Miyambo 19:1-29

  • Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake (11)

  • Mkazi wolongolola ali ngati denga lodontha (13)

  • Mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova (14)

  • Langa mwana wako padakali chiyembekezo (18)

  • Ubwino womvetsera malangizo (20)

19  Ndi bwino kukhala wosauka nʼkumachita zinthu mokhulupirika+Kusiyana nʼkukhala munthu wopusa nʼkumalankhula mabodza.+   Munthu wosadziwa zinthu si wabwino,+Ndipo amene amachita zinthu mopupuluma* akuchimwa.   Kupusa kwa munthu nʼkumene kumapotoza njira yake,Ndipo mtima wake umakwiyira Yehova.   Chuma chimachititsa kuti munthu akhale ndi anzake ambiri,Koma munthu wosauka amasiyidwa ngakhale ndi mnzake weniweni.+   Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha sadzathawa chilango.+   Anthu ambiri amafuna kukondedwa ndi munthu wolemekezeka,*Ndipo aliyense ndi bwenzi la munthu wopereka mphatso.   Abale ake onse a munthu wosauka amadana naye,+Kuwonjezera pamenepo anzake amamupewa,+ Iye amawachonderera kuti amuthandize, koma palibe amene amamuyankha.   Munthu amene wapeza nzeru amakonda moyo wake.+ Amene amaona kuti kukhala wozindikira nʼkofunika kwambiri zinthu zidzamuyendera bwino.+   Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha adzawonongedwa.+ 10  Nʼzosayenera kuti munthu wopusa azikhala moyo wawofuwofu.Chimodzimodzinso kuti munthu wantchito alamulire anthu audindo!+ 11  Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake,+Ndipo kunyalanyaza cholakwa kumamʼchititsa kukhala wokongola.+ 12  Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+Koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera. 13  Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake,+Ndipo mkazi wolongolola* ali ngati denga limene silisiya kudontha.+ 14  Nyumba komanso chuma ndi cholowa chochokera kwa makolo,Koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.+ 15  Ulesi umabweretsa tulo tofa nato,Ndipo munthu waulesi adzakhala ndi njala.+ 16  Amene amasunga lamulo amasunga moyo wake.+Amene amachita zinthu mosasamala adzafa.+ 17  Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+Ndipo adzamʼbwezera* zimene anachitazo.+ 18  Langa mwana wako padakali chiyembekezo,+Ndipo usakhale ndi mlandu wochititsa* kuti afe.+ 19  Munthu wosachedwa kupsa mtima ayenera kulipira,Chifukwa ukayesa kumʼpulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri.+ 20  Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo*+Kuti udzakhale wanzeru mʼtsogolo.+ 21  Munthu amakhala ndi mapulani ambiri mumtima mwake,Koma zolinga za Yehova nʼzimene zidzakwaniritsidwe.+ 22  Chinthu chosiririka mwa munthu ndi chikondi chake chokhulupirika,+Ndipo ndi bwino kukhala wosauka kusiyana nʼkukhala munthu wonama. 23  Kuopa Yehova kumathandiza munthu kuti apeze moyo.+Munthu amene amachita zimenezi amagona tulo tokoma ndipo zoipa sizimugwera.+ 24  Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,Koma nʼkulephera kulibweretsa pakamwa.+ 25  Menya munthu wonyoza+ kuti wosadziwa zinthu achenjere,+Ndipo dzudzula munthu womvetsa zinthu kuti awonjezere zimene akudziwa.+ 26  Munthu amene amazunza bambo ake ndiponso kuthamangitsa mayi ake,Ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.+ 27  Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo,Udzasochera nʼkusiya kutsatira mawu anzeru. 28  Mboni yopanda pake imanyoza chilungamo,+Munthu woipa amasangalala kuchita zoipa ngati mmene amasangalalira ndi chakudya.+ 29  Zilango amazisungira anthu onyoza,+Ndipo zikwapu ndi zokwapulira msana wa anthu opusa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “amayenda mofulumira ndi mapazi ake.”
Kapena kuti, “wowolowa manja.”
Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
Kapena kuti, “adzamʼpatsa mphoto pa.”
Kapena kuti, “Ndipo usalakelake.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.