Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA

Palibe Chinthu Chabwino Kwambiri Kuposa Kukhala pa Ubwenzi Ndi Mulungu

Palibe Chinthu Chabwino Kwambiri Kuposa Kukhala pa Ubwenzi Ndi Mulungu

Kodi mungatani kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima? Taona zinthu zingapo zimene mungachite. Zinthu zake ndi izi:

  1. Muyenera kudziwa dzina la Mulungu n’kumatchula dzinali mukamanena za iye.

  2. Muzilankhulana naye. Mungachite zimenezi popemphera kwa iye komanso kuphunzira Mawu ake, Baibulo.

  3. Muzichita zimene iye amafuna.

Kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima muzitchula dzina lake mukamanena za iye, muzipemphera kwa iye, muziphunzira Baibulo komanso muzichita zimene iye amafuna

Mukaganizira mfundo zimenezi, kodi mukuona kuti mukuchita zonse zofunika kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima? Kodi pali zimene mukuona kuti mukufunika kukonza kuti ubwenzi umenewu utheke? N’zoona kuti pamafunika khama, koma zotsatira zake zimakhala zabwino.

Jennifer wa ku United States anati: “Pamafunika khama kuti Mulungu akhale mnzako wapamtima, koma mpake. Mulungu akakhala mnzako wapamtima, umamudalira, umamudziwa bwino komanso umamukonda. Ndisaname, palibe chinthu chabwino kwambiri kuposa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.”

Ngati mukufuna kuti nanunso Mulungu akhale mnzanu wapamtima, a Mboni za Yehova angakuthandizeni. Akhoza kumaphunzira nanu Baibulo kwaulere. Komanso, mungathe kupita ku Nyumba ya Ufumu yomwe ili m’dera lanu komwe a Mboni za Yehova amaphunzira nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo. Mukadzapita kumeneko, mudzasangalala kucheza ndi anthu amene amaona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri. * Nanunso mudzamva ngati mmene munthu wina amene analemba nawo masalimo anamvera. Iye anati: “Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.”—Salimo 73:28.

^ ndime 9 Kuti mupeze munthu woti aziphunzira nanu Baibulo kapena kuti mudziwe komwe Nyumba ya Ufumu ili m’dera lanu, lankhulani ndi munthu amene anakupatsani magaziniyi kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.mt711.com/ny. Pitani pamene palembedwa kuti POYAMBIRA › TIPEZENI pamunsi pa tsambalo.