Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MAVUTO A M’DZIKOLI

3 | Muziteteza Ubwenzi Wanu ndi Anzanu

3 | Muziteteza Ubwenzi Wanu ndi Anzanu

CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA

Mavuto a m’dzikoli akumachititsa kuti anthu ambiri azikhala ndi nkhawa. Chifukwa cha zimenezi, mosadziwa, anthu ena akumachita zinthu zosonyeza kuti sakonda anzawo.

  • Anthu ena amadzipatula kuti azichita zinthu paokha.

  • Anthu ena apabanja sakumachedwa kuyambana.

  • Chidwi cha makolo ena pa ana awo chachepa, pomwe ena sakumaganizira n’komwe nkhawa zimene ana awo amakhala nazo.

Zimene Muyenera Kudziwa

  • Kukhala ndi anzathu n’kwabwino, chifukwa amatithandiza kukhala ndi moyo wabwino komanso amatilimbikitsa makamaka pa nthawi imene takumana ndi mavuto.

  • Nkhawa zimene zimabwera chifukwa cha mavuto a m’dzikoli, zingachititse kuti musamagwirizane m’banja mwanu m’njira zimene simunkaziganizira.

  • Ana anu akamamvetsera pa wailesi kapena kuonera nkhani zoopsa pa TV, zingawasokoneze kwambiri.

Zimene Mungachite Panopa

Baibulo limanena kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”​—Miyambo 17:17.

Ganizirani za munthu amene angakuthandizeni komanso amene angakupatseni malangizo othandiza kenako m’pempheni. Kudziwa kuti winawake amakuganizirani kungakulimbikitseni kupirira mavuto amene mumakumana nawo.