Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | MUNGACITE CIANI KUTI MUZISANGALALA NDI NCHITO YANU?

Kodi Kugwila Nchito Mwamphamvu N’kofunikadi?

Kodi Kugwila Nchito Mwamphamvu N’kofunikadi?

Alex, amene amagwila nchito pa kampani yonyamula katundu, akuoneka wotopa pamene akunyamula katoni ina ya katundu kuika m’galimoto. Iye akudzifunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani ndikuvutika ndi nchito yaukapolo imeneyi? Ndi liti pamene ndidzapeza nchito yabwino? Zingakhale bwino nditangosiya kugwila nchitoyi.’

Monga Alex amene tamuchula pamwambapa, anthu ambili safuna kugwila nchito yolemetsa. Aaron, amene amagwila nchito yokonza magalimoto, anati: “Anthu ambili amaona kuti kugwila nchito yamanja kumawacotsela ulemu. Iwo amaganiza kuti adzaleka kugwila nchito yamanja akadzapeza nchito ina yabwino.”

N’cifukwa ciani anthu ambili safuna kugwila nchito mwamphamvu? Mwina io amatengela maganizo a anthu ofalitsa nkhani pa wailesi, pa TV, ndi m’manyuzipepala. Ofalitsa nkhani amenewa amaonetsa kuti anthu olemela amene sagwila nchito zolemetsa ndiwo ali ndi “umoyo wabwino.” Matthew, amene amagwila nchito yokonza zinthu zoonongeka, anati: “Anthu amaganiza kuti pamene ugwila nchito kwambili kuti upeze zofunikila pa umoyo, m’pamenenso umapeza zocepa.” Komanso Shane, amene amagwila nchito yosamalila panyumba anakamba zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Masiku ano anthu safuna kugwila nchito tsiku lonse kuti apeze zofunikila pa umoyo.”

Ngakhale ndi conco, pali anthu ambili amene amagwila nchito mwamphamvu koma amasangalala ndi nchito yao. Daniel, amene ali ndi zaka 25 ndipo amagwila nchito yomangamanga, anati: “Ndiganiza kuti kugwila nchito mwamphamvu n’kosangalatsa kwambili, makamaka munthu akakhala ndi zolinga zabwino zogwilila nchitoyo. Nayenso Andre, amene ali ndi zaka 23, anakamba zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Ndimakhulupilila kuti munthu afunika kugwila nchito mwamphamvu kuti akhale wacimwemwe. Kugwila nchito yocepa sikubweletsa cimwemwe cokhalitsa koma kumapangitsa munthu kukhala ndi umoyo wosasangalala.”

N’ciani cinathandiza anthu monga Daniel ndi Andre kukhala ndi maganizo oyenela pa nchito? Kunena mwacidule, cinawathandiza ndi mfundo za m’Baibulo zimene amagwilitsila nchito pa umoyo wao. Baibulo sililetsa anthu kugwila nchito mwamphamvu. M’malomwake limalimbikitsa anthu kugwila nchito mwakhama. Baibulo silimangotiuza kuti tizigwila nchito koma limatiuzanso zimene tiyenela kucita kuti tizisangalala ndi nchito yathu.

Ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusangalala ndi nchito yanu? Tikupemphani kuti muŵelenge nkhani yotsatila kuti mumve zina mwa mfundo zimenezi.