Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA

Kodi Mumadziwa Ndiponso Kutchula Dzina la Mulungu?

Kodi Mumadziwa Ndiponso Kutchula Dzina la Mulungu?

Kodi muli ndi mnzanu wapamtima amene simudziwa dzina lake? Kunena zoona zimenezi sizingatheke. Ndiyetu n’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Mayi wina wa ku Bulgaria, dzina lake Irina, anati: “N’zosatheka kuti Mulungu akhale mnzako wapamtima ngati sudziwa n’komwe dzina lake.” Koma monga taonera m’nkhani yapita ija, Mulungu amafuna kuti mudziwe dzina lake, kuti akhale mnzanu. Choncho kudzera m’Baibulo tingati iye wakuuzani dzina lake kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”—Yesaya 42:8.

Kudzera m’Baibulo tingati Mulungu wakuuzani dzina lake kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”—Yesaya 42:8.

Kodi Mulungu amaona kuti n’zofunika kuti mudziwe dzina lake ndiponso kuti muzilitchula? Inde. Mwachitsanzo, zilembo zomwe zimaimira dzina la Mulungu, zomwe zinkalembedwa popanda mavawelo, zinkapezeka pafupifupi ka 7,000 m’mipukutu yoyambirira ya Malemba Achiheberi. Apa ndiye kuti dzina la Mulungu linkapezeka m’Malemba kambiri kuposa dzina lililonse. Umenewutu ndi umboni woti Yehova amafuna kuti mudziwe dzina lake komanso muzilitchula. *

Kuti anthu akhale mabwenzi, amayamba ndi kuuzana mayina. Kodi inuyo mumadziwa dzina la Mulungu?

Komabe anthu ena angaganize kuti popeza Mulungu ndi woyera komanso Wamphamvuyonse, kutchula dzina lake ndi kupanda ulemu. N’zoona kuti n’zosayenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu molakwika, monga kulumbira potchula dzinali koma ukudziwa kuti zomwe ukunenazo n’zabodza. Izi n’zofanana ndi mmenenso zilili kuti sungamagwiritse ntchito dzina la mnzako pa zifukwa zosayenera. Komabe Yehova amafuna kuti anthu amene amamukonda azilemekeza dzina lake komanso azithandiza ena kudziwa dzinali. (Salimo 69:30, 31; 96:2, 8) Kumbukirani kuti Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ifenso tingathandizire kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe pouza ena za dzinali. Tikamachita zimenezi, ubwenzi wathu ndi Mulungu umalimba.

Baibulo limanena kuti ‘munthu akamaganizira za dzina la Mulungu,’ Mulunguyo amatchera khutu ndi kumvetsera. (Malaki 3:16) Ponena za munthu wotereyu, Yehova amalonjeza kuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda, inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa. Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha. Ndidzakhala naye m’nthawi ya masautso.” (Salimo 91:14, 15) Choncho, ngati tikufuna kuti Yehova akhale mnzathu wapamtima, tiyenera kudziwa dzina lake komanso kumalitchula.

^ ndime 4 Ngakhale kuti dzina la Mulungu linkapezeka kambirimbiri m’Malemba Achiheberi, omwe ambiri amati Chipangano Chakale, n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri omasulira Mabaibulo sanaike dzinali m’Mabaibulo amene anamasulira. Pamene panali dzinali anaikapo mayina audindo monga akuti, “Ambuye” kapena “Mulungu.” Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani tsamba 195 mpaka 197 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.