petulo 3:18; Machitidwe 13:34; 1 Akorinto 15:45; 2 Akorinto 5:16.

 Ngakhalenso Yesu anasonyeza kuti sadzaukitsidwa ndi thupi limene anali nalo. Ananena kuti: ‘Ndidzapereka mnofu wangawu kuti dzikoli lipeze moyo.’ (Yohane 6:51; Mateyu 20:28) Choncho ngati Yesu akanaukitsidwa ndi thupi lakelo, zikanakhala ngati sanapereke nsembe ya dipo. Koma izi si zimene zinachitika chifukwa Baibulo limanena kuti Yesu anapereka thupi ndiponso magazi ake nsembe “kamodzi kokha.”—Aheberi 9:11, 12.

Ngati Yesu anaukitsidwa ndi thupi lauzimu, ndiye zinatheka bwanji kuti ophunzira ake amuone?

  •  Nthawi zina angelo amatha kudzichititsa kuti aoneke ngati anthu. Mwachitsanzo, kale angelo ena anaonekera kwa anthu ndipo anadya ndiponso kumwa limodzi ndi anthuwo. (Genesis 18:1-8; 19:1-3) Komabe anali adakali angelo moti kenako anasinthanso n’kupita kumwamba.​—Oweruza 13:15-21.

  •  Nayenso Yesu ataukitsidwa anadzichititsa kuti aoneke ngati munthu kwa kanthawi. Koma popeza anali ndi thupi ngati la mngelo, Yesu ankatha kuonekera kwa anthu ndiponso kusowa mosadziwika bwino. (Luka 24:31; Yohane 20:19, 26) Ngakhale ndi choncho, sikuti nthawi iliyonse imene ankaonekera kwa anthu ankaoneka mofanana. N’chifukwa chake ophunzira ake ankamuzindikira chifukwa cha zimene ankanena kapena kuchita.​—Luka 24:30, 31, 35; Yohane 20:14-16; 21:6, 7.

  •  Pa nthawi imene Yesu ankaonekera kwa mtumwi Tomasi, ankaoneka ngati munthu wokhala ndi mabala. Anachita zimenezi kuti athandize Tomasi chifukwa poyamba ankakayikira zoti Yesu waukitsidwadi.​—Yohane 20:24-29.