Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

WEBUSAITI YA JW.ORG

Onerani Mavidiyo pa JW.ORG

Onerani Mavidiyo pa JW.ORG

Onerani vidiyo kapena mavidiyo onse omwe akupezeka pagawo limodzi. Imitsani, ibwezeni kapena ifulumizitseni.

 Pezani Ndiponso Onerani Vidiyo

Kuti muone mavidiyo onse omwe alipo, pitani pa LAIBULALE > MAVIDIYO ndipo muonanso mavidiyo omwe anajambulidwa kuchokera musitudiyo yathu ya JW Broadcasting.

Sankhani gawo la vidiyo.

Gawo lililonse lili ndi mutu wake ndipo muli mavidiyo osiyanasiyana. Kuti muone mavidiyo ena omwe akupezeka m’gawo linalake, dinani chizindikiro cholozera kumanzere kapena kumanja pagawolo kapena dinani batani lakuti Onani Zonse.

Onerani kapena patsani ena vidiyo potsatira njira izi:

  • Dinani batani lakuti Onerani vidiyo.

  • Dinani batani lakuti Pangani Dawunilodi kuti musunge vidiyo mu kompyuta kapena m’chipangizo chanu cham’manja. (Dziwani izi: Zipangizo zina zam’manja zimafunika kuti zikhale kaye ndi pulogalamu yapadera yopangira dawunilodi zinthu. Ngati munaika pulogalamu ya JW Library m’chipangizo chanu cham’manja, tikukulimbikitsani kuti muziigwiritsa ntchito pa mavidiyo omwe mukufuna kupanga dawunilodi komanso kuonera mukakhala kuti simunalowe pa intaneti.)

  • Dinani batani lakuti Patsani Ena kuti mutumize linki ya vidiyo kwa munthu wina. Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Share a Link to an Article, a Video, or a Publication.”

  • Kuti muonere vidiyo m’chinenero china, sankhani chinenero chomwe mukufuna pam’ndandanda wa Zinenero kumanja kwa mutu wa vidiyo womwe walembedwa m’munsi.

 Onerani Mavidiyo Onse M’gawo kapena M’kagulu

Dinani batani lakuti Shuffle lomwe lili pagawo la vidiyo kuti muonere mavidiyo onse popanda kutsatira mmene anawasanjira.

Pali njira ziwiri zimene mungatsatire kuti muonere mavidiyo onse omwe ali m’gawo kapena m’kagulu.

  • Dinani batani lakuti Onani Zonse limene lili m’kagulu kuti muonere mavidiyo onse omwe ali m’kagulu potengera mmene anawasanjira.

  • Dinani batani lakuti Shuffle lomwe lili m’kagulu kuti muonere mavidiyo onse omwe ali m’kaguluko popanda kutsatira mmene anawasanjira.

Dziwani izi: Mavidiyo onse omwe ali m’gawo kapena m’kagulu kamene mwasankha akamaliza kusewera, asiya kuoneka.

 Sinthani Zina ndi Zina Mukamaonera Vidiyo

Sinthani zina ndi zina mukamaonera vidiyo potsatira izi:

  • Dinani batani lakuti Kulitsani Vidiyo pakabokosi kamene kakuonetsa vidiyo kuti mukulitse kapena kuchepetsa vidiyo.

  • Dinani batani lakuti Imitsani kuti muimitse vidiyo.

  • Dinani batani lakuti Onerani Vidiyo kuti mupitirize kuonera.

  • Pititsani kutsogolo kapena kumbuyo Kachizindikiro Kosonyeza Mmene Vidiyo Ikuyendera kuti muonere mbali inayake.

  • Dinani batani la Voliyumu ndipo sunthani m’mwamba kapena m’munsi kuti musinthe voliyumu. Pachipangizo chanu cham’manja, mukhozanso kudina batani la voliyumu m’mbali mwa chipangizocho.

 Sinthani Zomwe Mukufuna Zokhudza Vidiyo

Dinani batani losonyeza chizindikiro cha Settings kenako sankhani kaonekedwe komwe mukufuna. (Dziwani izi: Mapulogalamu ena otsegulira zinthu pa intaneti alibe mbali imeneyi.)

Kodi manambalawo akutanthauza chiyani? Nambala yaikulu ikuimira vidiyo yooneka bwino kwambiri. Ndiyeno kuti ioneke, imafunikira intaneti yachangu. Sankhani nambala imene ikugwira ntchito bwino potengera ndi mmene intaneti yanu ikufulumirira, kukula kwa sikirini komanso ndalama zanu.

Mfundo zotsatirazi zikufotokoza zokhudza kaonekedwe ka vidiyo:

Kaonekedwe

Tanthauzo lake

240p

Yosaoneka bwino kwambiri. Imakhala bwino pazipangizo zam’manja zokhala ndi sikirini yaing’ono.

360p

Yosaoneka bwino kwenikweni. Imakhala bwino pazipangizo zam’manja zokhala ndi sikirini yaing’ono.

480p

Yooneka bwino mwachikatikati. Imakhala bwino pamatabuleti, masikirini a kompyuta, ndi ma TV ooneka bwinoko.

720p

Yooneka bwino kwambiri (HD). Imakhala bwino pamasikirini a kompyuta okhala ndi kaonekedwe kuyambira 1024 x 768 kapena ma HDTV okhala ndi kaonekedwe koyambira 1280 x 720.

N’chifukwa chiyani mukufunika kusintha kaonekedwe? Ngati intaneti yanu isakufulumira, mukamaonera vidiyo imayamba kuimaima ndiye mungachite bwino kusankha kaonekedwe kocheperapo. Sankhani nambala ya kaonekedwe komwe kakukhala bwino pa kompyuta kapena chipangizo chanu. Mukhozanso kusankha kaonekedwe kocheperapo kuti musagwiritse ntchito ndalama zambiri za intaneti.

Dinani batani lakuti Onetsani Mawu Ake kuti muone kapena kuchotsa mawu a m’chinenero chimene chikumveka muvidiyoyo.

Dziwani izi: Si mavidiyo onse omwe amaonetsa mawu ake.