Miyambo 4:1-27

  • Malangizo anzeru a bambo (1-27)

    • Kuposa zonse, peza nzeru (7)

    • Kupewa njira zoipa (14, 15)

    • Njira ya wolungama imapitiriza kuwala (18)

    • “Uteteze mtima wako” (23)

4  Ana anga, mverani malangizo* a bambo anu.+Mvetserani kuti mupeze luso lomvetsa zinthu,   Chifukwa ndidzakupatsani malangizo abwino.Musasiye kutsatira zimene ndimakuphunzitsani.*+   Ndinali mwana wabwino kwambiri kwa bambo anga+Ndipo mayi anga ankandikonda kwambiri.+   Bambo anga ankandiphunzitsa kuti: “Mtima wako ugwire mwamphamvu mawu anga.+ Uzisunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+   Upeze nzeru, upezenso luso lomvetsa zinthu.+ Usaiwale ndipo usapatuke pa zimene ndimakuuza.   Nzeruzo usazisiye ndipo zidzakuteteza. Uzikonde ndipo zidzakuteteza.   Nzeru ndi chinthu chofunika kwambiri,+ choncho upeze nzeru,Ndipo pa zinthu zonse zimene upeze, upezenso luso lomvetsa zinthu.+   Uzilemekeze kwambiri ndipo zidzakukweza.+ Zidzakulemekeza chifukwa chakuti wazikumbatira.+   Zidzaika nkhata yamaluwa yokongola kumutu kwako.Zidzakuveka chisoti chachifumu chokongola.” 10  Tamvera mwana wanga, ndipo utsatire mawu anga.Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka.+ 11  Ndidzakutsogolera mʼnjira ya nzeru.+Ndidzakutsogolera mʼnjira zowongoka.+ 12  Ukamayenda, mapazi ako sadzapanikizika.Ndipo ngati ukuthamanga sudzapunthwa. 13  Gwira mwamphamvu malangizo ndipo usawasiye.+ Uwasunge bwino chifukwa iwo ndi moyo wako.+ 14  Usatengere zochita za anthu oipa,Ndipo usayende panjira ya anthu oipa.+ 15  Uipewe, usayende mʼnjirayo.+Upatukepo ndipo uilambalale.+ 16  Chifukwa iwo sangagone mpaka atachita zoipa. Tulo sitiwabwerera mpaka atachititsa kuti wina agwe. 17  Amadya chakudya chimene achipeza chifukwa chochita zoipa,Ndipo amamwa vinyo amene amupeza chifukwa chochita chiwawa. 18  Koma njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kwa mʼmawaKumene kumawonjezereka mpaka kunja kutawala kwambiri.+ 19  Njira ya oipa ili ngati mdima.Iwo sadziwa chimene chimawapunthwitsa. 20  Mwana wanga, tchera khutu ku mawu anga.Mvetsera mosamala* zonena zanga. 21  Zisachoke pamaso pako.Uzisunge mkati mwa mtima wako.+ 22  Chifukwa amene amazipeza adzakhala ndi moyo+Ndipo thupi lawo lonse lidzakhala lathanzi. 23  Uteteze mtima wako kuposa zinthu zonse zimene umaziteteza,+Chifukwa mumtimamo ndi mmene muli akasupe a moyo. 24  Usamalankhule mawu abodza,+Ndipo usamanene zinthu zimene si zoona. 25  Maso ako aziyangʼana patsogolo.Inde, uziyangʼanitsitsa* zinthu zimene zili patsogolo pako.+ 26  Salaza* njira imene phazi lako likuyenda,+Ndipo njira zako zonse zidzakhala zotetezeka. 27  Usakhotere kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ Phazi lako lipatuke pa zinthu zoipa.

Mawu a M'munsi

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
Kapena kuti, “lamulo langa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Tchera khutu lako ku.”
Kapena kuti, “maso ako owala aziyangʼanitsitsa.”
Mabaibulo ena amati, “Sinkhasinkha bwino.”