Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Anthu Ambiri Ankadana Nane”

“Anthu Ambiri Ankadana Nane”
  • CHAKA CHOBADWA: 1978

  • DZIKO: CHILE

  • POYAMBA: NDINALI WACHIWAWA KWAMBIRI

KALE LANGA:

Ndinakulira ku Santiago, likulu la dziko la Chile. Anthu a m’dera limene ndinkakhala ankakonda kugulitsa mankhwala osokoneza bongo ndiponso m’derali munali magulu ambiri a zigawenga zomwe zinkachita zachiwawa. Ndili ndi zaka 5, bambo anga anaphedwa. Kenako mayi anga anakwatiwa ndi bambo winawake yemwe anali wankhanza ndipo nthawi zina ankatimenya tonse. Zimandipwetekabe kwambiri mumtima ndikakumbukira nkhanza zimene ankatichitira.

Zimenezi zinapangitsa kuti ndili wachinyamata ndikhale wachiwawa kwambiri. Ndinkamvera nyimbo za heavy-metal, ndinkamwa mowa kwambiri komanso nthawi zina ndinkagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nthawi zambiri ndinkamenyana ndi anthu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo omwe nthawi zingapo ankafuna kundipha. Pa nthawi ina gulu lina la zigawenga limene tinkalimbana nalo kwambiri, linalemba ganyu chigawenga choopsa kwambiri n’cholinga choti chindiphe, koma mwamwayi ndinakwanitsa kuthawa atandibaya ndi mpeni.

Mu 1996 ndinayamba chibwenzi ndi mtsikana wina dzina lake Carolina ndipo tinakwatirana mu 1998. Mwana wathu woyamba atabadwa, ndinayamba kuda nkhawa kuti khalidwe langa losachedwa kupsa mtima lingachititse kuti ndikhale ngati bambo anga ondipeza n’kumazunza banja langa. Choncho ndinapita kuchipatala chothandiza anthu ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Anandipatsa thandizo loyenerera ndiponso mankhwala, koma sizinathandize. Ndinapitirizabe kumangokwiya ndi chilichonse moti anthu ankalephera kundithandiza. Sindinkafuna kuti banja langa lizizunzika chifukwa cha ine, choncho ndinaganiza zodzipha. Mwamwayi sindinafe.

Kwa zaka zambiri sindinkakhulupirira kuti kuli Mulungu, komabe ndinkafuna nditayamba kukhulupirira Mulungu. Choncho kwa kanthawi ndinalowa mpingo wa Evanjeliko. Pa nthawiyi n’kuti mkazi wanga akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinkadana ndi a Mboni ndipo nthawi zambiri ndinkawatukwana koma ndinkadabwa nawo chifukwa sankandibwezera.

Tsiku lina mkazi wanga anandiuza kuti nditenge Baibulo langa ndipo ndiwerenge lemba la Salimo 83:18. Vesili limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Zimenezi zinandidabwitsa chifukwa kutchalitchi kwathu sankatiphunzitsa za Yehova. Kumayambiriro  kwa chaka cha 2000, nanenso ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Pamene ndinkaphunzira, ndinasangalala kudziwa kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo komanso amakhululuka. Mwachitsanzo, pa Ekisodo 34:6, 7 Baibulo limafotokoza kuti Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.”

Komabe zinkandivuta kuti ndizigwiritsa ntchito zimene ndinkaphunzira. Ndinkaona kuti n’zosatheka kusiya khalidwe langa lankhanza. Nthawi zonse ndikalephera kuugwira mtima, Carolina ankandilimbikitsa mwachikondi. Ankandikumbutsa kuti Yehova akuona kuyesetsa kwanga. Zimenezi zinandilimbikitsa kupitirizabe kuyesetsa kusangalatsa Yehova ngakhale kuti nthawi zambiri ndinkalephera.

Tsiku lina m’bale amene ankandiphunzitsa Baibulo, dzina lake Alejandro, anandiuza kuti ndiwerenge Agalatiya 5:22, 23. Lembali limanena kuti mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa makhalidwe monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.” Alejandro anandiuza kuti sindingakhale ndi makhalidwe amenewa pandekha. Ndikufunika kudalira mzimu woyera wa Mulungu. Mfundo imeneyi inandithandiza kusintha maganizo amene ndinali nawo.

Kenako ndinapita ku msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Anthu ake ankachita zinthu mwadongosolo, anali aukhondo ndiponso anandilandira bwino kwambiri. Zimenezi zinanditsimikizira kuti ndapeza chipembedzo choona. (Yohane 13:34, 35) Kenako ndinabatizidwa mu February 2001.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Yehova wandithandiza kuti ndisinthe khalidwe langa lokonda zachiwawa moti panopa ndine munthu wokonda mtendere. Ndimaona kuti anandipulumutsa ku mavuto amene sindikanatha kuwathetsa ndekha. Anthu ambiri ankadana nane, ndipo sindingawaimbe mlandu. Panopa, ndikusangalala kwambiri kuti ndikutumikira Yehova pamodzi ndi mkazi wanga komanso ana anga awiri.

Abale anga komanso anzanga samamvetsa akaona kuti ndinasintha. Zimenezi zachititsa kuti ambiri akhale ndi chidwi chophunzira Baibulo. Ndakhalanso ndi mwayi wothandiza anthu ena kudziwa Yehova ndipo ndimasangalala kwambiri kuona nawonso akusintha moyo wawo chifukwa cha mfundo za m’Baibulo.