Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Genesis 1:1​—“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi”

Genesis 1:1​—“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi”

 “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”​—Genesis 1:1, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.”​—Genesis 1:1, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Genesis 1:1

 Mawu oyamba a m’Baibulowa amanena mfundo ziwiri zoona zomwe n’zofunika. Choyamba, amanena kuti “kumwamba ndi dziko lapansi,” kapena kuti zinthu zonse zooneka ndi maso m’chilengedwe, zinali ndi chiyambi. Chachiwiri, zonsezi zinalengedwa ndi Mulungu.​—Chivumbulutso 4:11.

 Baibulo silinena nthawi kapena njira imene Mulungu analengera zinthuzi. Koma limanena kuti analenga zinthuzi pogwiritsa ntchito ‘mphamvu zake zochuluka komanso zoopsa, ndiponso . . . mphamvu [zake] zambiri zochitira zinthu.’​—Yesaya 40:26.

 Mawu oti “kulenga” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi amene amagwiritsidwa ntchito ponena za zinthu zimene Mulungu yekha amachita. a Ndipotu m’Baibulo Yehova b Mulungu yekha ndi amene amatchulidwa kuti Mlengi.​—Yesaya 42:5; 45:18.

Nkhani yonse ya Genesis 1:1Genesis 1:1

 Vesi loyamba la m’Baibuloli ndi mawu oyamba a nkhani yofotokoza za kulengedwa kwa zinthu mu Genesis chaputala 1 ndi 2. Kuyambira pa Genesis 1:1 mpaka 2:4, Baibulo limafotokoza mwachidule zimene Mulungu anachita polenga dziko lapansi ndi zinthu zonse zapadzikoli, kuphatikizapo mwamuna ndi mkazi oyamba. Baibulo litafotokoza mwachidule zimenezi, limafotokoza mwatsatanetsatane kulengedwa kwa mwamuna ndi mkazi.​—Genesis 2:7-25.

 Buku la Genesis limafotokoza kuti Mulungu analenga zinthu pa “masiku” 6. Masiku amenewa sanali a maola 24 koma a nthawi yosadziwika. Sikuti mawu oti “tsiku” nthawi zonse amanena za maola 24 basi. Mwachitsanzo, lemba la Genesis 2:4 limagwiritsa ntchito mawu oti “tsiku” kutanthauza “nthawi.” Limanena za ‘tsiku’ limene Mulungu anapanga zinthu zonse zimene anazilenga m’masiku 6.

Maganizo Olakwika Okhudza Genesis 1:1

 Maganizo olakwika: Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi zaka masauzande angapo zapitazo.

 Zoona zake: Baibulo silinena nthawi imene zinthuzi zinalengedwa. Mawu a pa Genesis 1:1 sasemphana ndi zimene asayansi amanena kuti kumwamba ndi dziko lapansi zakhalapo kwa zaka mabiliyoni angapo. c

 Maganizo olakwika: Lemba la Genesis 1:1 limasonyeza kuti Mulungu ndi Utatu, kapena kuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi chifukwa mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti “Mulungu” m’vesili sanena za Mulungu mmodzi yekha.

 Zoona zake: Mawu oti “Mulungu” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi akuti ’Elo·himʹ, omwe sanena za mmodzi yekha chifukwa amasonyeza ukulu kapena kulemekezeka. Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo amanena kuti mawu oti ’Elo·himʹ omwe anagwiritsidwa ntchito pa Genesis 1:1 “nthawi zonse amakhala ndi verebu yonena za munthu mmodzi kusonyeza kuti mawuwo sakunena za milungu ingapo koma ndi olemekeza basi.​—New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Voliyumu 6, tsamba 272.

Werengani Genesis chaputala 1, mawu am’munsi ndi malifalensi ake.

a Ponena za mawu amenewa, Baibulo lina lophunzirira limati: “Verebu ya Chiheberi yakuti bara’, yotanthauza kuti ‘kulenga,’ sigwiritsidwa ntchito pofotokoza zimene munthu akuchita. Choncho mawuwa amanena za ntchito imene Mulungu yekha amagwira.”​—HCSB Study Bible, tsamba 7.

b Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.

c Ponena za mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti “pa chiyambi,” buku lina lofotokoza Baibulo limati: “Mawuwa sasonyeza kuti nthawiyo inali yaitali bwanji.”​—The Expositor’s Bible Commentary, Revised Edition, Voliyumu 1, tsamba 51.