Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?

Uthenga Wabwino Wopita ku Mitundu Yonse

Uthenga Wabwino Wopita ku Mitundu Yonse

Kuukitsidwa kwa Yesu kunalimbikitsa ophunzira ake kuti agwire ntchito yolalikira mwakhama kwambiri. Mtumwi Paulo anayenda m’madera onse a ku Asia Minor ndi m’mphepete mwa nyanja ya Mediterranean ndipo anakhazikitsa mipingo. Iye analimbikitsanso Akhristu kupirira mayesero ndi nkhanza zimene ankachitiridwa. Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto amenewa, Chikhristu chinapitirizabe kufalikira m’madera ena.

Nayenso Pauloyo nthawi ina anaikidwa m’ndende. Komabe anapitiriza kulembera mipingo makalata owalangiza komanso kuwalimbikitsa. Anawachenjeza za vuto lina lalikulu, lomwe ndi mpatuko. Motsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, Paulo anadziwiratu zoti pakati pawo padzakhala anthu ena angati “mimbulu yopondereza,” omwe azidzalankhula “zinthu zopotoka” n’cholinga choti “apatutse ophunzira aziwatsatira.”—Machitidwe 20:29, 30.

Mpatuko umenewu unayamba chakumapeto kwa nthawi ya atumwi. Nthawi imeneyi Yesu, yemwe anali ataukitsidwa, anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya omwe ali m’buku la Chivumbulutso. Yohane analemba kuti anthu otsutsa kapena aphunzitsi onyenga sangalepheretse Mulungu kukwaniritsa cholinga chimene anali nacho polenga dziko lapansi ndiponso anthu. Iye analemba kuti anthu a ‘dziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse’ adzamva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 14:6) Paradaiso adzabwezeretsedwa padziko lapansi ndipo aliyense amene amachita chifuniro cha Mulungu akhoza kudzakhalamo.

Kodi inuyo mukuona kuti umenewu ndi “uthenga wabwino”? Ngati mukuona choncho, muyenera kuwerenga uthenga wa Mulungu womwe uli m’Baibulo kuti mudziwe mmene uthengawo ungakuthandizireni panopa komanso m’tsogolo.

Mukhoza kuwerenga Baibulo pa webusaiti ya www.mt711.com. Pa webusaiti imeneyi mukhoza kuwerenganso kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? ndi kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu komanso buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Palinso mabuku ena amene amafotokoza chifukwa chake tiyenera kukhulupirira zimene Baibulo limanena komanso mmene tingatsatirire malangizo ake pa moyo wathu. Mukhozanso kufunsa wa Mboni za Yehova aliyense ngati muli ndi mafunso.

Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Machitidwe; Aefeso; Afilipi; Akolose; Filemoni; 1 Yohane; Chivumbulutso.