Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MAVUTO A M’DZIKOLI

4 | Muziteteza Chiyembekezo Chanu

4 | Muziteteza Chiyembekezo Chanu

CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA

Nkhawa zobwera chifukwa cha mavuto a m’dzikoli zingakhudze anthu m’njira zosiyanasiyana. Anthu ambiri amene amakhudzidwa ndi zimenezi amakhala opanda chiyembekezo ndipo amati zinthu sizingasinthe. Kodi ndiye amachita zotani?

  • Ena safuna n’komwe kuganizira zam’tsogolo.

  • Ena amamwa mowa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kuti aiwale mavuto.

  • Enanso amaona kuti kuli bwino kungofa ndipo amafunsa kuti, “Moyo uli ndi phindu lanji?”

Zimene Muyenera Kudziwa

  • Mavuto ena amene mumakumana nawo akhoza kukhala a kanthawi ndipo akhoza kutha nthawi iliyonse.

  • Ngakhale zitakhala kuti mavuto amene mukumana nawo sangasinthe, pali zina zimene mungachite kuti mupirire.

  • Baibulo limatipatsa chiyembekezo chodalirika. Limati mavuto onse amene timakumana nawo panopa adzatha.

Zimene Mungachite Panopa

Baibulo limanena kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”​—Mateyu 6:34.

Muzithana ndi nkhawa za tsiku lililonse palokha. Musamadere nkhawa zamawa mpaka kufika polephera kuchita zinthu zofunika zalero.

Kumangodera nkhawa zinthu zoipa zimene mukuona ngati zichitika, kungangokuwonjezerani nkhawa ndipo kungakuchititseni kuti muzikayikira kuti m’tsogolo mavuto adzatha.

Baibulo Limapereka Chiyembekezo Chodalirika

Wolemba masalimo wina anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, ndi kuwala kounikira njira yanga.” (Salimo 119:105) Kodi Baibulo lomwe ndi mawu a Mulungu limachita bwanji zimenezi?

Tikamayenda usiku, nyale imatithandiza kuona pamene tingaponde. Mofananamo, m’Baibulo muli malangizo anzeru omwe angatithandize tikamapanga zosankha zovuta.

Kuwala kumatithandiza kuti tione kumene tikupita. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limatithandiza kudziwa zinthu zimene zichitike m’tsogolo.

Baibulo ndi Buku lopatulika lomwe limafotokoza mmene moyo wamunthu unayambira. Limafotokozanso chiyembekezo chodalirika cha zomwe zichitike m’tsogolo. Limafotokoza: