Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 100

Paulo ndi Timoteyo

Paulo ndi Timoteyo

Timoteyo anali m’bale wachinyamata mumpingo wa ku Lusitara. Bambo ake anali Mgiriki ndipo mayi ake anali Myuda. Mayi ake anali a Yunike ndipo agogo ake anali a Loisi. Timoteyo anaphunzira Mawu a Mulungu kuyambira ali wakhanda ndipo amene anamuphunzitsa ndi mayi ake ndi agogo ake.

Paulo atafika ku Lusitara pa ulendo wake wachiwiri, anazindikira kuti Timoteyo amakonda kwambiri abale ndipo ali ndi mtima wofuna kuwathandiza. Choncho Paulo anapempha Timoteyo kuti ayende naye. Paulo anaphunzitsa Timoteyo kulalikira komanso kuphunzitsa uthenga wabwino mwaluso.

Mzimu woyera unkathandiza Paulo ndi Timoteyo kulikonse kumene ankapita. Tsiku lina usiku, Paulo anaona masomphenya. Anaona munthu akumuuza kuti apite ku Makedoniya kukawathandiza. Choncho Paulo, Timoteyo, Sila ndi anthu ena anapita kukalalikira ku Makedoniya ndipo anakhazikitsa mipingo.

Atafika mumzinda wa Tesalonika, anthu ambiri anakhala Akhristu. Koma Ayuda ena ankachitira nsanje Paulo ndi anzakewo. Iwo anakopa gulu la anthu n’kutenga Paulo ndi anzakewo kupita nawo kwa olamulira a mzinda. Anthuwo ankafuula kuti: ‘Anthu awa ndi adani a boma la Roma!’ Apa moyo wa Paulo ndi Timoteyo unali pa ngozi choncho kutangoda iwo anathawira ku Bereya.

Anthu a ku Bereya anali ofunitsitsa kumvetsera uthenga wabwino ndipo Agiriki ndi Ayuda omwe, anakhala okhulupirira. Koma Ayuda ochokera ku Tesalonika atabwera anayambitsa chipolowe. Zitatero Paulo anachoka kupita ku Atene. Timoteyo ndi Sila anatsala ku Bereya komweko kuti azilimbikitsa abale. Patapita nthawi, Paulo anatumiza Timoteyo ku Tesalonika kuti akalimbikitse abale kumeneko, omwe ankazunzidwa kwambiri. Kenako anamutumizanso kumipingo ina kuti akalimbikitse abale ndi alongo.

Paulo anauza Timoteyo kuti: ‘Amene akufuna kutumikira Yehova adzazunzidwa.’ Timoteyo anazunzidwa ndiponso kutsekeredwa m’ndende chifukwa chotumikira Mulungu. Iye ankaona kuti umenewu unali mwayi wake wosonyeza kuti ndi wokhulupirika.

Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: ‘Ndakutumizirani Timoteyo kuti adzakuphunzitseni zoyenera kuchita potumikira Mulungu komanso polalikira.’ Paulo anachita zimenezi chifukwa chakuti Timoteyo anali wodalirika. Iwo ankagwirizana kwambiri ndipo anatumikira Mulungu limodzi kwa zaka zambiri.

“Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima. Pakuti ena onse akungofuna za iwo eni, osati za Khristu Yesu.”—Afilipi 2:20, 21