Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 3

Muziwaphunzitsa Kukhala Opirira

Muziwaphunzitsa Kukhala Opirira

KODI MUNTHU WOPIRIRA AMATANI?

Munthu wopirira ndi amene amatha kuyambiranso kuchita zinthu ngati kale, ngakhale kuti anakumana ndi zovuta zinazake. Munthu amaphunzira khalidweli akakumana ndi mavuto mobwerezabwereza. Monga mmene zilili kuti mwana sangaphunzire kuyenda popanda kugwa, n’zosathekanso kuti mwana wanu azichita zinthu bwinobwino popanda kulakwitsa chinachake.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUPIRIRA N’KOFUNIKA?

Ana ena amakhumudwa akalephera kuchita zinazake, akakumana ndi mavuto kapena akadzudzulidwa pa zimene alakwitsa. Ndipo ena amangotayiratu mtima. Komabe anawo amafunika kudziwa mfundo zofunika izi:

  • Sizingatheke kuti zinthu zonse zizingoyenda mmene tikufunira.​—Yakobo 3:2.

  • Aliyense amakumana ndi mavuto pa moyo wake.​—Mlaliki 9:11.

  • Tikauzidwa zimene tikulephera m’pamene timaphunzirapo kanthu.​—Miyambo 9:9.

Ana akakhala opirira amalimba mtima n’kuthana ndi vuto lililonse limene angakumane nalo.

MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKHALA OPIRIRA?

Ngati alephera kusukulu.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.”—Miyambo 24:16.

Muzithandiza mwana wanu kuti asamataye mtima zinthu zikavuta. Mwachitsanzo akalephera mayeso, akhoza kumangodziona kuti ndi wolephera pa chilichonse.

Kuti mum’thandize muyenera kumuuza zimene angachite kuti asadzalepherenso nthawi ina. Mukamachita zimenezi mungamuthandize kuti azitha kulimbana ndi mavuto ake m’malo mogwa ulesi.

Komabe, pomuthandizapo musamukonzere zinthu zimene walakwitsazo. M’malomwake muzimusiya kuti apeze yekha njira yothetsera vutolo. Mwachitsanzo, mungamufunse kuti, “Kodi ungatani kuti uyambe kukhoza bwino phunziroli?”

Akakumana ndi mavuto.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”​—Yakobo 4:14.

Moyo ndi wosapanganika. Munthu amene ndi wolemera lero, akhoza kusauka mawa ndipo munthu amene ali wathanzi lero, akhoza kudwala mawa. Baibulo limati: “Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo.” Limapitirizanso kuti: “Chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”​—Mlaliki 9:11.

Monga kholo, mungachite zonse zimene mungathe kuti muteteze mwana wanu ku zinthu zoipa. Koma zoona zake n’zakuti n’zosatheka kuteteza mwana wanu ku mavuto onse amene angamugwere.

N’zoona kuti mwana wanu sangadziwe mmene zimapwetekera munthu akachotsedwa ntchito kapena akakumana ndi mavuto a zachuma. Komabe, mukhoza kumuthandiza kuti azitha kupirira akakumana ndi mavuto ena monga imfa ya wachibale kapena akasiyana ndi anzake omwe ankagwirizana nawo kwambiri. *

Ngati wadzudzulidwa chifukwa cha zimene walakwitsa.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Mvera uphungu . . . kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo.”​—Miyambo 19:20.

Munthu akadzudzula mwana wanu sikuti amakhala kuti akudana naye, koma amafuna kuti amuthandize kusiya khalidwe loipa.

Choncho mukaphunzitsa mwana kumvera malangizo, inuyo ndi mwanayo zinthu zimakuyenderani bwino. Bambo ena dzina lawo a John anati: “Mukamangomuyikira kumbuyo mwana wanu akalakwitsa zinazake, samaphunzira kukhala womvera. Mwanayo amangokhalira kupalamula ndipo inuyo mumakhala pa chintchito chomakonza zimene walakwitsa. Zimenezi zimabweretsa mavuto aakulu kwa makolo komanso kwa mwanayo.”

Kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti azimvera malangizo akamadzudzulidwa? Anthu akamudzudzula, kaya ndi kusukulu kapena malo ena, muzipewa kunena kuti amulakwira kwambiri. M’malomwake mungamufunse kuti:

  • “Ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani akupatsa malangizowa?”

  • “Ungatani kuti usadzabwerezenso zimene unachitazo?”

  • “Udzatani ulendo wina ukadzakumananso ndi zimenezi?”

Muzikumbukira kuti malangizo angamuthandize kwambiri mwana wanuyo panopa, komanso akadzakula.

^ ndime 21 Onani nkhani yakuti, “Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2008.