Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI A MBONI ZA YEHOVA NDI ANTHU OTANI?

N’chifukwa Chiyani Timalalikira?

N’chifukwa Chiyani Timalalikira?

Anthu ambiri amatidziwa bwino chifukwa cha ntchito yolalikira, yomwe timagwira padziko lonse. Timalalikira kunyumba ndi nyumba, m’malo opezeka anthu ambiri komanso kulikonse komwe timapeza anthu. Koma kodi n’chifukwa chiyani timalalikira?

Timalalikira pofuna kulemekeza Mulungu komanso kuthandiza anthu ena kudziwa dzina lake. (Aheberi 13:15) Timachitanso zimenezi pomvera zimene Yesu ananena. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mateyu 28:19, 20.

Timalalikiranso chifukwa choti timakonda anthu ena. (Mateyu 22:39) Timadziwa kuti anthu omwe timawalalikira ali ndi zipembedzo zawo komanso kuti si onse amene amasangalala ndi uthenga wathu. Komabe, timachita zimenezi chifukwa timadziwa kuti uthenga wa m’Baibulo udzathandiza kuti anthu adzapulumuke. N’chifukwa chake ‘timapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.’—Machitidwe 5:41, 42.

Nyuzipepala ina ya ku Venezuela inanena zimene katswiri wina wophunzira za chikhalidwe cha anthu, dzina lake Antonio Cova Maduro, analemba zokhudza a Mboni za Yehova. Inati: “A Mboni za Yehova amagwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri ndiponso amalolera kuzunzidwa . . . n’cholinga choti uthenga wawo womwe ndi wofunika kwambiri ufike padziko lonse.”—El Universal.

Anthu ambiri amene amawerenga mabuku athu, si a Mboni. Ndiponso anthu ambiri omwe timaphunzira nawo Baibulo, ali ndi zipembedzo zawo. Komabe anthuwa amasangalala kwambiri tikafika kunyumba zawo.

Tikudziwa kuti pali zambiri zomwe mungafune kudziwa zokhudza a Mboni za Yehova. Choncho, pali njira zingapo zomwe zingakuthandizeni kudziwa zambiri.

  • Mungafunse wa Mboni za Yehova aliyense.

  • Mungapite pa webusaiti yathu ya www.mt711.com/ny.

  • Mukhozanso kufika pa misonkhano yathu. Misonkhanoyi imachitika kwaulere ndipo aliyense ndi wolandiridwa.