Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tikondanadi

Tikondanadi

Daunilodi:

  1. 1. Cikwati ni mphatso yabwino

    Yocokeladi kwa Yehova.

    Pamene mwamuna na mkazi

    Akondana amakondwela (O)

    (KOLASI)

    Atate Yehova ni Mulungu wathu;

    Ngati alimo

    Mu banja

    Tidzasangalaladi iwe na ine.

    Nimakondwa kudziŵa kuti

    Tikondanadi—

    (O) Tikondana.

  2. 2. Tingakumane

    Na mavuto na mayeselo.

    Koma ise sitidzasiyana.

    Tidzakondanabe mpaka imfa—

    Tidzakondana.

    (KOLASI)

    Atate Yehova ni Mulungu wathu;

    Ngati alimo

    Mu banja

    Tidzasangalaladi iwe na ine.

    Nimakondwa kudziŵa kuti

    Tikondanadi—

    (O) Tikondana

    (BILIJI)

    Ndise thupi limodzi. (Sitidzasiyana)

    Yehova wanipatsa wonikonda. (Nikukonda.)

    Cikondi coona sicimasila;

    Ngakhale m’mavuto cipilila zonse.

    Ndiwe mkazi wabwino, woposa onse!

    Sinidzakaleka kukukonda.

  3. 3. Nifuna iwe udziŵe

    Nikukondadi na mtima wonse.

    Niyamika M’lungu pokupeza.

    Nakuti ndiwe mkazi wanga.

    Ndiwe wanga.

    (KOLASI)

    Atate Yehova ni Mulungu wathu;

    Ngati alimo

    (O) mu banja

    Tidzasangalaladi iwe na ine.

    Nimakondwa kudziŵa kuti

    Tikondanadi—

    Tikondana (O)

    Nimakondwa kudziŵa kuti

    Tikondanadi.