Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Banja Lanu?

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Banja Lanu?

Zipangizo zamakono zikamagwiritsidwa ntchito moyenera zikhoza kulimbitsa ubwenzi umene umakhalapo pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Mwachitsanzo, zingathandize anthu okwatirana kuti azilankhulana nthawi iliyonse.

Komabe anthu ena omwe ali pabanja amagwiritsa ntchito molakwika zipangizo zawo zamakono, ndipo amalola kuti . . .

  • asamakhale ndi nthawi yochezera limodzi.

  • azigwirira ntchito kunyumba popanda zifukwa zomveka.

  • abise zinthu zina ngakhalenso kusiya kukhulupirirana.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

MUKAMACHITIRA ZINTHU LIMODZI

Mwamuna wina dzina lake Michael ananena kuti: “Nthawi zina ndikamacheza ndi mkazi wanga zimangokhala ngati iyeyo ‘palibepo.’ Amangokhalira pafoni ndipo amanena kuti, ‘Chichereni sindinagwireko foni.’” Mwamuna wina dzina lake Jonathan ananena kuti n’zochitika ngati zimenezi “anthu okwatirana amaoneka ngati ali limodzi koma zisali choncho.”

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi ndi kangati pamene foni kapena meseji imakusokonezani mukamacheza ndi mkazi kapena mwamuna wanu?​—AEFESO 5:33.

NTCHITO

Anthu ena amagwira ntchito imene imafunika kuti aziyankha foni kapenanso maimelo pamene ali kunyumba. Pomwe ena amene ntchito yawo sifuna nthawi yambiri, amagwirabe ngakhale pamene ali kunyumba. Mwamuna wina dzina lake Lee ananena kuti: “Zimakhala zovuta kuti ndisamayankhe foni kapena meseji iliyonse imene yabwera yochokera kuntchito pa nthawi imene ndapatula kuti ndicheze ndi mkazi wanga.” Mayi wina dzina lake Joy ananena kuti: “Ndimagwirira ntchito kunyumba choncho nthawi zonse ndimakhala ndikugwira ntchito. Zimafunika khama kuti uzigawa bwino nthawi.”

ZOTI MUGANIZIRE: Mwamuna kapena mkazi wanu akamalankhula nanu, kodi mumamvetsera mwatcheru?​—LUKA 8:18.

KUKHULUPIRIKA

Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu okwatirana amayamba kukayikirana chifukwa cha zimene mmodzi wa iwo waika pamalo ochezera a pa intaneti. Anthu 10 mwa 100 alionse amene anafunsidwawa ananena kuti ankaika zinthu pamalo ochezera a pa intaneti zomwe sankafuna kuti mwamuna kapena mkazi wawo adziwe.

Anthu ambiri amakhulupirira kuti malo ochezera a pa intaneti ali ndi zinthu zambiri “zoopsa zomwe ndi zobisika” komanso amachititsa kuti “kuchita chigololo kukhale kosavuta.” N’zosadabwitsa kuti maloya ena oona nkhani zothetsa ukwati amanena kuti nthawi zambiri malo ochezera a pa intaneti ndi amene amachititsa kuti mabanja ambiri azitha.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mumabisirana nkhani zimene mumacheza ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzanu?—MIYAMBO 4:23.

ZIMENE MUNGACHITE

MUZIDZIWA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI

Munthu amene amanyalanyaza kudya, sakhala ndi thanzi labwino. Mofanana ndi zimenezi, munthu amene amanyalanyaza kucheza ndi mkazi kapena mwamuna wake amakumana ndi mavuto ambiri m’banja lake.​—Aefeso 5:28, 29.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—AFILIPI 1:10.

Kambiranani mfundo zimene zili m’munsimu zomwe mungakonde kuti muzigwiritse ntchito, kapena lembani zanu zomwe zingathandize kuti zipangizo zamakono zisamasokoneze banja lanu.

  • Tsiku lililonse tiziyesetsa kuti ngakhale kamodzi tizidyera limodzi chakudya

  • Kukhala ndi nthawi yoti tisamagwiritse ntchito zipangizo zamakono

  • Kupeza nthawi yapadera yochitira limodzi zinthu zosangalatsa kapena kukaona malo enaake

  • Kuzimitsa mafoni usiku komanso kuwaika patali ndi pomwe timagona

  • Kuzimitsa mafoni kwa 15 minitsi tsiku lililonse, n’cholinga choti tizilankhulana popanda chosokoneza chilichonse

  • Tsiku lililonse kukhala ndi nthawi inayake yoti tisamagwiritse ntchito intaneti